[384] Tsiku lina Mneneri (s.a.w) atakhala ndi akuluakulu a Aquraishi. Adali kuwalalikira za chipembedzo mwachidwi, ndipo adali kuyembekezera kuti akavomereza Chisilamu iwo, ndiye kuti anthu owatsatira naonso avomereza. Chifukwa anthu ambiri sadalowe Chisilamu poopa atsogoleri awo. Pa nthawi imeneyi adatulukira wakhungu wina yemwe ankatchedwa Ibn Ummu Maktum. Sadadziwe kuti Mneneri (s.a.w) ali wotanganidwa. Adamukuwira: “E Iwe Mneneri wa Allah! Ndiphunzitse inenso zimene wakuphunzitsa Allah.” Ndipo ankangomubwerezera-bwerezera mawu amenewa. Mneneri (s.a.w) pakuti adali ndi chidwi ndi kulalikira akuluakulu aja, adamchitira tsinya wakhungu uja chifukwa chomuonongera ntchito yake; sadamumvere. Basi pamenepa Allah akumdzudzula Mneneri Wake pa zomwe adachita posiya kumumvera amene adamubwerera kudzafuna chiongoko.
[385] (Ndime 11-16) Apa Allah akumuletsa Mtumiki Wake kuti asachitenso zonga adachitazo ndi kumuuza kuti Qur’an ndi ulaliki chabe, amene afuna kulingalira za ulalikiwo, umuthandiza, ndipo amene safuna, kutaika ndi kwake. Ndiponso adamufotokozera kuti Qur’an idachokera m’mabuku olemekezeka; idachokera ku “Lauhil-Mahfudh” mabuku omwe ali m’manja mwa Angelo olemba, olemekezeka, ochita zabwino omwe ndi abwino kuposa Aquraishi.
[387] (Ndime 38-39) Tsiku limenelo anthu adzakhala kakhalidwe ka mitundu iwiri: amene adakhulupilira ndi kuchita ntchito zabwino nkhope zawo zidzawala ndi chimwemwe, ndipo amene adakanira ndikumachita zoipa, nkhope zawo zidzakhala zafumbi ndi zakuda monga momwe anenera ma Ayah 40 ndi 42.