Fassarar Ma'anonin Alqura'ni - Fassara da harshan Shishiyo - Khalid Ibrahim Bitala

Lambar shafi:close

external-link copy
44 : 24

يُقَلِّبُ ٱللَّهُ ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَعِبۡرَةٗ لِّأُوْلِي ٱلۡأَبۡصَٰرِ

Allah amasintha usiku ndi usana (pambuyo pa usiku, umadza usana, ndipo pambuyo pa usana, umadza usiku). Ndithu m’zimenezo muli phunziro kwa anthu ozindikira (zinthu). info
التفاسير:

external-link copy
45 : 24

وَٱللَّهُ خَلَقَ كُلَّ دَآبَّةٖ مِّن مَّآءٖۖ فَمِنۡهُم مَّن يَمۡشِي عَلَىٰ بَطۡنِهِۦ وَمِنۡهُم مَّن يَمۡشِي عَلَىٰ رِجۡلَيۡنِ وَمِنۡهُم مَّن يَمۡشِي عَلَىٰٓ أَرۡبَعٖۚ يَخۡلُقُ ٱللَّهُ مَا يَشَآءُۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ

Ndipo Allah adalenga ndi madzi nyama iliyonse; (madzi ndicho chiyambi cha zolengedwa zonse). Zina mwa izo zimayendera mimba zawo; ndipo zina mwa izo zimayenda ndi miyendo iwiri; ndipo zina mwa izo zimayenda ndi inayi. Ndithu Allah amalenga chimene wafuna; ndithu Allah ali ndi mphamvu pa chilichonse. info
التفاسير:

external-link copy
46 : 24

لَّقَدۡ أَنزَلۡنَآ ءَايَٰتٖ مُّبَيِّنَٰتٖۚ وَٱللَّهُ يَهۡدِي مَن يَشَآءُ إِلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ

Ndithu tavumbulutsa Ayah (ndime) zofotokoza momveka (chilichonse chofunika pa chipembedzo). Ndipo Allah amamuongolera ku njira yolunjika amene wamfuna. info
التفاسير:

external-link copy
47 : 24

وَيَقُولُونَ ءَامَنَّا بِٱللَّهِ وَبِٱلرَّسُولِ وَأَطَعۡنَا ثُمَّ يَتَوَلَّىٰ فَرِيقٞ مِّنۡهُم مِّنۢ بَعۡدِ ذَٰلِكَۚ وَمَآ أُوْلَٰٓئِكَ بِٱلۡمُؤۡمِنِينَ

Ndipo akunena (kuti): “Takhulupirira Allah ndi Mtumiki, ndipo tamvera.” Kenako ena a iwo amatembenuka pambuyo pa zimenezo; ndipo iwowo sali okhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
48 : 24

وَإِذَا دُعُوٓاْ إِلَى ٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦ لِيَحۡكُمَ بَيۡنَهُمۡ إِذَا فَرِيقٞ مِّنۡهُم مُّعۡرِضُونَ

Ndipo akawaitanira kwa Allah ndi Mtumiki Wake kuti awaweruze pakati pawo, ena a iwo akukana zimenezo (akadzizindikira okha kuti ngolakwa). info
التفاسير:

external-link copy
49 : 24

وَإِن يَكُن لَّهُمُ ٱلۡحَقُّ يَأۡتُوٓاْ إِلَيۡهِ مُذۡعِنِينَ

Koma akaona kuti chilungamo chili kwa iwo, amam’dzera (Mtumiki mwachangu) uku akusonyeza kumvera. info
التفاسير:

external-link copy
50 : 24

أَفِي قُلُوبِهِم مَّرَضٌ أَمِ ٱرۡتَابُوٓاْ أَمۡ يَخَافُونَ أَن يَحِيفَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِمۡ وَرَسُولُهُۥۚ بَلۡ أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلظَّٰلِمُونَ

Kodi ali ndi matenda m’mitima mwawo? Kapena akukaika, kapena akuopa kuti Allah ndi Mtumiki Wake awachitira chinyengo? Koma iwo ndi amene ali osalungama. info
التفاسير:

external-link copy
51 : 24

إِنَّمَا كَانَ قَوۡلَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ إِذَا دُعُوٓاْ إِلَى ٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦ لِيَحۡكُمَ بَيۡنَهُمۡ أَن يَقُولُواْ سَمِعۡنَا وَأَطَعۡنَاۚ وَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُفۡلِحُونَ

Ndithu yankho la okhulupirira akaitanidwa kwa Allah ndi Mtumiki Wake kuti aweruze pakati pawo silikhala lina koma kunena kuti: “Tamva ndipo titsatira.” Iwowo ndiwo opambana. info
التفاسير:

external-link copy
52 : 24

وَمَن يُطِعِ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ وَيَخۡشَ ٱللَّهَ وَيَتَّقۡهِ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡفَآئِزُونَ

Ndipo amene amvera Allah ndi Mtumiki Wake, ndikumalemekeza Allah ndi kumuopa, iwowo ndiwo opambana. info
التفاسير:

external-link copy
53 : 24

۞ وَأَقۡسَمُواْ بِٱللَّهِ جَهۡدَ أَيۡمَٰنِهِمۡ لَئِنۡ أَمَرۡتَهُمۡ لَيَخۡرُجُنَّۖ قُل لَّا تُقۡسِمُواْۖ طَاعَةٞ مَّعۡرُوفَةٌۚ إِنَّ ٱللَّهَ خَبِيرُۢ بِمَا تَعۡمَلُونَ

Ndipo akulumbilira dzina la Allah, kulumbira kwakukulu kuti ukawalamula (kupita ku nkhondo), ndithu apita. Nena: “Musalumbire; kumvera kwanu nkodziwika (kuti nkwabodza); ndithu Allah akudziwa nkhani zonse zomwe muchita. info
التفاسير: