Traduction des sens du Noble Coran - La traduction tchétchène - Khâlid Ibrâhîm Bîtâlâ

Numéro de la page:close

external-link copy
98 : 11

يَقۡدُمُ قَوۡمَهُۥ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ فَأَوۡرَدَهُمُ ٱلنَّارَۖ وَبِئۡسَ ٱلۡوِرۡدُ ٱلۡمَوۡرُودُ

Tsiku la Qiyâma, (Farawo) adzawatsogolera anthu ake ndi kuwafikitsa ku Moto. Ndipo taonani pamalo poipa kufikirapo. info
التفاسير:

external-link copy
99 : 11

وَأُتۡبِعُواْ فِي هَٰذِهِۦ لَعۡنَةٗ وَيَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۚ بِئۡسَ ٱلرِّفۡدُ ٱلۡمَرۡفُودُ

Iwo adatsatizidwa ndi tembelero pano pa dziko lapansi ndipo pa tsiku la Qiyâma (adzatsatizidwanso). Taonani kuipa mphoto (yawo) yopatsidwa! info
التفاسير:

external-link copy
100 : 11

ذَٰلِكَ مِنۡ أَنۢبَآءِ ٱلۡقُرَىٰ نَقُصُّهُۥ عَلَيۡكَۖ مِنۡهَا قَآئِمٞ وَحَصِيدٞ

Izi ndi zina mwa nkhani za m’mizinda (zomwe) tikukusimbira. Ina mwa iyo ikadalipobe, ndipo ina idatha. info
التفاسير:

external-link copy
101 : 11

وَمَا ظَلَمۡنَٰهُمۡ وَلَٰكِن ظَلَمُوٓاْ أَنفُسَهُمۡۖ فَمَآ أَغۡنَتۡ عَنۡهُمۡ ءَالِهَتُهُمُ ٱلَّتِي يَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ مِن شَيۡءٖ لَّمَّا جَآءَ أَمۡرُ رَبِّكَۖ وَمَا زَادُوهُمۡ غَيۡرَ تَتۡبِيبٖ

Ndipo sitidawachitire choipa (powaononga). Koma adadzichitira okha zoipa (pakusakhulupirira Allah ndi kupembedza mafano ndikuipitsa pa dziko), milungu yawo yomwe ankaipembedza kusiya Allah siidawathandize chilichonse pamene lidadza lamulo la Mbuye wako (la kuwaononga). Ndipo (milunguyo) siidawaonjezere (china chake) koma chionongeko basi. info
التفاسير:

external-link copy
102 : 11

وَكَذَٰلِكَ أَخۡذُ رَبِّكَ إِذَآ أَخَذَ ٱلۡقُرَىٰ وَهِيَ ظَٰلِمَةٌۚ إِنَّ أَخۡذَهُۥٓ أَلِيمٞ شَدِيدٌ

Ndipo mmenemo ndi momwe kumakhalira kulanga kwa Mbuye wako pamene alanga anthu a m’mizinda akakhala oipa (pa makhalidwe). Ndithu kulanga kwake (Allah) nkowawa, nkwaukali. info
التفاسير:

external-link copy
103 : 11

إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗ لِّمَنۡ خَافَ عَذَابَ ٱلۡأٓخِرَةِۚ ذَٰلِكَ يَوۡمٞ مَّجۡمُوعٞ لَّهُ ٱلنَّاسُ وَذَٰلِكَ يَوۡمٞ مَّشۡهُودٞ

Ndithu m’zimenezi muli lingaliro kwa yemwe akuopa chilango cha tsiku lachimaliziro. Limenelo ndi tsiku losonkhanitsidwa anthu. Ndipo limenelo ndi tsiku lochitiridwa umboni (ndi zolengedwa zonse). info
التفاسير:

external-link copy
104 : 11

وَمَا نُؤَخِّرُهُۥٓ إِلَّا لِأَجَلٖ مَّعۡدُودٖ

Ndipo sitikulichedwetsa koma m’nthawi yowerengeka (kwa Allah, ngakhale kuti kwa anthu likuoneka kuti lili kutali.) info
التفاسير:

external-link copy
105 : 11

يَوۡمَ يَأۡتِ لَا تَكَلَّمُ نَفۡسٌ إِلَّا بِإِذۡنِهِۦۚ فَمِنۡهُمۡ شَقِيّٞ وَسَعِيدٞ

Tsiku lakudza (zoopsa zake), sadzayankhula aliyense koma mwachilolezo Chake (Allah). Ena adzakhala oipa, ndipo (ena) adzakhala abwino. info
التفاسير:

external-link copy
106 : 11

فَأَمَّا ٱلَّذِينَ شَقُواْ فَفِي ٱلنَّارِ لَهُمۡ فِيهَا زَفِيرٞ وَشَهِيقٌ

Tsono amene adzakhala oipa kobwerera kwawo nkumoto. Iwo adzakhala m’menemo akufuula potulutsa mawu ndi kuwabweza (monga kulira kwa bulu). info
التفاسير:

external-link copy
107 : 11

خَٰلِدِينَ فِيهَا مَا دَامَتِ ٱلسَّمَٰوَٰتُ وَٱلۡأَرۡضُ إِلَّا مَا شَآءَ رَبُّكَۚ إِنَّ رَبَّكَ فَعَّالٞ لِّمَا يُرِيدُ

Adzakhala m’menemo nthawi yaitali momwe thambo ndi nthaka zidzakhalire, kupatula Mbuye wako akadzafuna. Ndithu Mbuye wako Ngochita chimene wafuna. info
التفاسير:

external-link copy
108 : 11

۞ وَأَمَّا ٱلَّذِينَ سُعِدُواْ فَفِي ٱلۡجَنَّةِ خَٰلِدِينَ فِيهَا مَا دَامَتِ ٱلسَّمَٰوَٰتُ وَٱلۡأَرۡضُ إِلَّا مَا شَآءَ رَبُّكَۖ عَطَآءً غَيۡرَ مَجۡذُوذٖ

Tsono amene adzakhale abwino adzakhala m’Munda wamtendere. Adzakhala mmenemo nthawi yaitali momwe thambo ndi nthaka zidzakhalire, kupatula Mbuye wako akadzafuna; zopatsa (za Mbuye wako ndizo zopatsa) zosatha. info
التفاسير: