Traduzione dei Significati del Sacro Corano - Traduzione chicheŵa - Khalid Ibrahim Betyala

Numero di pagina:close

external-link copy
62 : 24

إِنَّمَا ٱلۡمُؤۡمِنُونَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ بِٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦ وَإِذَا كَانُواْ مَعَهُۥ عَلَىٰٓ أَمۡرٖ جَامِعٖ لَّمۡ يَذۡهَبُواْ حَتَّىٰ يَسۡتَـٔۡذِنُوهُۚ إِنَّ ٱلَّذِينَ يَسۡتَـٔۡذِنُونَكَ أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ يُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦۚ فَإِذَا ٱسۡتَـٔۡذَنُوكَ لِبَعۡضِ شَأۡنِهِمۡ فَأۡذَن لِّمَن شِئۡتَ مِنۡهُمۡ وَٱسۡتَغۡفِرۡ لَهُمُ ٱللَّهَۚ إِنَّ ٱللَّهَ غَفُورٞ رَّحِيمٞ

Ndithu okhulupirira (owona) ndiamene akhulupirira mwa Allah ndi Mtumiki Wake; ndipo akakhala naye pa chinthu chokhudza onse, sachoka mpaka atampempha (Mtumiki) chilolezo. Ndithu amene akukupempha chilolezo, iwowo ndi amene akukhulupirira Allah ndi Mtumiki Wake. Choncho akakupempha chilolezo chifukwa cha zinthu zawo zina, muloleze mwa iwo amene wamfuna (ngati utaona kuti chidandaulo chake nchoona), ndipo uwapemphere chikhululuko kwa Allah; ndithu Allah Ngokhululuka kwabasi; Ngwachisoni chosatha. info
التفاسير:

external-link copy
63 : 24

لَّا تَجۡعَلُواْ دُعَآءَ ٱلرَّسُولِ بَيۡنَكُمۡ كَدُعَآءِ بَعۡضِكُم بَعۡضٗاۚ قَدۡ يَعۡلَمُ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ يَتَسَلَّلُونَ مِنكُمۡ لِوَاذٗاۚ فَلۡيَحۡذَرِ ٱلَّذِينَ يُخَالِفُونَ عَنۡ أَمۡرِهِۦٓ أَن تُصِيبَهُمۡ فِتۡنَةٌ أَوۡ يُصِيبَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٌ

Kumuitana Mtumiki pakati panu musakuchite monga momwe mumaitanirana nokhanokha, ndithu Allah akudziwa amene akuchoka pamalo mozemba ndi modzibisa mwa inu. Choncho achenjere amene akunyozera lamulo lake kuti mliri ungawapeze, kapena kuwapeza chilango chowawa. info
التفاسير:

external-link copy
64 : 24

أَلَآ إِنَّ لِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ قَدۡ يَعۡلَمُ مَآ أَنتُمۡ عَلَيۡهِ وَيَوۡمَ يُرۡجَعُونَ إِلَيۡهِ فَيُنَبِّئُهُم بِمَا عَمِلُواْۗ وَٱللَّهُ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمُۢ

Mverani! Ndithu zili kumwamba ndi pansi nzake Allah, ndipo akudziwa zimene muli nazo. Ndipo patsiku limene adzabwezedwe kwa Iye, adzawauza zimene adachita ndipo Allah Ngodziwa chilichonse. info
التفاسير: