[136] (Ndime 97-99) Kalelo Mtumiki (s.a.w) atasamukira ku Madina pamodzi ndi omtsatira ake, Asilamu adawalamula kuti asamukire ku Madinako kusiya nyumba zawo, chuma chawo, abale awo ndi ana awo. Izi zidali chonchi chifukwa iwo akanakhalabe m’midzi yawo pansi pautsogoleri wa anthu osakhulupilira sakanatha kukwaniritsa malamulo a Chisilamu. Tero Chisilamu chake sichikanakhala ndi ntchito. Ndipo Chisilamu chopanda ntchito si Chisilamunso. Tero nchifukwa chake apa akuwadzudzula amene sanasamuke kuti adzafa ndi imfa yoipa kupatula okhawo amene sanapeze njira yosamukira ku Madina chifukwa chakufooka kwa matupi awo. Amenewa madandaulo awo akhoza kuwavomera. Koma chachikulu nkuti ayesetse kusamukira ku Madina.
[137] Apa akuwalimbikitsa za kusamuka ndi kuwauza kuti kumene akupitako akapeza bwino. Akuwalimbikitsanso okalamba ndi odwala kuti asamuke. Ngati atafera pa njira kuwerengedwa kuti adasamukabe ndipo adzapeza mphoto yonga ya yemwe adasamuka nkukakhala ku Madina pamodzi ndi Mtumiki (s.a.w) ndi kukathandiza kukamenya nkhondo yoteteza Chisilamu kwa adani. Ndichimodzomodzi munthu akapita ku Makka kukachita Hajj ndipo nkumwalira Hajjiyo asanachite, kapena asanamalize zina zofunika pa Hajj, kwa Allah amamuwerenga kuti wachita mapemphero a Hajj. Komabe abale ake akhoza kukamchitiranso mapemphero a Hajj.
[138] Pamene Asilamu adawalamulira zakusamuka, adawafupikitsira Swala chifukwa cha mavuto am’njira monga kuti (a) Swala zokhala ndi raka zinayi akhoza kuziswali ndi raka ziwiriziwiri. (b) Akhoza kuswali katatu kokha patsiku m’malo mwakasanu. Izi zili motere: Swala ya Dhuhr nkuiphatikiza pamodzi ndi Swala ya Asr; kuzipemphera panthawi ya Dhuhr kapena kuzipemphera panthawi ya Asr. Swala ya Maghrib nkuipemphera pamodzi ndi Swala ya Isha. Adzayamba kupemphera Swala ya Maghrib raka zitatu kenako nkupemphera Isha raka ziwiri. Koma Swala ya Subh yokha njomwe imapempheredwa payokha ndiponso m’nthawi yake. Lamuloli analikhazikitsa pamene Asilamu adali ndi mantha ndi masautso am’njira. Ndipo lidasiidwa momwemo losasinthika mpaka lero m’nthawi yomwe anthu akukwera galimoto, sitima ndi ndege.