Firo maanaaji al-quraan tedduɗo oo - Eggo e ɗemngal Ciiciiwa - Kaalid Ibrahiima Biitala.

Tonngoode hello ngoo:close

external-link copy
160 : 7

وَقَطَّعۡنَٰهُمُ ٱثۡنَتَيۡ عَشۡرَةَ أَسۡبَاطًا أُمَمٗاۚ وَأَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰ مُوسَىٰٓ إِذِ ٱسۡتَسۡقَىٰهُ قَوۡمُهُۥٓ أَنِ ٱضۡرِب بِّعَصَاكَ ٱلۡحَجَرَۖ فَٱنۢبَجَسَتۡ مِنۡهُ ٱثۡنَتَا عَشۡرَةَ عَيۡنٗاۖ قَدۡ عَلِمَ كُلُّ أُنَاسٖ مَّشۡرَبَهُمۡۚ وَظَلَّلۡنَا عَلَيۡهِمُ ٱلۡغَمَٰمَ وَأَنزَلۡنَا عَلَيۡهِمُ ٱلۡمَنَّ وَٱلسَّلۡوَىٰۖ كُلُواْ مِن طَيِّبَٰتِ مَا رَزَقۡنَٰكُمۡۚ وَمَا ظَلَمُونَا وَلَٰكِن كَانُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ يَظۡلِمُونَ

Ndipo tidawagawa iwo m’mafuko khumi ndi awiri (osiyanasiyana) monga mitundu ikuluikulu. Ndipo tidamuvumbulutsira Mûsa pamene anthu ake adampempha madzi, kuti: “Menya mwala ndi ndodo yakoyo.” Ndipo mudatuluka akasupe khumi ndi awiri mwakuti fuko lililonse lidadziwa malo ake omwera. Ndipo tidawaphimba ndi mthunzi wa mtambo, ndi kuwatumizira mana ndi salwa (mbalame). (Tidawauza): “Idyani zinthu zabwinozi zomwe takupatsani.” Komatu sadatichitire choipa (pamene adachita zamphulupulu), koma adadzichitira okha zoipa. info
التفاسير:

external-link copy
161 : 7

وَإِذۡ قِيلَ لَهُمُ ٱسۡكُنُواْ هَٰذِهِ ٱلۡقَرۡيَةَ وَكُلُواْ مِنۡهَا حَيۡثُ شِئۡتُمۡ وَقُولُواْ حِطَّةٞ وَٱدۡخُلُواْ ٱلۡبَابَ سُجَّدٗا نَّغۡفِرۡ لَكُمۡ خَطِيٓـَٰٔتِكُمۡۚ سَنَزِيدُ ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Ndipo pamene adauzidwa: “Khalani mu Mzinda uwu (Yerusalemu), ndipo idyani m’menemo paliponse pamene mwafuna, ndipo nenani (polowa mu mzindamo uku mutawerama): “Tifafanizireni machimo athu, (E Inu Mbuye wathu)!” Ndipo lowerani pa chipata (chake) modzichepetsa; tikukhululukirani zolakwa zanu ndipo tiwaonjezera zabwino ochita zabwino. info
التفاسير:

external-link copy
162 : 7

فَبَدَّلَ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ مِنۡهُمۡ قَوۡلًا غَيۡرَ ٱلَّذِي قِيلَ لَهُمۡ فَأَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمۡ رِجۡزٗا مِّنَ ٱلسَّمَآءِ بِمَا كَانُواْ يَظۡلِمُونَ

Koma aja amene adadzichitira okha zoipa, mwa iwo adasintha mawu ena kusiya omwe adauzidwa; choncho, tidawatumizira chilango chochokera kumwamba chifukwa chodzichitira okha zoipa. info
التفاسير:

external-link copy
163 : 7

وَسۡـَٔلۡهُمۡ عَنِ ٱلۡقَرۡيَةِ ٱلَّتِي كَانَتۡ حَاضِرَةَ ٱلۡبَحۡرِ إِذۡ يَعۡدُونَ فِي ٱلسَّبۡتِ إِذۡ تَأۡتِيهِمۡ حِيتَانُهُمۡ يَوۡمَ سَبۡتِهِمۡ شُرَّعٗا وَيَوۡمَ لَا يَسۡبِتُونَ لَا تَأۡتِيهِمۡۚ كَذَٰلِكَ نَبۡلُوهُم بِمَا كَانُواْ يَفۡسُقُونَ

Tawafunsani nkhani ya mudzi umene udali m’mphepete mwa nyanja; (anthu am’mudziwo) pamene adali kuswa (lamulo la) tsiku la Sabata (lomwe adauzidwa kuti pa tsikuli asamachite usodzi wa nsomba, koma m’malo mwake azichita mapemphero okha). Nsomba zawo zinkawadzera yandayanda patsiku la Sabata, koma patsiku lomwe silidali la Sabata sizidali kuwabwerera (yandayanda). Motero tidawayesa mayeso chifukwa chakuchimwa kwawo. info
التفاسير: