Firo maanaaji al-quraan tedduɗo oo - Eggo e ɗemngal Ciiciiwa - Kaalid Ibrahiima Biitala.

Tonngoode hello ngoo:close

external-link copy
96 : 7

وَلَوۡ أَنَّ أَهۡلَ ٱلۡقُرَىٰٓ ءَامَنُواْ وَٱتَّقَوۡاْ لَفَتَحۡنَا عَلَيۡهِم بَرَكَٰتٖ مِّنَ ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِ وَلَٰكِن كَذَّبُواْ فَأَخَذۡنَٰهُم بِمَا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ

Chikhala kuti eni midziwo adakhulupirira naopa (Allah pamene aneneri adawadzera), tikadawatsekulira madalitso ochokera kumwamba ndi pansi. Koma adatsutsa (aneneri) ndipo tidawaononga chifukwa cha zoipa zomwe ankachita.[188] info

[188] Apa tanthauzo lake nkuti akanapeza mtendere wambiri pompano padziko lapansi akadakhala kuti adali olungama.

التفاسير:

external-link copy
97 : 7

أَفَأَمِنَ أَهۡلُ ٱلۡقُرَىٰٓ أَن يَأۡتِيَهُم بَأۡسُنَا بَيَٰتٗا وَهُمۡ نَآئِمُونَ

Kodi anthu a m’mizinda (iyo momwe muli anthu oipa) ali ndi chitetezo cholimba kuti chilango chathu sichingawadzere usiku iwo ali mtulo? info
التفاسير:

external-link copy
98 : 7

أَوَأَمِنَ أَهۡلُ ٱلۡقُرَىٰٓ أَن يَأۡتِيَهُم بَأۡسُنَا ضُحٗى وَهُمۡ يَلۡعَبُونَ

Kapena anthu a m’mizindayo ali ndi chitetezo cholimba kuti chilango Chathu sichingawafike masana uku iwo akusewera? info
التفاسير:

external-link copy
99 : 7

أَفَأَمِنُواْ مَكۡرَ ٱللَّهِۚ فَلَا يَأۡمَنُ مَكۡرَ ٱللَّهِ إِلَّا ٱلۡقَوۡمُ ٱلۡخَٰسِرُونَ

Kodi akudziika pa chitetezo ku chilango cha Allah? Sangadziike pa chitetezo ku chilango cha Allah kupatula anthu otayika basi. info
التفاسير:

external-link copy
100 : 7

أَوَلَمۡ يَهۡدِ لِلَّذِينَ يَرِثُونَ ٱلۡأَرۡضَ مِنۢ بَعۡدِ أَهۡلِهَآ أَن لَّوۡ نَشَآءُ أَصَبۡنَٰهُم بِذُنُوبِهِمۡۚ وَنَطۡبَعُ عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ فَهُمۡ لَا يَسۡمَعُونَ

Kodi sadadziwe awa omwe alandira dziko molowa mmalo pambuyo pa eni dzikolo (anthu akale) kuti tikadafuna tikadawaika m’masautso chifukwa cha machimo awo ndi kuwadinda mitima yawo kotero iwo sakadamva (kanthu)? info
التفاسير:

external-link copy
101 : 7

تِلۡكَ ٱلۡقُرَىٰ نَقُصُّ عَلَيۡكَ مِنۡ أَنۢبَآئِهَاۚ وَلَقَدۡ جَآءَتۡهُمۡ رُسُلُهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ فَمَا كَانُواْ لِيُؤۡمِنُواْ بِمَا كَذَّبُواْ مِن قَبۡلُۚ كَذَٰلِكَ يَطۡبَعُ ٱللَّهُ عَلَىٰ قُلُوبِ ٱلۡكَٰفِرِينَ

Iyo ndi midzi (ikuluikulu) yomwe tikukusimbira iwe zina mwa nkhani zake. Ndithudi, adawadzera atumiki awo ndi zizindikiro (zoonekera poyera zosonyeza kuti iwo ndi atumiki a Allah). Koma sadali oti nkukhulupirira pa zomwe adazitsutsapo kale. Umo ndi mmene Allah amadindira ndi kuitseka mitima ya osakhulupirira (kotero kuti sangathandizike ndi malangizo a mtundu uliwonse). info
التفاسير:

external-link copy
102 : 7

وَمَا وَجَدۡنَا لِأَكۡثَرِهِم مِّنۡ عَهۡدٖۖ وَإِن وَجَدۡنَآ أَكۡثَرَهُمۡ لَفَٰسِقِينَ

Ndipo ambiri a iwo sitidawapeze akukwaniritsa lonjezo lililonse koma tidawapeza ambiri a iwo ali opandukira (chilamulo cha Allah). info
التفاسير:

external-link copy
103 : 7

ثُمَّ بَعَثۡنَا مِنۢ بَعۡدِهِم مُّوسَىٰ بِـَٔايَٰتِنَآ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَمَلَإِيْهِۦ فَظَلَمُواْ بِهَاۖ فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُفۡسِدِينَ

Kenako pambuyo pawo (aneneriwo) tidamtumiza Mûsa pamodzi ndi zizindikiro Zathu kwa Farawo ndi nduna zake, koma adazikana (zizindikirozo). Choncho taona momwe adalili mathero aoononga. info
التفاسير:

external-link copy
104 : 7

وَقَالَ مُوسَىٰ يَٰفِرۡعَوۡنُ إِنِّي رَسُولٞ مِّن رَّبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

Ndipo Mûsa adati: “E iwe Farawo! Ndithu ine ndine mthenga wochokera kwa Mbuye wa zolengedwa zonse.” info
التفاسير: