Fassarar Ma'anonin Alqura'ni - Fassara da harshan Shishiyo - Khalid Ibrahim Bitala

Lambar shafi: 243:235 close

external-link copy
70 : 12

فَلَمَّا جَهَّزَهُم بِجَهَازِهِمۡ جَعَلَ ٱلسِّقَايَةَ فِي رَحۡلِ أَخِيهِ ثُمَّ أَذَّنَ مُؤَذِّنٌ أَيَّتُهَا ٱلۡعِيرُ إِنَّكُمۡ لَسَٰرِقُونَ

Ndipo pamene adawakonzera chakudya chawo, adaika chikho chomwera madzi mumtolo wa m’bale wakeyo. Kenako woitana adaitana: “E inu a paulendo! Ndithu inu ndinu akuba.” info
التفاسير:

external-link copy
71 : 12

قَالُواْ وَأَقۡبَلُواْ عَلَيۡهِم مَّاذَا تَفۡقِدُونَ

(Onse abale ake a Yûsuf) pamene adawacheukira, adati: “Kodi mukusowa chiyani?” info
التفاسير:

external-link copy
72 : 12

قَالُواْ نَفۡقِدُ صُوَاعَ ٱلۡمَلِكِ وَلِمَن جَآءَ بِهِۦ حِمۡلُ بَعِيرٖ وَأَنَا۠ بِهِۦ زَعِيمٞ

Adati: “Tikusowa muyeso wa Mfumu; ndipo amene aubweretse, alandira mtolo wangamira yathunthu.” (Ndipo Mneneri Yûsuf adati): “Ndipo ine ndine muimiliri pa zimenezi.” info
التفاسير:

external-link copy
73 : 12

قَالُواْ تَٱللَّهِ لَقَدۡ عَلِمۡتُم مَّا جِئۡنَا لِنُفۡسِدَ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَمَا كُنَّا سَٰرِقِينَ

(Iwo) adati: “Tikulumbira Allah! Ndithu inu mukudziwa kuti sitidadze kudzaononga m’dziko, ndiponso sitili akuba.” info
التفاسير:

external-link copy
74 : 12

قَالُواْ فَمَا جَزَٰٓؤُهُۥٓ إِن كُنتُمۡ كَٰذِبِينَ

Adati: “Mphoto (chilango) yake ikhala yotani ngati mukunena bodza?” info
التفاسير:

external-link copy
75 : 12

قَالُواْ جَزَٰٓؤُهُۥ مَن وُجِدَ فِي رَحۡلِهِۦ فَهُوَ جَزَٰٓؤُهُۥۚ كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلظَّٰلِمِينَ

Adati: “Mphoto yake ndi yemwe (chikhocho) chapezeka mu mtolo wake, iye ndiye mphoto yake. (Agwidwe monga kapolo kwa chaka chimodzi).” Umu ndi momwe timawalipirira anthu achinyengo. info
التفاسير:

external-link copy
76 : 12

فَبَدَأَ بِأَوۡعِيَتِهِمۡ قَبۡلَ وِعَآءِ أَخِيهِ ثُمَّ ٱسۡتَخۡرَجَهَا مِن وِعَآءِ أَخِيهِۚ كَذَٰلِكَ كِدۡنَا لِيُوسُفَۖ مَا كَانَ لِيَأۡخُذَ أَخَاهُ فِي دِينِ ٱلۡمَلِكِ إِلَّآ أَن يَشَآءَ ٱللَّهُۚ نَرۡفَعُ دَرَجَٰتٖ مَّن نَّشَآءُۗ وَفَوۡقَ كُلِّ ذِي عِلۡمٍ عَلِيمٞ

Ndipo (mneneri Yûsuf) adayamba kufufuza m’mitolo mwawo asanafufuze mu mtolo wa m’bale wake; kenako adachitulutsa mu mtolo wa m’bale wake. Umu ndi momwe tidamlinganizira ndale Yûsuf (kuti ampeze m’bale wake). Mwachilamulo cha mfumu (ya m’dzikolo) sakadamutenga m’bale wake (monga kapolo) koma mmene Allah adafunira (powaonetsa abale ake za chilamulo cha kwawo chomuika mu ukapolo munthu wakuba). Timawakwezera pa ulemelero amene tawafuna. Ndipo pa wodziwa aliyense pali wodziwanso kuposa iye. info
التفاسير:

external-link copy
77 : 12

۞ قَالُوٓاْ إِن يَسۡرِقۡ فَقَدۡ سَرَقَ أَخٞ لَّهُۥ مِن قَبۡلُۚ فَأَسَرَّهَا يُوسُفُ فِي نَفۡسِهِۦ وَلَمۡ يُبۡدِهَا لَهُمۡۚ قَالَ أَنتُمۡ شَرّٞ مَّكَانٗاۖ وَٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِمَا تَصِفُونَ

(Iwo) adati: “Ngati waba, m’bale wakenso adabapo kale.” (Uku kudali kumunamizira Yûsuf bodza pomwe iwo sankadziwa kuti yemwe akuyankhula nayeyo ndiye Yûsuf). Koma Yûsuf adabisa (mawu awa) mu mtima mwake, (chifukwa chowamvera chisoni) ndipo sadawaululire. Adati: “Inu muli ndi chikhalidwe choipa ndipo Allah akudziwa zomwe mukunena!” info
التفاسير:

external-link copy
78 : 12

قَالُواْ يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡعَزِيزُ إِنَّ لَهُۥٓ أَبٗا شَيۡخٗا كَبِيرٗا فَخُذۡ أَحَدَنَا مَكَانَهُۥٓۖ إِنَّا نَرَىٰكَ مِنَ ٱلۡمُحۡسِنِينَ

(Iwo) adati: “E inu bwana! Uyu ali ndi bambo wake wokalamba kwambiri; choncho tengani mmodzi wa ife mmalo mwake; ndithudi, ife tikuona kuti inu ndinu mmodzi mwa ochita zabwino.” info
التفاسير: