Translation of the Meanings of the Noble Qur'an - Chewa translation - Khaled Ibrahim Batyala

Al-Balad

external-link copy
1 : 90

لَآ أُقۡسِمُ بِهَٰذَا ٱلۡبَلَدِ

Ndikulumbilira mzinda uwu (wa Makka). info
التفاسير:

external-link copy
2 : 90

وَأَنتَ حِلُّۢ بِهَٰذَا ٱلۡبَلَدِ

Ndipo iwe udzatsikira mu mzindawu mwa ufulu (ndi kuuonjezera ulemelero). info
التفاسير:

external-link copy
3 : 90

وَوَالِدٖ وَمَا وَلَدَ

Ndiponso ndikulumbilira chobereka ndi choberekedwa, (kudzera mwa iwo mtundu wa anthu udasungidwa). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 90

لَقَدۡ خَلَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ فِي كَبَدٍ

Ndithudi tamulenga munthu mmavuto (kuyambira chiyambi chake mpaka malekezero a moyo wake).[439] info

[439] Munthu ali ndi mavuto ambiri amene nyama zina zilibe: chakudya amachipeza movutikira, ndipo kudya kwa iye nkofunikira pa moyo wake, chovala amachipeza movutikira pomwe iye ndiwoyenera kuvala. Sangathe kupilira ndi kutentha kapena kuzizira. Sangathenso kudziteteza popanda chida. Ndipo pamwamba pa izi, Allah wamukakamiza zinthu zambiri ndi kumuletsanso zinthu zambiri. Ndipo chilichonse chimene iye achita chikulembedwa. Pa tsiku lachimaliziro adzawerengedwa chilichonse chimene adachichita; chachikulu kapena chaching’ono.

التفاسير:

external-link copy
5 : 90

أَيَحۡسَبُ أَن لَّن يَقۡدِرَ عَلَيۡهِ أَحَدٞ

Kodi (munthu wolengedwa ndi mavutoyu) akuganiza kuti palibe amene angamuthe? [440] info

[440] Tanthauzo lake apa nkuti munthu akuganiza kuti palibe aliyense amene angamuweruze pa zolakwa zake.

التفاسير:

external-link copy
6 : 90

يَقُولُ أَهۡلَكۡتُ مَالٗا لُّبَدًا

Akunena (monyadira kuti): “Ndaononga chuma chambiri (chifukwa choletsa Chisilamu kufala).”[441] info

[441] (Ndime 6-7) Mawu awa akunenedwa kwa okanira omwe adali kupereka chuma chawo pomenyana ndi Usilamu kapena kufuna kumupha Mneneri (s.a.w). Kenako adali kudzitama chifukwa chopereka chuma chambiri pa njirayo. Izi zikumukhudza aliyense amene akufuna kuti Chisilamu chionongeke. Ndipo iwo amaganiza kuti Allah sakudziwa za maganizo awo oipa.

التفاسير:

external-link copy
7 : 90

أَيَحۡسَبُ أَن لَّمۡ يَرَهُۥٓ أَحَدٌ

Kodi akuganiza kuti palibe akumuona? info
التفاسير:

external-link copy
8 : 90

أَلَمۡ نَجۡعَل لَّهُۥ عَيۡنَيۡنِ

Kodi sitidampangire maso awiri (amene akuyang’anira)? info
التفاسير:

external-link copy
9 : 90

وَلِسَانٗا وَشَفَتَيۡنِ

Ndilirime ndi milomo iwiri (zimene akulankhulira)? info
التفاسير:

external-link copy
10 : 90

وَهَدَيۡنَٰهُ ٱلنَّجۡدَيۡنِ

Ndipo tamlongosolera njira ziwiri: (yabwino ndi yoipa, ndipo tampatsa mphamvu yosankhira njira imene akufuna). info
التفاسير:

external-link copy
11 : 90

فَلَا ٱقۡتَحَمَ ٱلۡعَقَبَةَ

Kodi walikwera phiri lovutalo (lomwe lingakamfikitse ku Jannah)?[442] info

[442] Tanthauzo lake ndikuti bwanji munthu sathokoza chifundo chimenechi (chopatsidwa maso ndi pakamwa) pogwiritsa ntchito chuma chake pa zinthu zabwino zimene Allah wazitchula m’ma Ayah akubwerawa? Ndipo tanthauzo la “kukwera phiri lovuta’’ ndiko kupereka chuma panjira ya Allah chimene chili ndinthu chovuta kwa anthu ambiri ndipo chimafanana ndikukwera phiri losongoka.

التفاسير:

external-link copy
12 : 90

وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا ٱلۡعَقَبَةُ

Nanga nchiyani chakudziwitsa za kukwera phiri lovutalo? info
التفاسير:

external-link copy
13 : 90

فَكُّ رَقَبَةٍ

(Kutero ndiko) kupereka ufulu kwa kapolo, info
التفاسير:

external-link copy
14 : 90

أَوۡ إِطۡعَٰمٞ فِي يَوۡمٖ ذِي مَسۡغَبَةٖ

Kapena kuwadyetsa (osowa) pa tsiku la njala, info
التفاسير:

external-link copy
15 : 90

يَتِيمٗا ذَا مَقۡرَبَةٍ

Amasiye achibale, info
التفاسير:

external-link copy
16 : 90

أَوۡ مِسۡكِينٗا ذَا مَتۡرَبَةٖ

Kapena wosauka wa fumbi lokhalokha (chifukwa cha kuvutika kwambiri), info
التفاسير:

external-link copy
17 : 90

ثُمَّ كَانَ مِنَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَتَوَاصَوۡاْ بِٱلصَّبۡرِ وَتَوَاصَوۡاْ بِٱلۡمَرۡحَمَةِ

Komanso nakhala mmodzi mwa okhulupirira ndikumalangizana za kupirira, ndi kumalangizananso za chifundo. info
التفاسير:

external-link copy
18 : 90

أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡمَيۡمَنَةِ

Otero ndiwo (anthu abwino) a ku dzanja lamanja. info
التفاسير:

external-link copy
19 : 90

وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِـَٔايَٰتِنَا هُمۡ أَصۡحَٰبُ ٱلۡمَشۡـَٔمَةِ

Koma amene sanakhulupirire Ayah Zathu, ndi anthu a kudzanja lamanzere (oipa). info
التفاسير:

external-link copy
20 : 90

عَلَيۡهِمۡ نَارٞ مُّؤۡصَدَةُۢ

Moto wozungulira mbali zonse udzakhala pa iwo (ndikuwatsekera makomo). info
التفاسير: