[401] Kutsutsa kulipo kwa mitundu itatu:
(a) Kutsutsa kwa mawu ndi zochita;
(b) Kutsutsa kwa zochita zokha, monga ukauzidwa kuti chinthu ichi nchoipa, munthu nkudziwa kuti zoona nchoipadi koma nkudzachichita chimenecho mosalabadira;
(c) Kutsutsa ndi zolankhula zokha. Kumeneko ndiko monga munthu akudziwa kuti chakutichakuti ncholetsedwa (haramu) koma m’malo mwake iye nkumati chimenecho nchovomerezeka (halali)
[402] Munthu akachita choipa koyamba ndipo osalapa, limalowa dontho lakuda mu mtima mwake; nthawi iliyonse pamene akuonjezera machimo, dontho lija limakulirakulira mpaka kuuphimba mtima wonse. Dontho limeneli ndilo likutchedwa “Ran.” Tsono mtima ngati utaphimbidwa chotere sulabadira kuchita zoipa, ngakhale kuti auongole sungaongoke.
[403] Apa, akutilamula kupikisana pakuchita zabwino kuti tipeze madalitso amene awakonzera anthu abwino. Kumeneko ndikuti munthu aliyense alimbikire kuchita mapemphero ndi zina zabwino.
[404] (Ndime 34-36) Tanthauzo lake ndikuti okhulupilira, tsiku lachimaliziro adzakhala m’mipando ya ulemu uku akuwayang’ana ndi kuwaseka anthu osakhulupilira ali m’mavuto monga momwe iwo adali kuseka okhulupilira pa dziko lapansi.