ಪವಿತ್ರ ಕುರ್‌ಆನ್ ಅರ್ಥಾನುವಾದ - ಚೇವಾ ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ

‘Abasa

external-link copy
1 : 80

عَبَسَ وَتَوَلَّىٰٓ

Adachita tsinya (Mneneri) ndi kuyang’ana kumbali.[384] info

[384] Tsiku lina Mneneri (s.a.w) atakhala ndi akuluakulu a Aquraishi. Adali kuwalalikira za chipembedzo mwachidwi, ndipo adali kuyembekezera kuti akavomereza Chisilamu iwo, ndiye kuti anthu owatsatira naonso avomereza. Chifukwa anthu ambiri sadalowe Chisilamu poopa atsogoleri awo. Pa nthawi imeneyi adatulukira wakhungu wina yemwe ankatchedwa Ibn Ummu Maktum. Sadadziwe kuti Mneneri (s.a.w) ali wotanganidwa. Adamukuwira: “E Iwe Mneneri wa Allah! Ndiphunzitse inenso zimene wakuphunzitsa Allah.” Ndipo ankangomubwerezera-bwerezera mawu amenewa. Mneneri (s.a.w) pakuti adali ndi chidwi ndi kulalikira akuluakulu aja, adamchitira tsinya wakhungu uja chifukwa chomuonongera ntchito yake; sadamumvere. Basi pamenepa Allah akumdzudzula Mneneri Wake pa zomwe adachita posiya kumumvera amene adamubwerera kudzafuna chiongoko.

التفاسير:

external-link copy
2 : 80

أَن جَآءَهُ ٱلۡأَعۡمَىٰ

Chifukwa chakuti adamdzera wakhungu (kudzamfunsa zokhudzana ndi chipembedzo chake pamene iye adali kuyankhula ndi atsogoleri Achiquraishi). info
التفاسير:

external-link copy
3 : 80

وَمَا يُدۡرِيكَ لَعَلَّهُۥ يَزَّكَّىٰٓ

Nanga chingakudziwitse nchiyani kuti mwina iye angadziyeretse (pomvera ulaliki wako watsopano)? info
التفاسير:

external-link copy
4 : 80

أَوۡ يَذَّكَّرُ فَتَنفَعَهُ ٱلذِّكۡرَىٰٓ

Kapena akumbukira, ndipo kukumbukirako kumthandiza? info
التفاسير:

external-link copy
5 : 80

أَمَّا مَنِ ٱسۡتَغۡنَىٰ

Koma amene wadzikwaniritsa (ndi chuma chake ndi mphamvu zake), info
التفاسير:

external-link copy
6 : 80

فَأَنتَ لَهُۥ تَصَدَّىٰ

Ameneyo ndi yemwe ukumchitira chidwi. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 80

وَمَا عَلَيۡكَ أَلَّا يَزَّكَّىٰ

Palibe chilichonse pa iwe ngati sadziyeretsa. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 80

وَأَمَّا مَن جَآءَكَ يَسۡعَىٰ

Koma amene wakudzera uku akuthamanga (kufuna maphunziro ndi chiongoko), info
التفاسير:

external-link copy
9 : 80

وَهُوَ يَخۡشَىٰ

Ndipo iye akuopa (Allah mu mtima mwake). info
التفاسير:

external-link copy
10 : 80

فَأَنتَ عَنۡهُ تَلَهَّىٰ

Za iye, iwe sukusamala, (ukuyikira chidwi kwa wina). info
التفاسير:

external-link copy
11 : 80

كَلَّآ إِنَّهَا تَذۡكِرَةٞ

Sichoncho! Ndithudi iyi (Qur’an) ndi chikumbutso (chenjezo).[385] info

[385] (Ndime 11-16) Apa Allah akumuletsa Mtumiki Wake kuti asachitenso zonga adachitazo ndi kumuuza kuti Qur’an ndi ulaliki chabe, amene afuna kulingalira za ulalikiwo, umuthandiza, ndipo amene safuna, kutaika ndi kwake. Ndiponso adamufotokozera kuti Qur’an idachokera m’mabuku olemekezeka; idachokera ku “Lauhil-Mahfudh” mabuku omwe ali m’manja mwa Angelo olemba, olemekezeka, ochita zabwino omwe ndi abwino kuposa Aquraishi.

التفاسير:

external-link copy
12 : 80

فَمَن شَآءَ ذَكَرَهُۥ

Basi, amene wafuna alangizika (ndi Qur’an, ndipo amene sakufuna msiye). info
التفاسير:

external-link copy
13 : 80

فِي صُحُفٖ مُّكَرَّمَةٖ

(Malangizowa akuchokera) mmakalata olemekezeka (kwa Allah); info
التفاسير:

external-link copy
14 : 80

مَّرۡفُوعَةٖ مُّطَهَّرَةِۭ

Apamwamba ndiponso oyeretsedwa (kumbiri iliyonse yopunguka); info
التفاسير:

external-link copy
15 : 80

بِأَيۡدِي سَفَرَةٖ

Omwe ali m’manja mwa Alembi (Angelo). info
التفاسير:

external-link copy
16 : 80

كِرَامِۭ بَرَرَةٖ

Olemekezeka, omvera. info
التفاسير:

external-link copy
17 : 80

قُتِلَ ٱلۡإِنسَٰنُ مَآ أَكۡفَرَهُۥ

Waonongeka (watembeleredwa) munthu. Nkotani kusayamika kwake kotereku. info
التفاسير:

external-link copy
18 : 80

مِنۡ أَيِّ شَيۡءٍ خَلَقَهُۥ

Kuchokera mchinthu chanji chimene iye adamulenga. info
التفاسير:

external-link copy
19 : 80

مِن نُّطۡفَةٍ خَلَقَهُۥ فَقَدَّرَهُۥ

Kuchokera ku dontho lamadzi (onyozeka) adamulenga, namkonzeratu mkalengedwe kosiyanasiyana. info
التفاسير:

external-link copy
20 : 80

ثُمَّ ٱلسَّبِيلَ يَسَّرَهُۥ

Kenako adamfewetsera njira (yotulukira m’mimba mwa mai ake). info
التفاسير:

external-link copy
21 : 80

ثُمَّ أَمَاتَهُۥ فَأَقۡبَرَهُۥ

Ndipo amamchititsa kuti amwalire namukumbula m’manda, info
التفاسير:

external-link copy
22 : 80

ثُمَّ إِذَا شَآءَ أَنشَرَهُۥ

Kenako akadzafuna adzamuukitsa (pambuyo pa imfa). info
التفاسير:

external-link copy
23 : 80

كَلَّا لَمَّا يَقۡضِ مَآ أَمَرَهُۥ

Ayi ndithu (munthu) sanakwaniritsebe zimene adamulamula Mbuye wake (Allah chingakhale wakhala nthawi yaitali pa dziko lapansi). info
التفاسير:

external-link copy
24 : 80

فَلۡيَنظُرِ ٱلۡإِنسَٰنُ إِلَىٰ طَعَامِهِۦٓ

Alingalire munthu (mmene chilili) chakudya chake;[386] info

[386] Ngati munthu sakumbuka chilengedwe chake, ayang’ane chakudya chimene akudya momwe chimapezekera. Azindikira mphamvu za Allah.

التفاسير:

external-link copy
25 : 80

أَنَّا صَبَبۡنَا ٱلۡمَآءَ صَبّٗا

Ndithu Ife timagwetsa mvula yambiri (kuchokera ku mitambo). info
التفاسير:

external-link copy
26 : 80

ثُمَّ شَقَقۡنَا ٱلۡأَرۡضَ شَقّٗا

Kenako timaing’amba nthaka kuti mmera utuluke; info
التفاسير:

external-link copy
27 : 80

فَأَنۢبَتۡنَا فِيهَا حَبّٗا

Ndipo timameretsa m’menemo njere (ya chakudya cha anthu ndi zina zimene amasunga mnkhokwe), info
التفاسير:

external-link copy
28 : 80

وَعِنَبٗا وَقَضۡبٗا

Ndi mphesa ndi msipu. info
التفاسير:

external-link copy
29 : 80

وَزَيۡتُونٗا وَنَخۡلٗا

Ndi mzitona (wabwino) ndi (zipatso za) kanjedza, info
التفاسير:

external-link copy
30 : 80

وَحَدَآئِقَ غُلۡبٗا

Ndi minda yothothana nthambi za mitengo, info
التفاسير:

external-link copy
31 : 80

وَفَٰكِهَةٗ وَأَبّٗا

Ndi zipatso (zodyedwa ndi anthu) ndi msipu (wodyedwa ndi nyama); info
التفاسير:

external-link copy
32 : 80

مَّتَٰعٗا لَّكُمۡ وَلِأَنۡعَٰمِكُمۡ

(Tazimeretsa zimenezo kuti) zikondweretse inu ndi ziweto zanu. info
التفاسير:

external-link copy
33 : 80

فَإِذَا جَآءَتِ ٱلصَّآخَّةُ

Choncho likadzafika lipenga logonthetsa mkhutu (ndi kuumitsa makosi). info
التفاسير:

external-link copy
34 : 80

يَوۡمَ يَفِرُّ ٱلۡمَرۡءُ مِنۡ أَخِيهِ

Patsikuli munthu adzathawa m’bale wake, info
التفاسير:

external-link copy
35 : 80

وَأُمِّهِۦ وَأَبِيهِ

Mayi wake ndi bambo wake, info
التفاسير:

external-link copy
36 : 80

وَصَٰحِبَتِهِۦ وَبَنِيهِ

Mkazi wake ndi ana ake. info
التفاسير:

external-link copy
37 : 80

لِكُلِّ ٱمۡرِيٕٖ مِّنۡهُمۡ يَوۡمَئِذٖ شَأۡنٞ يُغۡنِيهِ

Munthu aliyense mwa iwo, tsiku limenelo adzakhala ndi zakezake zotangwanika nazo. (Sadzalabadira za anzake). info
التفاسير:

external-link copy
38 : 80

وُجُوهٞ يَوۡمَئِذٖ مُّسۡفِرَةٞ

Tsiku limenelo nkhope zina zidzakhala zowala;[387] info

[387] (Ndime 38-39) Tsiku limenelo anthu adzakhala kakhalidwe ka mitundu iwiri: amene adakhulupilira ndi kuchita ntchito zabwino nkhope zawo zidzawala ndi chimwemwe, ndipo amene adakanira ndikumachita zoipa, nkhope zawo zidzakhala zafumbi ndi zakuda monga momwe anenera ma Ayah 40 ndi 42.

التفاسير:

external-link copy
39 : 80

ضَاحِكَةٞ مُّسۡتَبۡشِرَةٞ

Zosekelera ndi zachimwemwe (chifukwa cha nkhani yabwino ya ku Munda wamtendere.) info
التفاسير:

external-link copy
40 : 80

وَوُجُوهٞ يَوۡمَئِذٍ عَلَيۡهَا غَبَرَةٞ

Ndipo nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zokutidwa ndi fumbi. info
التفاسير:

external-link copy
41 : 80

تَرۡهَقُهَا قَتَرَةٌ

Mdima udzazikuta. info
التفاسير:

external-link copy
42 : 80

أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡكَفَرَةُ ٱلۡفَجَرَةُ

Iwo ndi anthu osakhulupirira oipa (olakwira Allah). info
التفاسير: