Firo maanaaji al-quraan tedduɗo oo - Eggo e ɗemngal Ciiciiwa - Kaalid Ibrahiima Biitala.

Tonngoode hello ngoo:close

external-link copy
105 : 7

حَقِيقٌ عَلَىٰٓ أَن لَّآ أَقُولَ عَلَى ٱللَّهِ إِلَّا ٱلۡحَقَّۚ قَدۡ جِئۡتُكُم بِبَيِّنَةٖ مِّن رَّبِّكُمۡ فَأَرۡسِلۡ مَعِيَ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ

“Ndikofunika kwa ine kuti ndisamnenere Allah chilichonse koma choonadi basi. Ndithu ndakudzerani ndi chizindikiro choonekera kuchokera kwa Mbuye wanu. Choncho, aleke ndinke nawo ana a Israyeli.” info
التفاسير:

external-link copy
106 : 7

قَالَ إِن كُنتَ جِئۡتَ بِـَٔايَةٖ فَأۡتِ بِهَآ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ

(Farawo) adati: “Ngati wadza ndi chizindikiro, bwera nacho (tichione), ngati iwe ulidi mmodzi wa onena zoona.” info
التفاسير:

external-link copy
107 : 7

فَأَلۡقَىٰ عَصَاهُ فَإِذَا هِيَ ثُعۡبَانٞ مُّبِينٞ

Choncho adaponya ndodo yake pansi. Mwadzidzidzi, idasanduka njoka yooneka. info
التفاسير:

external-link copy
108 : 7

وَنَزَعَ يَدَهُۥ فَإِذَا هِيَ بَيۡضَآءُ لِلنَّٰظِرِينَ

Ndipo adatulutsa dzanja lake pompo lidakhala loyera, lowala kwa oliona. info
التفاسير:

external-link copy
109 : 7

قَالَ ٱلۡمَلَأُ مِن قَوۡمِ فِرۡعَوۡنَ إِنَّ هَٰذَا لَسَٰحِرٌ عَلِيمٞ

Nduna za mwa anthu a Farawo zidati: “Ndithu uyu ndi wamatsenga wodziwa (kwambiri zamatsenga).” info
التفاسير:

external-link copy
110 : 7

يُرِيدُ أَن يُخۡرِجَكُم مِّنۡ أَرۡضِكُمۡۖ فَمَاذَا تَأۡمُرُونَ

“Akufuna kukusamutsani mdziko mwanu. Nanga mukulangiza zotani?” info
التفاسير:

external-link copy
111 : 7

قَالُوٓاْ أَرۡجِهۡ وَأَخَاهُ وَأَرۡسِلۡ فِي ٱلۡمَدَآئِنِ حَٰشِرِينَ

(Iwo) adati (kwa Farawo): “Muleke pang’ono iye ndi m’bale wakeyu (usawaphe); ndipo tumiza osonkhanitsa m’mizinda kuti akusonkhanitsire (amatsenga onse akuluakulu).” info
التفاسير:

external-link copy
112 : 7

يَأۡتُوكَ بِكُلِّ سَٰحِرٍ عَلِيمٖ

“Kuti akubweretsere wamatsenga aliyense wodziwa kwambiri.” info
التفاسير:

external-link copy
113 : 7

وَجَآءَ ٱلسَّحَرَةُ فِرۡعَوۡنَ قَالُوٓاْ إِنَّ لَنَا لَأَجۡرًا إِن كُنَّا نَحۡنُ ٱلۡغَٰلِبِينَ

Amatsenga adadza kwa Farawo; nati: “Kodi ife tipeza malipiro ngati titapambana?” info
التفاسير:

external-link copy
114 : 7

قَالَ نَعَمۡ وَإِنَّكُمۡ لَمِنَ ٱلۡمُقَرَّبِينَ

(Farawo) adati: “Inde, ndipo mudzakhala mwa oyandikitsidwa (mudzakhala nduna zanga).” info
التفاسير:

external-link copy
115 : 7

قَالُواْ يَٰمُوسَىٰٓ إِمَّآ أَن تُلۡقِيَ وَإِمَّآ أَن نَّكُونَ نَحۡنُ ٱلۡمُلۡقِينَ

(Amatsenga) adati: “E iwe Mûsa! Kodi uyamba kuponya ndiwe (matsenga ako pamaso pa anthu), kapena ife tikhale oyambilira kuponya?” info
التفاسير:

external-link copy
116 : 7

قَالَ أَلۡقُواْۖ فَلَمَّآ أَلۡقَوۡاْ سَحَرُوٓاْ أَعۡيُنَ ٱلنَّاسِ وَٱسۡتَرۡهَبُوهُمۡ وَجَآءُو بِسِحۡرٍ عَظِيمٖ

Mûsa adati: “Ponyani.” Choncho pamene adaponya adalodza maso a anthu ndikuwaopseza. Ndipo adadza ndi matsenga aakulu zedi. info
التفاسير:

external-link copy
117 : 7

۞ وَأَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰ مُوسَىٰٓ أَنۡ أَلۡقِ عَصَاكَۖ فَإِذَا هِيَ تَلۡقَفُ مَا يَأۡفِكُونَ

Ndipo tidamzindikiritsa Mûsa ndi chivumbulutso (kuti): “Ponya ndodo yako.” Pompo iyo idameza zamatsengazo. info
التفاسير:

external-link copy
118 : 7

فَوَقَعَ ٱلۡحَقُّ وَبَطَلَ مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ

Choncho, choonadi chidatsimikizika, ndipo zidapita pachabe zomwe ankachita. info
التفاسير:

external-link copy
119 : 7

فَغُلِبُواْ هُنَالِكَ وَٱنقَلَبُواْ صَٰغِرِينَ

Choncho adagonjetsedwa pamenepo, nakhala onyozeka. info
التفاسير:

external-link copy
120 : 7

وَأُلۡقِيَ ٱلسَّحَرَةُ سَٰجِدِينَ

Ndipo amatsenga adadzigwetsa uku akulambira (Allah). info
التفاسير: