Fassarar Ma'anonin Alqura'ni - Fassara da harshan Shishiyo - Khalid Ibrahim Bitala

external-link copy
224 : 2

وَلَا تَجۡعَلُواْ ٱللَّهَ عُرۡضَةٗ لِّأَيۡمَٰنِكُمۡ أَن تَبَرُّواْ وَتَتَّقُواْ وَتُصۡلِحُواْ بَيۡنَ ٱلنَّاسِۚ وَٱللَّهُ سَمِيعٌ عَلِيمٞ

Ndipo kulumbilira kwanu dzina la Allah musakuchite kukhala chokuletsani kuchita zinthu zabwino (za m’Chisilamu) ndi kuopa Allah, ndi kuyanjanitsa pakati pa anthu. Ndipo Allah Ngwakumva, Ngodziwa.[33] info

[33] Munthu ngati atalumbira kuti sachita chakutichakuti monga kunena kuti, “ndikulumbira Allah sindidzayankhulana naye uje”, asasiye kukamba naye munthuyo chifukwa chakuti adalumbilira kusayankhulana naye. Koma ayankhulane naye pambuyo popereka dipo kwa masikini pa zomwe adalumbirazo.

التفاسير: