ការបកប្រែអត្ថន័យគួរអាន - ការបកប្រែជាភាសាឆេវ៉ា - ខលីទ អុីប្រហុីម ប៊ីតាឡា

លេខ​ទំព័រ:close

external-link copy
87 : 4

ٱللَّهُ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۚ لَيَجۡمَعَنَّكُمۡ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ لَا رَيۡبَ فِيهِۗ وَمَنۡ أَصۡدَقُ مِنَ ٱللَّهِ حَدِيثٗا

Allah! Palibe wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye basi. Ndithudi, adzakusonkhanitsani tsiku la chiweruziro lopanda chikaiko mwa ilo. Kodi ndani ali onena zoona kuposa Allah? info
التفاسير:

external-link copy
88 : 4

۞ فَمَا لَكُمۡ فِي ٱلۡمُنَٰفِقِينَ فِئَتَيۡنِ وَٱللَّهُ أَرۡكَسَهُم بِمَا كَسَبُوٓاْۚ أَتُرِيدُونَ أَن تَهۡدُواْ مَنۡ أَضَلَّ ٱللَّهُۖ وَمَن يُضۡلِلِ ٱللَّهُ فَلَن تَجِدَ لَهُۥ سَبِيلٗا

Kodi mwatani inu pokhala magulu awiri pa nkhani ya achiphamaso (achinyengo) pomwe Allah wawatembenuza chifukwa cha (zoipa) zomwe achita? Kodi mukufuna kuti mumuongole amene Allah wamlekelera kusokera? Ndipo amene Allah wamulekelera kusokera, simungathe kumpezera njira (yomuikira ku chilungamo). info
التفاسير:

external-link copy
89 : 4

وَدُّواْ لَوۡ تَكۡفُرُونَ كَمَا كَفَرُواْ فَتَكُونُونَ سَوَآءٗۖ فَلَا تَتَّخِذُواْ مِنۡهُمۡ أَوۡلِيَآءَ حَتَّىٰ يُهَاجِرُواْ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِۚ فَإِن تَوَلَّوۡاْ فَخُذُوهُمۡ وَٱقۡتُلُوهُمۡ حَيۡثُ وَجَدتُّمُوهُمۡۖ وَلَا تَتَّخِذُواْ مِنۡهُمۡ وَلِيّٗا وَلَا نَصِيرًا

Ndipo akufuna kuti mukadakhala osakhulupirira monga momwe iwo sadakhulupirire tero kuti mukhale ofanana. Musawachite kukhala abwenzi mpaka asamukire panjira ya Allah. Koma ngati anyoza, agwireni ndi kuwapha paliponse mwawapeza (monga momwe akukuchitirani inu). Ndipo musamuyese mtetezi ngakhale mthandizi aliyense wa iwo. info
التفاسير:

external-link copy
90 : 4

إِلَّا ٱلَّذِينَ يَصِلُونَ إِلَىٰ قَوۡمِۭ بَيۡنَكُمۡ وَبَيۡنَهُم مِّيثَٰقٌ أَوۡ جَآءُوكُمۡ حَصِرَتۡ صُدُورُهُمۡ أَن يُقَٰتِلُوكُمۡ أَوۡ يُقَٰتِلُواْ قَوۡمَهُمۡۚ وَلَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ لَسَلَّطَهُمۡ عَلَيۡكُمۡ فَلَقَٰتَلُوكُمۡۚ فَإِنِ ٱعۡتَزَلُوكُمۡ فَلَمۡ يُقَٰتِلُوكُمۡ وَأَلۡقَوۡاْ إِلَيۡكُمُ ٱلسَّلَمَ فَمَا جَعَلَ ٱللَّهُ لَكُمۡ عَلَيۡهِمۡ سَبِيلٗا

Kupatula omwe akugwirizana ndi anthu amene pali pangano pakati panu ndi iwo, kapena omwe akudza kwa inu uku zifuwa zawo zili zobanika kumenyana nanu, kapena kumenyana ndi anthu awo. (Oterewo musamenyane nawo). Ngati Allah akadafuna, akadawapatsa mphamvu yokugonjetserani, choncho akadakumenyani. Ngati atakupewani, osamenyana nanu ndipo nkukupatsani mtendere, ndiye kuti Allah sadakupangireni njira pa iwo (yakuti mumenyane nawo). info
التفاسير:

external-link copy
91 : 4

سَتَجِدُونَ ءَاخَرِينَ يُرِيدُونَ أَن يَأۡمَنُوكُمۡ وَيَأۡمَنُواْ قَوۡمَهُمۡ كُلَّ مَا رُدُّوٓاْ إِلَى ٱلۡفِتۡنَةِ أُرۡكِسُواْ فِيهَاۚ فَإِن لَّمۡ يَعۡتَزِلُوكُمۡ وَيُلۡقُوٓاْ إِلَيۡكُمُ ٱلسَّلَمَ وَيَكُفُّوٓاْ أَيۡدِيَهُمۡ فَخُذُوهُمۡ وَٱقۡتُلُوهُمۡ حَيۡثُ ثَقِفۡتُمُوهُمۡۚ وَأُوْلَٰٓئِكُمۡ جَعَلۡنَا لَكُمۡ عَلَيۡهِمۡ سُلۡطَٰنٗا مُّبِينٗا

Muzawapeza ena omwe akufuna kupeza chitetezo kwa inu ndi kupeza chitetezo kwa anthu awo. Nthawi iliyonse akabwezedwa ku ukafiri (ndi anzawo osakhulupirira), amagweramo mwamtheradi (nkuyamba kumenyananso ndi inu), ngati sadzipatula kwa inu ndipo osakupatsani mtendere ndi kutsekereza manja awo, agwireni ndi kuwapha paliponse pamene mwawapeza (monga momwe iwo akuchitira kwa inu) ndipo takupangirani chisonyezo choonekera pa iwo info
التفاسير: