[439] Munthu ali ndi mavuto ambiri amene nyama zina zilibe: chakudya amachipeza movutikira, ndipo kudya kwa iye nkofunikira pa moyo wake, chovala amachipeza movutikira pomwe iye ndiwoyenera kuvala. Sangathe kupilira ndi kutentha kapena kuzizira. Sangathenso kudziteteza popanda chida. Ndipo pamwamba pa izi, Allah wamukakamiza zinthu zambiri ndi kumuletsanso zinthu zambiri. Ndipo chilichonse chimene iye achita chikulembedwa. Pa tsiku lachimaliziro adzawerengedwa chilichonse chimene adachichita; chachikulu kapena chaching’ono.
[441] (Ndime 6-7) Mawu awa akunenedwa kwa okanira omwe adali kupereka chuma chawo pomenyana ndi Usilamu kapena kufuna kumupha Mneneri (s.a.w). Kenako adali kudzitama chifukwa chopereka chuma chambiri pa njirayo. Izi zikumukhudza aliyense amene akufuna kuti Chisilamu chionongeke. Ndipo iwo amaganiza kuti Allah sakudziwa za maganizo awo oipa.
[442] Tanthauzo lake ndikuti bwanji munthu sathokoza chifundo chimenechi (chopatsidwa maso ndi pakamwa) pogwiritsa ntchito chuma chake pa zinthu zabwino zimene Allah wazitchula m’ma Ayah akubwerawa? Ndipo tanthauzo la “kukwera phiri lovuta’’ ndiko kupereka chuma panjira ya Allah chimene chili ndinthu chovuta kwa anthu ambiri ndipo chimafanana ndikukwera phiri losongoka.