Fassarar Ma'anonin Alqura'ni - Fassara da harshan Shishiyo - Khalid Ibrahim Bitala

external-link copy
51 : 12

قَالَ مَا خَطۡبُكُنَّ إِذۡ رَٰوَدتُّنَّ يُوسُفَ عَن نَّفۡسِهِۦۚ قُلۡنَ حَٰشَ لِلَّهِ مَا عَلِمۡنَا عَلَيۡهِ مِن سُوٓءٖۚ قَالَتِ ٱمۡرَأَتُ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡـَٰٔنَ حَصۡحَصَ ٱلۡحَقُّ أَنَا۠ رَٰوَدتُّهُۥ عَن نَّفۡسِهِۦ وَإِنَّهُۥ لَمِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ

(Mfumu idasonkhanitsa akazi aja ndipo) idati: “Kodi nkhani yanu njotani pamene mudamulakalaka Yûsuf pomwe iye sakufuna?” Adati: “Hasha Lillah! (Tikudzitchinjiriza kwa Allah)! Ife sitidadziwe choipa chilichonse kwa iye. (Tidayesayesa kuti achite nafe choipa koma sadalole).” (Nayenso) mkazi wa nduna adati: “Tsopano choonadi chatsimikizika; ine ndine amene ndidamulakalaka pomwe iye sakufuna. Ndithu iye ndi mmodzi mwa owona.” info
التفاسير: