[158] Chakudya chozingidwa sichingakhale chovomerezeka kwa Asilamu pokhapokha chitazingidwa ndi Asilamu. Izi zili ngati atatsatira malamulo akazingidwe, osati kupotokola khosi, kapena kumenya ndimyala kapena chibonga. Tsono chakudya chozingidwa nchovomerezeka kwa Msilamu kuchidya ngakhale chitakonzedwa ndi achikunja (akafiri) ngati:- (a) simudaone kuti athiramo najisi (uve) (b) Sichili chakudya choletsedwa. Nkovomerezeka kwa mwamuna wa Chisilamu kukwatira:- (a) Mkazi wa Chiyuda (b) Mkazi wa Chikhrisitu ngati makolo awo adali Ayuda kapena Akhrisitu chisilamu chisanadze.
N.B! Koma awa a Mishoni omwe alowa m’Chikhrisitu posachedwapa nkosaloledwa kuwakwatira pokhapokha atayamba alowa m’Chisilamu Tsono mkazi wa Chisilamu nkosaloledwa kukwatiwa ndi myuda kapena mkhrisitu. Ndipo apa apitirizanso machitidwe achiwerewere chomangira nyumba ndi chapatchire. Munthu akafuna kukwatira mkazi atsate mfundo zikudzazi kuti ukwati wakewo ukhale wovomerezeka pa malamulo a Chisilamu:- (a) Mkazi alole kukwatiwa ndi mwamunayo. (b) Myang’aniri wa wamkazi apereke kwa munthu chilolezo choti akwatitsire mkazi uja, kapena amkwatitse iye mwini pomuuza mkwati kuti “Ndakukwatitsa uje mwana wa uje.’’ (c) Mkwati avomereze kuti: “Ndavomera kumkwatira uje, mwana wa uje’.’ (d) Pakhale anthu aamuna oikira umboni osachepera pa awiri. Anthuwo akhale aulemu wawo pamaso pa anthu. (e) Chiperekedwe chiongo. (f) Iwerengedwe khutba ya ukwati.