Sali (mafanowo) chilichonse koma ndi maina basi omwe mudawatcha inu ndi makolo anu, (molingana ndi zilakolako zanu zachabe); Allah sadatsitse umboni pazimenezo (wotsimikiza pamawu anuwo). Sakutsatira koma zoganizira basi ndi zimene ikufuna mitima (yawo yopotoka). Ndithu chidawadzera chiongoko kuchokera kwa Mbuye wawo (chomwe m’kati mwake mudali kuongoka kwawo akadachitsatira).
Ndipo kuli angelo ambiri kumwamba omwe kuchondelera kwawo sikungathandize china chilichonse pokhapokha Allah ataloleza kwa amene wamfuna ndi kumuyanja.
Ndipo zonse za kumwamba ndi zadziko lapansi nza Allah Yekha, (pozilenga ndi kuziyang’anira), kuti adzawalipire amene adaipitsa pa zimene adachita ndi kutinso adzawalipire zabwino amene adachita zabwino.
Ndipo (adawaononganso) anthu a Nuh, kale (asadaononge Âdi ndi Samudu). Ndithu iwo adali osalungama ndi olumpha malire kwambiri (kuposa Âdi ndi Samudu).
التفاسير:
53:53
وَٱلۡمُؤۡتَفِكَةَ أَهۡوَىٰ
Ndi midzi yotembenuzidwa kumwamba kukhala pansi, pansi kukhala kumwamba, (ya anthu a Luti) adaigwetsa.