[310] Malembo awa akudziwitsa kuti Qur’an idalembedwa mwachidule chomveka ndi kulozera kuti bukuli lomwe ilo anthu anzeru zakuya akulephera kulemba, lapangika kuchokera m’malembo amenewa omwe anthu akuwadziwa ndi kugwiritsa ntchito. Ngati iwo ali ndi chipeneko kuti silidachokere kwa Allah, koma kuti Muhammad (s.a.w) adangolilemba yekha ngakhale kuti adali wosadziwa kulemba, alembe buku lawo longa ili. Malembo a bukuli ndi omwenso iwo amawadziwa. Komatu sangathe kulemba buku longa ili ngakhale anthu onse a m’dziko lapansi atathandizana. Uwu ndi umboni waukulu umene ukusonyeza kuti bukuli lidachokera kwa Allah.
[311] M’ndime iyi Allah akutifotokozera kuti adalenga thambo monga lilili m’kukula kwake ndi m’kuphanuka kwake ndi kulimba kwake popanda mizati yolichirikiza. Ndipo inu anthu mukuliona mmene lili lopanda chilichonse choligwira koma mphamvu za Allah Wamkulu Wapamwambamwamba.
Ndipo m’nthaka adaikamo mapiri akuluakulu kuti nthaka isamagwedezeke ndi kumakusowetsani mtendere, kapena kumakugumulirani nyumba zanu. Ndipo Allah adafalitsa padziko zamoyo zochuluka ndi kumeretsa mbewu zosiyanasiyana. Zonsezi zikusonyeza mphamvu Zake zoopsa.