Salin ng mga Kahulugan ng Marangal na Qur'an - Salin sa Wikang Chichewa ni Khalid Ibrahim Bityala

Luqmân

external-link copy
1 : 31

الٓمٓ

Alif-Lâm-Mîm.[310] info

[310] Malembo awa akudziwitsa kuti Qur’an idalembedwa mwachidule chomveka ndi kulozera kuti bukuli lomwe ilo anthu anzeru zakuya akulephera kulemba, lapangika kuchokera m’malembo amenewa omwe anthu akuwadziwa ndi kugwiritsa ntchito. Ngati iwo ali ndi chipeneko kuti silidachokere kwa Allah, koma kuti Muhammad (s.a.w) adangolilemba yekha ngakhale kuti adali wosadziwa kulemba, alembe buku lawo longa ili. Malembo a bukuli ndi omwenso iwo amawadziwa. Komatu sangathe kulemba buku longa ili ngakhale anthu onse a m’dziko lapansi atathandizana. Uwu ndi umboni waukulu umene ukusonyeza kuti bukuli lidachokera kwa Allah.

التفاسير:

external-link copy
2 : 31

تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱلۡكِتَٰبِ ٱلۡحَكِيمِ

Izi ndi Ayah za buku lodzadza ndi nzeru. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 31

هُدٗى وَرَحۡمَةٗ لِّلۡمُحۡسِنِينَ

(Lomwe ndi) chiongoko ndi chifundo kwa ochita zabwino, info
التفاسير:

external-link copy
4 : 31

ٱلَّذِينَ يُقِيمُونَ ٱلصَّلَوٰةَ وَيُؤۡتُونَ ٱلزَّكَوٰةَ وَهُم بِٱلۡأٓخِرَةِ هُمۡ يُوقِنُونَ

Amene akupemphera Swala moyenera ndi kupereka chopereka (Zakaat) omwenso akutsimikiza za tsiku lachimaliziro. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 31

أُوْلَٰٓئِكَ عَلَىٰ هُدٗى مِّن رَّبِّهِمۡۖ وَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُفۡلِحُونَ

Iwowo ali pa chiongoko chochokera kwa Mbuye wawo; ndipo iwowo ndiwo opambana. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 31

وَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن يَشۡتَرِي لَهۡوَ ٱلۡحَدِيثِ لِيُضِلَّ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ بِغَيۡرِ عِلۡمٖ وَيَتَّخِذَهَا هُزُوًاۚ أُوْلَٰٓئِكَ لَهُمۡ عَذَابٞ مُّهِينٞ

Koma alipo ena mwa anthu amene akusankha nkhani ya bodza (ndi kumaifotokoza kwa anthu) ndi cholinga choti awasokeretse ku njira ya Allah popanda kuzindikira. Ndipo akuichitira zachipongwe (njira ya Allah yi). Iwo adzapeza chilango chowasambula. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 31

وَإِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِ ءَايَٰتُنَا وَلَّىٰ مُسۡتَكۡبِرٗا كَأَن لَّمۡ يَسۡمَعۡهَا كَأَنَّ فِيٓ أُذُنَيۡهِ وَقۡرٗاۖ فَبَشِّرۡهُ بِعَذَابٍ أَلِيمٍ

Ndipo pamene Ayah Zathu zilakatulidwa kwa iye, akuzitembenuzira msana modzikuza ngati kuti sanazimve, ngati kutinso m’makutu mwake muli ugonthi. Choncho muuze nkhani ya chilango chopweteka. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 31

إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَهُمۡ جَنَّٰتُ ٱلنَّعِيمِ

Ndithu amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, adzakhala ndi Minda yamtendere. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 31

خَٰلِدِينَ فِيهَاۖ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقّٗاۚ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ

Adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Ili nlonjezo la Allah lomwe lili loona. Ndipo Iye Ngwamphamvu, Ngwanzeru zakuya. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 31

خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ بِغَيۡرِ عَمَدٖ تَرَوۡنَهَاۖ وَأَلۡقَىٰ فِي ٱلۡأَرۡضِ رَوَٰسِيَ أَن تَمِيدَ بِكُمۡ وَبَثَّ فِيهَا مِن كُلِّ دَآبَّةٖۚ وَأَنزَلۡنَا مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَأَنۢبَتۡنَا فِيهَا مِن كُلِّ زَوۡجٖ كَرِيمٍ

Adalenga thambo popanda mizati yomwe mukuiona. Ndipo adaika mapiri m’nthaka kuti isakugwedezeni. Ndipo (Iye) adafalitsa nyama m’menemo zamitundu yosiyanasiyana. Ndipo tidatsitsa madzi kuchokera ku mitambo, choncho tidameretsa m’menemo (m’nthaka) mmera wokongola wamitundu yosiyanasiyana.[311] info

[311] M’ndime iyi Allah akutifotokozera kuti adalenga thambo monga lilili m’kukula kwake ndi m’kuphanuka kwake ndi kulimba kwake popanda mizati yolichirikiza. Ndipo inu anthu mukuliona mmene lili lopanda chilichonse choligwira koma mphamvu za Allah Wamkulu Wapamwambamwamba.
Ndipo m’nthaka adaikamo mapiri akuluakulu kuti nthaka isamagwedezeke ndi kumakusowetsani mtendere, kapena kumakugumulirani nyumba zanu. Ndipo Allah adafalitsa padziko zamoyo zochuluka ndi kumeretsa mbewu zosiyanasiyana. Zonsezi zikusonyeza mphamvu Zake zoopsa.

التفاسير:

external-link copy
11 : 31

هَٰذَا خَلۡقُ ٱللَّهِ فَأَرُونِي مَاذَا خَلَقَ ٱلَّذِينَ مِن دُونِهِۦۚ بَلِ ٱلظَّٰلِمُونَ فِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٖ

Izi (zonse) nzolengedwa za Allah. Choncho, tandisonyezani, nchiyani adalenga amene sali Allah. Koma odzichitira okha zoipa ali mkusokera koonekera. info
التفاسير: