クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 - Khalid Ibrahim

An-Najm

external-link copy
1 : 53

وَٱلنَّجۡمِ إِذَا هَوَىٰ

Ndikulumbira nyenyezi pamene zikulowa. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 53

مَا ضَلَّ صَاحِبُكُمۡ وَمَا غَوَىٰ

Sadasokere m’bale wanu (Mtumiki panjira ya choonadi) ndipo sadakhulupirire zonama. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 53

وَمَا يَنطِقُ عَنِ ٱلۡهَوَىٰٓ

Ndipo sayankhula zofuna za mtima wake. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 53

إِنۡ هُوَ إِلَّا وَحۡيٞ يُوحَىٰ

Iyoyi (Qur’an imene akuinena), sichina, koma ndichivumbulutso chovumbulutsidwa. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 53

عَلَّمَهُۥ شَدِيدُ ٱلۡقُوَىٰ

Adamphunzitsa (chivumbulutsochi) (Jibril) wanyonga zambiri. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 53

ذُو مِرَّةٖ فَٱسۡتَوَىٰ

Wanzeru zakuya; ndipo adakhazikika (m’maonekedwe ake). info
التفاسير:

external-link copy
7 : 53

وَهُوَ بِٱلۡأُفُقِ ٱلۡأَعۡلَىٰ

Ali m’chizimezime kumwamba. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 53

ثُمَّ دَنَا فَتَدَلَّىٰ

Kenako (Jibril) adamuyandikira (Mtumiki {s.a.w}) ndikuonjezera kumuyandikira. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 53

فَكَانَ قَابَ قَوۡسَيۡنِ أَوۡ أَدۡنَىٰ

(Kumuyandikira kwake) kudali ngati (mpata wa) nsonga ziwiri za uta, kapena kuyandikira kuposa apo. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 53

فَأَوۡحَىٰٓ إِلَىٰ عَبۡدِهِۦ مَآ أَوۡحَىٰ

(Choncho Jibril) adavumbulutsira kapolo wake (wa Allah) zimene adazivumbulutsa. info
التفاسير:

external-link copy
11 : 53

مَا كَذَبَ ٱلۡفُؤَادُ مَا رَأَىٰٓ

Sudaname mtima (wa Mtumiki) pazimene adaziona. info
التفاسير:

external-link copy
12 : 53

أَفَتُمَٰرُونَهُۥ عَلَىٰ مَا يَرَىٰ

Kodi mukutsutsana naye (Mthenga wa Allah) pazimene adaziona? info
التفاسير:

external-link copy
13 : 53

وَلَقَدۡ رَءَاهُ نَزۡلَةً أُخۡرَىٰ

Ndipo ndithu adamuona (Jibril) m’kuona kachiwiri mkaonekedwe kake. info
التفاسير:

external-link copy
14 : 53

عِندَ سِدۡرَةِ ٱلۡمُنتَهَىٰ

Pa ‘Sidratil Muntaha’ (mtengo wamasawu pothera zinthu zonse). info
التفاسير:

external-link copy
15 : 53

عِندَهَا جَنَّةُ ٱلۡمَأۡوَىٰٓ

Pafupi pake pali Janatu Ma’awa, (munda wokhalamo). info
التفاسير:

external-link copy
16 : 53

إِذۡ يَغۡشَى ٱلسِّدۡرَةَ مَا يَغۡشَىٰ

Pomwe chophimba chidaphimba msawuwo. info
التفاسير:

external-link copy
17 : 53

مَا زَاغَ ٱلۡبَصَرُ وَمَا طَغَىٰ

Maso ake sadaphonye kapena kupyola malire (oikidwa). info
التفاسير:

external-link copy
18 : 53

لَقَدۡ رَأَىٰ مِنۡ ءَايَٰتِ رَبِّهِ ٱلۡكُبۡرَىٰٓ

Ndithu (Mneneri Muhammad {s.a.w}) adaona zina mwa zizindikiro zikuluzikulu za Mbuye wake (zosonyeza mphamvu Zake) info
التفاسير:

external-link copy
19 : 53

أَفَرَءَيۡتُمُ ٱللَّٰتَ وَٱلۡعُزَّىٰ

Kodi mwamuona Laat ndi Uzza? info
التفاسير:

external-link copy
20 : 53

وَمَنَوٰةَ ٱلثَّالِثَةَ ٱلۡأُخۡرَىٰٓ

Ndi Manata; (fano lanu) lina lachitatu, (kuti iwowa ndi milungu)? info
التفاسير:

external-link copy
21 : 53

أَلَكُمُ ٱلذَّكَرُ وَلَهُ ٱلۡأُنثَىٰ

Kodi mwadzisankhira ana aamuna (kukhala anu), ndi aakazi nkukhala a Iye (Allah)? info
التفاسير:

external-link copy
22 : 53

تِلۡكَ إِذٗا قِسۡمَةٞ ضِيزَىٰٓ

Choncho kugawa kumeneko nkopanda chilungamo (pompatsa Allah zimene mumazida). info
التفاسير:

external-link copy
23 : 53

إِنۡ هِيَ إِلَّآ أَسۡمَآءٞ سَمَّيۡتُمُوهَآ أَنتُمۡ وَءَابَآؤُكُم مَّآ أَنزَلَ ٱللَّهُ بِهَا مِن سُلۡطَٰنٍۚ إِن يَتَّبِعُونَ إِلَّا ٱلظَّنَّ وَمَا تَهۡوَى ٱلۡأَنفُسُۖ وَلَقَدۡ جَآءَهُم مِّن رَّبِّهِمُ ٱلۡهُدَىٰٓ

Sali (mafanowo) chilichonse koma ndi maina basi omwe mudawatcha inu ndi makolo anu, (molingana ndi zilakolako zanu zachabe); Allah sadatsitse umboni pazimenezo (wotsimikiza pamawu anuwo). Sakutsatira koma zoganizira basi ndi zimene ikufuna mitima (yawo yopotoka). Ndithu chidawadzera chiongoko kuchokera kwa Mbuye wawo (chomwe m’kati mwake mudali kuongoka kwawo akadachitsatira). info
التفاسير:

external-link copy
24 : 53

أَمۡ لِلۡإِنسَٰنِ مَا تَمَنَّىٰ

Kodi munthu akuganiza kuti adzapeza chilichonse chimene akuchilakalaka? info
التفاسير:

external-link copy
25 : 53

فَلِلَّهِ ٱلۡأٓخِرَةُ وَٱلۡأُولَىٰ

Moyo wa tsiku lachimaliziro ndi wadziko lapansi ngwa Allah Yekha. info
التفاسير:

external-link copy
26 : 53

۞ وَكَم مِّن مَّلَكٖ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ لَا تُغۡنِي شَفَٰعَتُهُمۡ شَيۡـًٔا إِلَّا مِنۢ بَعۡدِ أَن يَأۡذَنَ ٱللَّهُ لِمَن يَشَآءُ وَيَرۡضَىٰٓ

Ndipo kuli angelo ambiri kumwamba omwe kuchondelera kwawo sikungathandize china chilichonse pokhapokha Allah ataloleza kwa amene wamfuna ndi kumuyanja. info
التفاسير:

external-link copy
27 : 53

إِنَّ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ لَيُسَمُّونَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ تَسۡمِيَةَ ٱلۡأُنثَىٰ

Ndithu amene sakhulupirira za (Moyo wa) tsiku lachimaliziro, amawatcha angelo kuti ndiakazi. info
التفاسير:

external-link copy
28 : 53

وَمَا لَهُم بِهِۦ مِنۡ عِلۡمٍۖ إِن يَتَّبِعُونَ إِلَّا ٱلظَّنَّۖ وَإِنَّ ٱلظَّنَّ لَا يُغۡنِي مِنَ ٱلۡحَقِّ شَيۡـٔٗا

Ndipo alibe kudziwa kulikonse pa zimenezo sakutsata china koma maganizo. Ndipo ndithu kuganizira sikuthandiza chilichonse pofuna kupeza choonadi. info
التفاسير:

external-link copy
29 : 53

فَأَعۡرِضۡ عَن مَّن تَوَلَّىٰ عَن ذِكۡرِنَا وَلَمۡ يُرِدۡ إِلَّا ٱلۡحَيَوٰةَ ٱلدُّنۡيَا

Choncho apewe (osakhulupirirawa) amene anyozera chikumbutso Chathu (Qur’an); ndipo palibe chimene akufuna koma moyo wa padziko lapansi basi. info
التفاسير:

external-link copy
30 : 53

ذَٰلِكَ مَبۡلَغُهُم مِّنَ ٱلۡعِلۡمِۚ إِنَّ رَبَّكَ هُوَ أَعۡلَمُ بِمَن ضَلَّ عَن سَبِيلِهِۦ وَهُوَ أَعۡلَمُ بِمَنِ ٱهۡتَدَىٰ

Zimenezo ndiwo mapeto a kudziwa kwawo. Ndithu Mbuye wako Ngodziwa kwambiri za amene akusokera njira Yake ndiponso akudziwa bwino za yemwe wawongoka. info
التفاسير:

external-link copy
31 : 53

وَلِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِ لِيَجۡزِيَ ٱلَّذِينَ أَسَٰٓـُٔواْ بِمَا عَمِلُواْ وَيَجۡزِيَ ٱلَّذِينَ أَحۡسَنُواْ بِٱلۡحُسۡنَى

Ndipo zonse za kumwamba ndi zadziko lapansi nza Allah Yekha, (pozilenga ndi kuziyang’anira), kuti adzawalipire amene adaipitsa pa zimene adachita ndi kutinso adzawalipire zabwino amene adachita zabwino. info
التفاسير:

external-link copy
32 : 53

ٱلَّذِينَ يَجۡتَنِبُونَ كَبَٰٓئِرَ ٱلۡإِثۡمِ وَٱلۡفَوَٰحِشَ إِلَّا ٱللَّمَمَۚ إِنَّ رَبَّكَ وَٰسِعُ ٱلۡمَغۡفِرَةِۚ هُوَ أَعۡلَمُ بِكُمۡ إِذۡ أَنشَأَكُم مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ وَإِذۡ أَنتُمۡ أَجِنَّةٞ فِي بُطُونِ أُمَّهَٰتِكُمۡۖ فَلَا تُزَكُّوٓاْ أَنفُسَكُمۡۖ هُوَ أَعۡلَمُ بِمَنِ ٱتَّقَىٰٓ

Amene akuwapewa machimo akuluakulu ndi zadama, kupatula timachimo tating’onoting’ono (timene Allah amatikhululuka); ndithu Mbuye wako ndiwokhululuka kwakukulu. Iye akudziwa chikhalidwe chanu kuyambira pomwe adakulengani kuchokera m’nthaka ndi pamene inu mudali makanda m’mimba mwa amayi anu (mosinthasintha; mosiyanasiyana). Choncho musadzitame nokha kuyera mtima; Iye Ngodziwa kwambiri za yemwe akumuopa (Allah). info
التفاسير:

external-link copy
33 : 53

أَفَرَءَيۡتَ ٱلَّذِي تَوَلَّىٰ

Kodi wamuona yemwe wadzipatula (pakusiya kutsatira choonadi)? info
التفاسير:

external-link copy
34 : 53

وَأَعۡطَىٰ قَلِيلٗا وَأَكۡدَىٰٓ

Ndipo wapereka (chuma) chochepa nasiyanso kuperekako. info
التفاسير:

external-link copy
35 : 53

أَعِندَهُۥ عِلۡمُ ٱلۡغَيۡبِ فَهُوَ يَرَىٰٓ

Kodi akudziwa zamseri, kotero kuti akuziwona (zomwe wadza nazo (Mtumiki {s.a.w) kuti sizoona)? info
التفاسير:

external-link copy
36 : 53

أَمۡ لَمۡ يُنَبَّأۡ بِمَا فِي صُحُفِ مُوسَىٰ

Kapena sadauzidwe zomwe zidali m’mabuku a Mûsa. info
التفاسير:

external-link copy
37 : 53

وَإِبۡرَٰهِيمَ ٱلَّذِي وَفَّىٰٓ

Ndi Ibrahim amene adakwaniritsa (lonjezo la Allah)? info
التفاسير:

external-link copy
38 : 53

أَلَّا تَزِرُ وَازِرَةٞ وِزۡرَ أُخۡرَىٰ

Kuti mzimu wamachimo sungasenze machimo a mzimu wina. info
التفاسير:

external-link copy
39 : 53

وَأَن لَّيۡسَ لِلۡإِنسَٰنِ إِلَّا مَا سَعَىٰ

Ndi kutinso munthu sakalipidwa koma zimene adachita. info
التفاسير:

external-link copy
40 : 53

وَأَنَّ سَعۡيَهُۥ سَوۡفَ يُرَىٰ

Ndipo ndithu ntchito zake zidzaonekera. info
التفاسير:

external-link copy
41 : 53

ثُمَّ يُجۡزَىٰهُ ٱلۡجَزَآءَ ٱلۡأَوۡفَىٰ

Kenako (munthu) adzalipidwa malipiro okwanira (pa ntchito zake zimene amachita). info
التفاسير:

external-link copy
42 : 53

وَأَنَّ إِلَىٰ رَبِّكَ ٱلۡمُنتَهَىٰ

Ndipo ndithu kwa Mbuye wako yekha ndiwo malekezero (a chilichonse). info
التفاسير:

external-link copy
43 : 53

وَأَنَّهُۥ هُوَ أَضۡحَكَ وَأَبۡكَىٰ

Ndithu Iye ndiAmene amapereka chisangalalo ndi zoliritsa. info
التفاسير:

external-link copy
44 : 53

وَأَنَّهُۥ هُوَ أَمَاتَ وَأَحۡيَا

Ndipo Iye yekha ndi Amene amapereka imfa ndi moyo. info
التفاسير:

external-link copy
45 : 53

وَأَنَّهُۥ خَلَقَ ٱلزَّوۡجَيۡنِ ٱلذَّكَرَ وَٱلۡأُنثَىٰ

Ndipo Iye ndiAmene adalenga mitundu iwiri: chachimuna ndi chachikazi, (anthu ndi zamoyo zina). info
التفاسير:

external-link copy
46 : 53

مِن نُّطۡفَةٍ إِذَا تُمۡنَىٰ

Kuchokera m’mbewu ya moyo pamene imafwamphukira (m’chiberekero). info
التفاسير:

external-link copy
47 : 53

وَأَنَّ عَلَيۡهِ ٱلنَّشۡأَةَ ٱلۡأُخۡرَىٰ

Ndipo ndithu ndi udindo Wake kuukitsa kwina (pambuyo pa imfa). info
التفاسير:

external-link copy
48 : 53

وَأَنَّهُۥ هُوَ أَغۡنَىٰ وَأَقۡنَىٰ

Ndipo Iye ndiAmene amapatsa chokwanira ndipo ndi amene amapatsa chosunga. info
التفاسير:

external-link copy
49 : 53

وَأَنَّهُۥ هُوَ رَبُّ ٱلشِّعۡرَىٰ

Ndipo ndithu Iye ndi Mbuye wa nyenyezi yotchedwa Shiira; info
التفاسير:

external-link copy
50 : 53

وَأَنَّهُۥٓ أَهۡلَكَ عَادًا ٱلۡأُولَىٰ

Ndipo Iye ndi amene adaononga Âdi oyamba; (anthu a Mneneri Hûd). info
التفاسير:

external-link copy
51 : 53

وَثَمُودَاْ فَمَآ أَبۡقَىٰ

Ndi Samudu; (anthu a Mneneri Swaleh;) choncho sadasiye (ndi mmodzi yemwe wa iwo). info
التفاسير:

external-link copy
52 : 53

وَقَوۡمَ نُوحٖ مِّن قَبۡلُۖ إِنَّهُمۡ كَانُواْ هُمۡ أَظۡلَمَ وَأَطۡغَىٰ

Ndipo (adawaononganso) anthu a Nuh, kale (asadaononge Âdi ndi Samudu). Ndithu iwo adali osalungama ndi olumpha malire kwambiri (kuposa Âdi ndi Samudu). info
التفاسير:

external-link copy
53 : 53

وَٱلۡمُؤۡتَفِكَةَ أَهۡوَىٰ

Ndi midzi yotembenuzidwa kumwamba kukhala pansi, pansi kukhala kumwamba, (ya anthu a Luti) adaigwetsa. info
التفاسير:

external-link copy
54 : 53

فَغَشَّىٰهَا مَا غَشَّىٰ

Tero chidaivindikira (midziyo) chomwe chidaivindikira (chilango). info
التفاسير:

external-link copy
55 : 53

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكَ تَتَمَارَىٰ

Kodi ndimtendere uti (mumtendere) wa Mbuye wako umene ukuukaikira? info
التفاسير:

external-link copy
56 : 53

هَٰذَا نَذِيرٞ مِّنَ ٱلنُّذُرِ ٱلۡأُولَىٰٓ

Uyu (Mtumiki) ndimchenjezi mwa achenjezi oyamba (amene adachenjezedwa nawo anthu a mibadwo yakale) info
التفاسير:

external-link copy
57 : 53

أَزِفَتِ ٱلۡأٓزِفَةُ

Chayandikira choyandikira (Qiyâma). info
التفاسير:

external-link copy
58 : 53

لَيۡسَ لَهَا مِن دُونِ ٱللَّهِ كَاشِفَةٌ

Palibe amene angachionetse koma Allah Yekha. info
التفاسير:

external-link copy
59 : 53

أَفَمِنۡ هَٰذَا ٱلۡحَدِيثِ تَعۡجَبُونَ

Kodi mukuidabwa nkhaniyi (ya Qur’an moikana)? info
التفاسير:

external-link copy
60 : 53

وَتَضۡحَكُونَ وَلَا تَبۡكُونَ

Mungoseka (mwachipongwe) ndipo simukulira (pamene mukuimva monga momwe akuchitira okhulupirira). info
التفاسير:

external-link copy
61 : 53

وَأَنتُمۡ سَٰمِدُونَ

Ndipo mukunyozera? info
التفاسير:

external-link copy
62 : 53

فَٱسۡجُدُواْۤ لِلَّهِۤ وَٱعۡبُدُواْ۩

Mlambireni ndi kumpembedza Allah (amene wavumbulutsa Qur’an kuti ikhale chiongoko cha anthu). info
التفاسير: