Traduzione dei Significati del Sacro Corano - Traduzione chicheŵa - Khalid Ibrahim Betyala

Numero di pagina:close

external-link copy
47 : 22

وَيَسۡتَعۡجِلُونَكَ بِٱلۡعَذَابِ وَلَن يُخۡلِفَ ٱللَّهُ وَعۡدَهُۥۚ وَإِنَّ يَوۡمًا عِندَ رَبِّكَ كَأَلۡفِ سَنَةٖ مِّمَّا تَعُدُّونَ

Ndipo akukufulumizitsa kuti udzetse chilango. Komatu Allah sadzaswa lonjezo Lake (limene adaliika lakuti chilango chenicheni chidzakhala patsiku la chimaliziro). Ndipo ndithu tsiku limodzi kwa Mbuye wako lili ngati zaka chikwi chimodzi mukawerengedwe kanu. info
التفاسير:

external-link copy
48 : 22

وَكَأَيِّن مِّن قَرۡيَةٍ أَمۡلَيۡتُ لَهَا وَهِيَ ظَالِمَةٞ ثُمَّ أَخَذۡتُهَا وَإِلَيَّ ٱلۡمَصِيرُ

Kodi ndi (anthu a) midzi ingati amene ndidawapatsa nthawi pomwe ankachita zoipa? Kenako ndidawathira m’dzanja. Ndipo kwa Iye nkobwerera. info
التفاسير:

external-link copy
49 : 22

قُلۡ يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ إِنَّمَآ أَنَا۠ لَكُمۡ نَذِيرٞ مُّبِينٞ

Nena: “E inu anthu! Ndithu ine kwa inu ndine Mchenjezi woonekera.” info
التفاسير:

external-link copy
50 : 22

فَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَهُم مَّغۡفِرَةٞ وَرِزۡقٞ كَرِيمٞ

“Tsono amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, chikhululuko ndi rizq laulemu zili pa iwo.” info
التفاسير:

external-link copy
51 : 22

وَٱلَّذِينَ سَعَوۡاْ فِيٓ ءَايَٰتِنَا مُعَٰجِزِينَ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡجَحِيمِ

“Ndipo amene akulimbikira kulimbana ndi Ayah Zathu, iwowo ndi anthu a ku Moto.” info
التفاسير:

external-link copy
52 : 22

وَمَآ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ مِن رَّسُولٖ وَلَا نَبِيٍّ إِلَّآ إِذَا تَمَنَّىٰٓ أَلۡقَى ٱلشَّيۡطَٰنُ فِيٓ أُمۡنِيَّتِهِۦ فَيَنسَخُ ٱللَّهُ مَا يُلۡقِي ٱلشَّيۡطَٰنُ ثُمَّ يُحۡكِمُ ٱللَّهُ ءَايَٰتِهِۦۗ وَٱللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٞ

Ndipo palibe pamene tidatuma mtumiki ngakhale m’neneri patsogolo pako, koma akamawerenga, satana amaponya (zosokoneza) m’kuwerenga kwakeko; koma Allah amachotsa zomwe satana akuponya; kenako nkuzilongosola Ayah Zake. Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri, Wanzeru zakuya. info
التفاسير:

external-link copy
53 : 22

لِّيَجۡعَلَ مَا يُلۡقِي ٱلشَّيۡطَٰنُ فِتۡنَةٗ لِّلَّذِينَ فِي قُلُوبِهِم مَّرَضٞ وَٱلۡقَاسِيَةِ قُلُوبُهُمۡۗ وَإِنَّ ٱلظَّٰلِمِينَ لَفِي شِقَاقِۭ بَعِيدٖ

(Izi zimachitika) kuti achichite chimene satana akuponya kukhala mayeso kwa omwe m’mitima mwawo muli matenda ndi ouma mitima yawo; ndithu osalungama ali m’kusiyana komwe kuli kutali (ndi choonadi). info
التفاسير:

external-link copy
54 : 22

وَلِيَعۡلَمَ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡعِلۡمَ أَنَّهُ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّكَ فَيُؤۡمِنُواْ بِهِۦ فَتُخۡبِتَ لَهُۥ قُلُوبُهُمۡۗ وَإِنَّ ٱللَّهَ لَهَادِ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ

Ndipo kuti adziwe amene apatsidwa kuzindikira kuti chimenechi n’choonadi chochokera kwa Mbuye wako ndi kuchikhulupirira ndikuti mitima yawo idzichepetse kwa Iye; ndithu Allah ndi Woongolera ku njira yolunjika amene akhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
55 : 22

وَلَا يَزَالُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ فِي مِرۡيَةٖ مِّنۡهُ حَتَّىٰ تَأۡتِيَهُمُ ٱلسَّاعَةُ بَغۡتَةً أَوۡ يَأۡتِيَهُمۡ عَذَابُ يَوۡمٍ عَقِيمٍ

Ndipo amene sadakhulupirire apitilira kukhala m’chikaiko ndi chimenecho (wadza nachocho) kufikira tsiku la chimaliziro liwadzera mowatutumutsa, kapena chiwadzera chilango pa tsiku lopanda chabwino (kwa iwo). info
التفاسير: