Traduzione dei Significati del Sacro Corano - Traduzione chicheŵa - Khalid Ibrahim Betyala

Numero di pagina:close

external-link copy
59 : 24

وَإِذَا بَلَغَ ٱلۡأَطۡفَٰلُ مِنكُمُ ٱلۡحُلُمَ فَلۡيَسۡتَـٔۡذِنُواْ كَمَا ٱسۡتَـٔۡذَنَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡۚ كَذَٰلِكَ يُبَيِّنُ ٱللَّهُ لَكُمۡ ءَايَٰتِهِۦۗ وَٱللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٞ

Ndipo mwa inu ana akatha nsinkhu, aodire monga momwe adali kuodira omwe adalipo patsogolo pawo. Umo ndi momwe Allah akukufotokozerani Ayah (ndime) Zake. Ndipo Allah Ngodziwa; Ngwanzeru zakuya. info
التفاسير:

external-link copy
60 : 24

وَٱلۡقَوَٰعِدُ مِنَ ٱلنِّسَآءِ ٱلَّٰتِي لَا يَرۡجُونَ نِكَاحٗا فَلَيۡسَ عَلَيۡهِنَّ جُنَاحٌ أَن يَضَعۡنَ ثِيَابَهُنَّ غَيۡرَ مُتَبَرِّجَٰتِۭ بِزِينَةٖۖ وَأَن يَسۡتَعۡفِفۡنَ خَيۡرٞ لَّهُنَّۗ وَٱللَّهُ سَمِيعٌ عَلِيمٞ

Nayonso mikwezembe (nkhalamba zachikhalire zazikazi) yomwe siyembekezera kukwatiwa, palibe uchimo pa iyo kusiya kufunda nsalu zawo (kumutu), popanda kuonetsa zodzikongoletsera zawo. Koma ngati zikudzikakamiza kuleka kuvula mipangoyo, ndibwino kwa iyo. Ndithu Allah Ngwakumva; Ngodziwa. info
التفاسير:

external-link copy
61 : 24

لَّيۡسَ عَلَى ٱلۡأَعۡمَىٰ حَرَجٞ وَلَا عَلَى ٱلۡأَعۡرَجِ حَرَجٞ وَلَا عَلَى ٱلۡمَرِيضِ حَرَجٞ وَلَا عَلَىٰٓ أَنفُسِكُمۡ أَن تَأۡكُلُواْ مِنۢ بُيُوتِكُمۡ أَوۡ بُيُوتِ ءَابَآئِكُمۡ أَوۡ بُيُوتِ أُمَّهَٰتِكُمۡ أَوۡ بُيُوتِ إِخۡوَٰنِكُمۡ أَوۡ بُيُوتِ أَخَوَٰتِكُمۡ أَوۡ بُيُوتِ أَعۡمَٰمِكُمۡ أَوۡ بُيُوتِ عَمَّٰتِكُمۡ أَوۡ بُيُوتِ أَخۡوَٰلِكُمۡ أَوۡ بُيُوتِ خَٰلَٰتِكُمۡ أَوۡ مَا مَلَكۡتُم مَّفَاتِحَهُۥٓ أَوۡ صَدِيقِكُمۡۚ لَيۡسَ عَلَيۡكُمۡ جُنَاحٌ أَن تَأۡكُلُواْ جَمِيعًا أَوۡ أَشۡتَاتٗاۚ فَإِذَا دَخَلۡتُم بُيُوتٗا فَسَلِّمُواْ عَلَىٰٓ أَنفُسِكُمۡ تَحِيَّةٗ مِّنۡ عِندِ ٱللَّهِ مُبَٰرَكَةٗ طَيِّبَةٗۚ كَذَٰلِكَ يُبَيِّنُ ٱللَّهُ لَكُمُ ٱلۡأٓيَٰتِ لَعَلَّكُمۡ تَعۡقِلُونَ

Palibe kulakwa pa akhungu (osapenya) ndiponso palibe kulakwa pa olumala; palibenso kulakwa pa odwala, ngakhalenso pa inu eni ngati muli kudya m’nyumba zanu kapena m’nyumba za atate anu, kapena m’nyumba za amayi anu, kapena m’nyumba za abale anu, kapena m’nyumba za alongo anu, kapena m’nyumba za abambo anu ang’ono kapena akulu, kapena m’nyumba za azakhali anu, kapena m’nyumba za atsibweni anu, kapena m’nyumba za amayi anu akulu kapena ang’ono, kapena m’nyumba za omwe mukuwasungira makiyi, kapena (m’nyumba za) anzanu; palibe kulakwa pa inu ngati mukudyera limodzi kapena payekhapayekha. Ndipo mukamalowa m’nyumba dziperekereni nokha salaamu. (lonjero ili) ndi malonje ochokera kwa Allah amadalitso, abwino. Umo ndi momwe Allah akukulongosolerani Ayah (ndime) Zake kuti muzindikire. info
التفاسير: