Traduzione dei Significati del Sacro Corano - Traduzione chicheŵa - Khalid Ibrahim Betyala

Numero di pagina:close

external-link copy
56 : 22

ٱلۡمُلۡكُ يَوۡمَئِذٖ لِّلَّهِ يَحۡكُمُ بَيۡنَهُمۡۚ فَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فِي جَنَّٰتِ ٱلنَّعِيمِ

Ufumu tsiku limenelo ngwa Allah; adzaweruza (mwachilungamo) pakati pawo; choncho amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, adzakhala m’Minda yamtendere. info
التفاسير:

external-link copy
57 : 22

وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَكَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا فَأُوْلَٰٓئِكَ لَهُمۡ عَذَابٞ مُّهِينٞ

Ndipo amene sadakhulupirire (Allah ndi Mtumiki Wake) ndikutsutsa Ayah Zathu, iwo adzapeza chilango choyalutsa. info
التفاسير:

external-link copy
58 : 22

وَٱلَّذِينَ هَاجَرُواْ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ ثُمَّ قُتِلُوٓاْ أَوۡ مَاتُواْ لَيَرۡزُقَنَّهُمُ ٱللَّهُ رِزۡقًا حَسَنٗاۚ وَإِنَّ ٱللَّهَ لَهُوَ خَيۡرُ ٱلرَّٰزِقِينَ

Ndipo amene asamuka chifukwa cha chipembedzo cha Allah, kenako ndikuphedwa kapena kufa, ndithu Allah adzawapatsa (patsiku la chiweruziro) zopatsa zabwino. Ndithu Allah Ngwabwino popatsa kuposa opatsa. info
التفاسير:

external-link copy
59 : 22

لَيُدۡخِلَنَّهُم مُّدۡخَلٗا يَرۡضَوۡنَهُۥۚ وَإِنَّ ٱللَّهَ لَعَلِيمٌ حَلِيمٞ

Ndithu adzawalowetsa pamalo pomwe adzapayanja. Ndithu Allah Ngodziwa; Ngodekha. info
التفاسير:

external-link copy
60 : 22

۞ ذَٰلِكَۖ وَمَنۡ عَاقَبَ بِمِثۡلِ مَا عُوقِبَ بِهِۦ ثُمَّ بُغِيَ عَلَيۡهِ لَيَنصُرَنَّهُ ٱللَّهُۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَعَفُوٌّ غَفُورٞ

Zimenezi zili chonchi, ndipo yemwe akubwezera kulanga molingana ndi momwe iye adalangidwira; kenakonso nkuchitidwa mtopola, ndithu Allah amthangata; Allah Ngofufuta uchimo; Wokhululuka kwambiri. info
التفاسير:

external-link copy
61 : 22

ذَٰلِكَ بِأَنَّ ٱللَّهَ يُولِجُ ٱلَّيۡلَ فِي ٱلنَّهَارِ وَيُولِجُ ٱلنَّهَارَ فِي ٱلَّيۡلِ وَأَنَّ ٱللَّهَ سَمِيعُۢ بَصِيرٞ

Zimenezo nchifukwa chakuti Allah amalowetsa usiku mu usana ndikulowetsa usana mu usiku, ndi chifukwanso chakuti ndithu Allah Ngwakumva Ngopenya. info
التفاسير:

external-link copy
62 : 22

ذَٰلِكَ بِأَنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡحَقُّ وَأَنَّ مَا يَدۡعُونَ مِن دُونِهِۦ هُوَ ٱلۡبَٰطِلُ وَأَنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡعَلِيُّ ٱلۡكَبِيرُ

Zimenezo nchifukwa chakuti Allah ndi Wowona (alipo;) ndipo zimene akuzipembedza kusiya Iye, nzachabe. Ndipo Allah Ngwapamwambamwamba Ngwamkulu. info
التفاسير:

external-link copy
63 : 22

أَلَمۡ تَرَ أَنَّ ٱللَّهَ أَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَتُصۡبِحُ ٱلۡأَرۡضُ مُخۡضَرَّةًۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَطِيفٌ خَبِيرٞ

Kodi suona kuti Allah amatsitsa madzi kuchokera ku mitambo, ndipo nthaka imakhala yobiriwira? Ndithu Allah Ngodziwa zobisika ndiponso Ngodziwa zoonekera. info
التفاسير:

external-link copy
64 : 22

لَّهُۥ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۚ وَإِنَّ ٱللَّهَ لَهُوَ ٱلۡغَنِيُّ ٱلۡحَمِيدُ

Zakumwamba ndi zapansi zonse ndizake; ndithu Allah Ngwachikwanekwane; Wotamandidwa. info
التفاسير: