Kilniojo Korano reikšmių vertimas - Vertimas į čevų k. - Khalid Ibrahim Bitala

Puslapio numeris:close

external-link copy
17 : 2

مَثَلُهُمۡ كَمَثَلِ ٱلَّذِي ٱسۡتَوۡقَدَ نَارٗا فَلَمَّآ أَضَآءَتۡ مَا حَوۡلَهُۥ ذَهَبَ ٱللَّهُ بِنُورِهِمۡ وَتَرَكَهُمۡ فِي ظُلُمَٰتٖ لَّا يُبۡصِرُونَ

Fanizo lawo lili ngati (munthu wa paulendo wafungatiridwa ndi mdima) yemwe wayatsa moto; ndipo pamene udaunika zomwe zidali m’mphepete mwake, Allah nkuwachotsera kuunika kwawoko nawasiya mu mdima osatha kuona. info
التفاسير:

external-link copy
18 : 2

صُمُّۢ بُكۡمٌ عُمۡيٞ فَهُمۡ لَا يَرۡجِعُونَ

(Nakhala ngati) agonthi, abubu, akhungu; ndipo sangabwelerenso (ku chiwongoko). info
التفاسير:

external-link copy
19 : 2

أَوۡ كَصَيِّبٖ مِّنَ ٱلسَّمَآءِ فِيهِ ظُلُمَٰتٞ وَرَعۡدٞ وَبَرۡقٞ يَجۡعَلُونَ أَصَٰبِعَهُمۡ فِيٓ ءَاذَانِهِم مِّنَ ٱلصَّوَٰعِقِ حَذَرَ ٱلۡمَوۡتِۚ وَٱللَّهُ مُحِيطُۢ بِٱلۡكَٰفِرِينَ

Kapena (fanizo lawonso) lili ngati chimvula chochokera ku mitambo m’kati mwake muukhala mdima, mphenzi ndi kung’anima, naika zala zawo m’makutu mwawo chifukwa chamkokomo ndikuopa imfa (pomwe kutero sikungawathandize chilichonse). Ndipo Allah akudziwa bwinobwino za osakhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
20 : 2

يَكَادُ ٱلۡبَرۡقُ يَخۡطَفُ أَبۡصَٰرَهُمۡۖ كُلَّمَآ أَضَآءَ لَهُم مَّشَوۡاْ فِيهِ وَإِذَآ أَظۡلَمَ عَلَيۡهِمۡ قَامُواْۚ وَلَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ لَذَهَبَ بِسَمۡعِهِمۡ وَأَبۡصَٰرِهِمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ

Kung’anima kukuyandikira kutsomphola maso awo; nthawi iliyonse kukawaunikira, nkuyenda m’menemo (mkuunikamo). Koma kukawachitira mdima, nkuyima. ndipo Allah akadafuna akadawachotsera kumva kwawo ndi kuona kwawo. Ndithudi, Allah Ngokhoza chilichonse. info
التفاسير:

external-link copy
21 : 2

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ ٱعۡبُدُواْ رَبَّكُمُ ٱلَّذِي خَلَقَكُمۡ وَٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تَتَّقُونَ

E inu anthu! pembedzani Mbuye wanu Yemwe adakulengani inu ndi omwe adalipo kale, kuti mukhale oopa (Allah). info
التفاسير:

external-link copy
22 : 2

ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلۡأَرۡضَ فِرَٰشٗا وَٱلسَّمَآءَ بِنَآءٗ وَأَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَأَخۡرَجَ بِهِۦ مِنَ ٱلثَّمَرَٰتِ رِزۡقٗا لَّكُمۡۖ فَلَا تَجۡعَلُواْ لِلَّهِ أَندَادٗا وَأَنتُمۡ تَعۡلَمُونَ

(Allah) Yemwe adakupangirani nthaka kukhala ngati mphasa, ndi thambo kukhala ngati denga; ndipo adatsitsa madzi kuchokera ku mitambo natulutsa ndi madziwo zipatso zosiyanasiyana kuti zikhale chakudya chanu. Choncho Allah musampangire anzake uku inu mukudziwa (kuti alibe wothandizana naye). info
التفاسير:

external-link copy
23 : 2

وَإِن كُنتُمۡ فِي رَيۡبٖ مِّمَّا نَزَّلۡنَا عَلَىٰ عَبۡدِنَا فَأۡتُواْ بِسُورَةٖ مِّن مِّثۡلِهِۦ وَٱدۡعُواْ شُهَدَآءَكُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ

Ndipo ngati muli m’chikaiko ndi zomwe tamvumbulutsira kapolo wathu (kuti sizinachokere kwa Ife,) tabweretsani sura imodzi yolingana ndi Quraniyi (m’kayankhulidwe ka nzeru ndi kayalidwe ka malamulo ake). Ndipo itanani athandizi anu (kuti akuthandizeni) osakhala Allah; ngati inu mukunena zoona (kuti Qur’an njopekedwa). info
التفاسير:

external-link copy
24 : 2

فَإِن لَّمۡ تَفۡعَلُواْ وَلَن تَفۡعَلُواْ فَٱتَّقُواْ ٱلنَّارَ ٱلَّتِي وَقُودُهَا ٱلنَّاسُ وَٱلۡحِجَارَةُۖ أُعِدَّتۡ لِلۡكَٰفِرِينَ

Choncho ngati simutha (kubweretsa sura imodzi yonga ya m’Qurani) ndiye kuti simudzatha. Choncho opani Moto omwe nkhuni zake ndi anthu ndi miyala umene wakonzedwera kwa osakhulupirira. info
التفاسير: