クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 - Khalid Ibrahim

Al-Mutaffîfîn

external-link copy
1 : 83

وَيۡلٞ لِّلۡمُطَفِّفِينَ

Kuonongeka koopsa kukawapeza opunguza miyeso ya malonda. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 83

ٱلَّذِينَ إِذَا ٱكۡتَالُواْ عَلَى ٱلنَّاسِ يَسۡتَوۡفُونَ

Amene amati akamadziyezera zinthu kwa anthu amafuna kulandira miyeso yodzadza. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 83

وَإِذَا كَالُوهُمۡ أَو وَّزَنُوهُمۡ يُخۡسِرُونَ

Koma pamene iwo akamawayesera pa muyeso wa mbale kapena wa sikelo amapungula (choyenera kulandira ogulawo). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 83

أَلَا يَظُنُّ أُوْلَٰٓئِكَ أَنَّهُم مَّبۡعُوثُونَ

Kodi amenewa (akupungula miyeso pamalondawo) sakuganiza kuti adzaukitsidwa; info
التفاسير:

external-link copy
5 : 83

لِيَوۡمٍ عَظِيمٖ

Pa tsiku lalikulu (ndiponso loopsa)? info
التفاسير:

external-link copy
6 : 83

يَوۡمَ يَقُومُ ٱلنَّاسُ لِرَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

Tsiku limene adzaimilira anthu pamaso pa Mbuye wa zolengedwa. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 83

كَلَّآ إِنَّ كِتَٰبَ ٱلۡفُجَّارِ لَفِي سِجِّينٖ

Ayi! Ndithu (siyani chinyengo pamalonda ndi kusalabadira kuuka mmanda); zolembedwa za ntchito ya oipa zili mu Sijjin. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 83

وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا سِجِّينٞ

Nanga nchiyani chitakudziwitse za Sijjin? info
التفاسير:

external-link copy
9 : 83

كِتَٰبٞ مَّرۡقُومٞ

Ameneyu ndi kaundula wamkulu yemwe walembedwa (mkati mwake ntchito za anthu oipa). info
التفاسير:

external-link copy
10 : 83

وَيۡلٞ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡمُكَذِّبِينَ

Chilango chaukali tsiku limenelo chili pa otsutsa,[401] info

[401] Kutsutsa kulipo kwa mitundu itatu:
(a) Kutsutsa kwa mawu ndi zochita;
(b) Kutsutsa kwa zochita zokha, monga ukauzidwa kuti chinthu ichi nchoipa, munthu nkudziwa kuti zoona nchoipadi koma nkudzachichita chimenecho mosalabadira;
(c) Kutsutsa ndi zolankhula zokha. Kumeneko ndiko monga munthu akudziwa kuti chakutichakuti ncholetsedwa (haramu) koma m’malo mwake iye nkumati chimenecho nchovomerezeka (halali)

التفاسير:

external-link copy
11 : 83

ٱلَّذِينَ يُكَذِّبُونَ بِيَوۡمِ ٱلدِّينِ

Amene akutsutsa za tsiku la malipiro. info
التفاسير:

external-link copy
12 : 83

وَمَا يُكَذِّبُ بِهِۦٓ إِلَّا كُلُّ مُعۡتَدٍ أَثِيمٍ

Ndipo palibe angalitsutse koma yekhayo wopyola malire (pochita zoipa), wa machimo ambiri; info
التفاسير:

external-link copy
13 : 83

إِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِ ءَايَٰتُنَا قَالَ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ

Pamene ma Ayah Athu akuwerengedwa kwa iye (onena za tsiku la malipiro ndikuuka mmanda) amanena kuti: “Izi ndi nthano za anthu akale.” info
التفاسير:

external-link copy
14 : 83

كَلَّاۖ بَلۡۜ رَانَ عَلَىٰ قُلُوبِهِم مَّا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ

Iyayi, sichoncho! Koma yaphimbidwa mitima yawo ndi dzimbiri (la machimo) omwe akhala akukolola.[402] info

[402] Munthu akachita choipa koyamba ndipo osalapa, limalowa dontho lakuda mu mtima mwake; nthawi iliyonse pamene akuonjezera machimo, dontho lija limakulirakulira mpaka kuuphimba mtima wonse. Dontho limeneli ndilo likutchedwa “Ran.” Tsono mtima ngati utaphimbidwa chotere sulabadira kuchita zoipa, ngakhale kuti auongole sungaongoke.

التفاسير:

external-link copy
15 : 83

كَلَّآ إِنَّهُمۡ عَن رَّبِّهِمۡ يَوۡمَئِذٖ لَّمَحۡجُوبُونَ

Ayi ndithu iwo (okanira) tsiku limenelo) adzatchingidwa kwa Mbuye wawo; (sadzamuona). info
التفاسير:

external-link copy
16 : 83

ثُمَّ إِنَّهُمۡ لَصَالُواْ ٱلۡجَحِيمِ

Pambuyo pake adzalowa ku Moto; (oyaka) info
التفاسير:

external-link copy
17 : 83

ثُمَّ يُقَالُ هَٰذَا ٱلَّذِي كُنتُم بِهِۦ تُكَذِّبُونَ

Kenaka adzauzidwa (powaliritsa) “Ichi nchilango chomwe mudali kuchitsutsa (pa dziko lapansi).” info
التفاسير:

external-link copy
18 : 83

كَلَّآ إِنَّ كِتَٰبَ ٱلۡأَبۡرَارِ لَفِي عِلِّيِّينَ

Zoona, ndithu kaundula wa anthu abwino (ochita ntchito zabwino) ali mu Illiyyun. info
التفاسير:

external-link copy
19 : 83

وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا عِلِّيُّونَ

Nanga nchiyani chitakudziwitse za Illiyyun? info
التفاسير:

external-link copy
20 : 83

كِتَٰبٞ مَّرۡقُومٞ

Ameneyu ndi kaundula (wamkulu) yemwe walembedwa (mkati mwake ntchito za anthu abwino); info
التفاسير:

external-link copy
21 : 83

يَشۡهَدُهُ ٱلۡمُقَرَّبُونَ

Amamuyikira umboni (angelo) amene ayandikitsidwa (kwa Allah). info
التفاسير:

external-link copy
22 : 83

إِنَّ ٱلۡأَبۡرَارَ لَفِي نَعِيمٍ

Ndithu ochita zabwino adzakhala mu mtendere, info
التفاسير:

external-link copy
23 : 83

عَلَى ٱلۡأَرَآئِكِ يَنظُرُونَ

Atakhala pa mipando ya ulemu uku akuyang’ana (zimene Allah wawapatsa monga mtendere ndi ulemelero). info
التفاسير:

external-link copy
24 : 83

تَعۡرِفُ فِي وُجُوهِهِمۡ نَضۡرَةَ ٱلنَّعِيمِ

Udzaona kuwala kwa mtendere pa nkhope zawo; info
التفاسير:

external-link copy
25 : 83

يُسۡقَوۡنَ مِن رَّحِيقٖ مَّخۡتُومٍ

Adzamwetsedwa vinyo (woyeretsedwa) wotsekeredwa ndi zitsekerero zolimba; info
التفاسير:

external-link copy
26 : 83

خِتَٰمُهُۥ مِسۡكٞۚ وَفِي ذَٰلِكَ فَلۡيَتَنَافَسِ ٱلۡمُتَنَٰفِسُونَ

Komalizira kwake (kwa vinyoyo) kuzikatuluka fungo la misk; kuti akapeze zimenezi, apikisane opikisana.[403] info

[403] Apa, akutilamula kupikisana pakuchita zabwino kuti tipeze madalitso amene awakonzera anthu abwino. Kumeneko ndikuti munthu aliyense alimbikire kuchita mapemphero ndi zina zabwino.

التفاسير:

external-link copy
27 : 83

وَمِزَاجُهُۥ مِن تَسۡنِيمٍ

Ndipo chosakanizira cha vinyoyo ndi madzi a Tasnim. info
التفاسير:

external-link copy
28 : 83

عَيۡنٗا يَشۡرَبُ بِهَا ٱلۡمُقَرَّبُونَ

(Tasnim ameneyo) ndi kasupe amene azikamwa amene ayandikitsidwa (kwa Allah.) info
التفاسير:

external-link copy
29 : 83

إِنَّ ٱلَّذِينَ أَجۡرَمُواْ كَانُواْ مِنَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ يَضۡحَكُونَ

Ndithu amene adachita machimo adali kuwaseka (mwachipongwe) okhulupirira (pa dziko lapansi); info
التفاسير:

external-link copy
30 : 83

وَإِذَا مَرُّواْ بِهِمۡ يَتَغَامَزُونَ

(Okhulupirira) akadutsa pafupi ndi iwo ankakodolerana maso (mwachipongwe); info
التفاسير:

external-link copy
31 : 83

وَإِذَا ٱنقَلَبُوٓاْ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِمُ ٱنقَلَبُواْ فَكِهِينَ

Ndipo akabwerera kwa anzawo amabwerera akusangalala (ndi kunyozedwa kwa okhulupirira); info
التفاسير:

external-link copy
32 : 83

وَإِذَا رَأَوۡهُمۡ قَالُوٓاْ إِنَّ هَٰٓؤُلَآءِ لَضَآلُّونَ

Ndipo (nthawi zonse) akawaona Asilamu amanena: “Ndithu awa ndi osokera (chifukwa chomkhulupirira Mtumiki).” (s.a.w) info
التفاسير:

external-link copy
33 : 83

وَمَآ أُرۡسِلُواْ عَلَيۡهِمۡ حَٰفِظِينَ

Sanatumizidwe (Akafiri) kukhala ayang’aniri kwa okhulupirira (ndikuwaweruza zakulungama ndi kusokera). info
التفاسير:

external-link copy
34 : 83

فَٱلۡيَوۡمَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مِنَ ٱلۡكُفَّارِ يَضۡحَكُونَ

Basi lero okhulupirira awaseka osakhulupirira (powabwezera chipongwe chawo chimene ankachita pa dziko lapansi),[404] info

[404] (Ndime 34-36) Tanthauzo lake ndikuti okhulupilira, tsiku lachimaliziro adzakhala m’mipando ya ulemu uku akuwayang’ana ndi kuwaseka anthu osakhulupilira ali m’mavuto monga momwe iwo adali kuseka okhulupilira pa dziko lapansi.

التفاسير:

external-link copy
35 : 83

عَلَى ٱلۡأَرَآئِكِ يَنظُرُونَ

Atakhala pa mipando ya ulemu uku akuyang’ana (mtendere umene Allah wawapatsa). info
التفاسير:

external-link copy
36 : 83

هَلۡ ثُوِّبَ ٱلۡكُفَّارُ مَا كَانُواْ يَفۡعَلُونَ

Kodi alipidwa osakhulupirira pa zomwe ankachita zija (pa dziko lapansi)? info
التفاسير: