Translation of the Meanings of the Noble Qur'an - Chewa translation - Khaled Ibrahim Batyala

Page Number:close

external-link copy
45 : 27

وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَآ إِلَىٰ ثَمُودَ أَخَاهُمۡ صَٰلِحًا أَنِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ فَإِذَا هُمۡ فَرِيقَانِ يَخۡتَصِمُونَ

Ndipo ndithu Asamudu tidawatumizira m’bale wawo Swalih kuti awauze: “Mpembedzeni Allah.” Choncho adali magulu awiri omwe amakangana. (Ena adam’tsata pomwe ena adam’kana). info
التفاسير:

external-link copy
46 : 27

قَالَ يَٰقَوۡمِ لِمَ تَسۡتَعۡجِلُونَ بِٱلسَّيِّئَةِ قَبۡلَ ٱلۡحَسَنَةِۖ لَوۡلَا تَسۡتَغۡفِرُونَ ٱللَّهَ لَعَلَّكُمۡ تُرۡحَمُونَ

(Swaleh) adati: “E inu anthu anga chifukwa ninji inu mukufulumizitsa choipa (kuti chidze) musanachite chabwino? Bwanji simukupempha chikhululuko kwa Allah kuti muchitiridwe chifundo?” info
التفاسير:

external-link copy
47 : 27

قَالُواْ ٱطَّيَّرۡنَا بِكَ وَبِمَن مَّعَكَۚ قَالَ طَٰٓئِرُكُمۡ عِندَ ٱللَّهِۖ بَلۡ أَنتُمۡ قَوۡمٞ تُفۡتَنُونَ

(Iwo) adati: “Tapeza masoka oipa chifukwa cha iwe ndi omwe uli nawo.” (Iye) adati: “Tsoka lanu lili kwa Allah (chifukwa cha zolakwa zanu); koma inu ndinu anthu amene mukuyesedwa (ndi Allah kuti aone ngati mutsatire Mtumiki Wake kapena simutsatira).” info
التفاسير:

external-link copy
48 : 27

وَكَانَ فِي ٱلۡمَدِينَةِ تِسۡعَةُ رَهۡطٖ يُفۡسِدُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَا يُصۡلِحُونَ

Ndipo m’mudzimo adalipo anthu asanu ndi anayi omwe amaononga pa dziko, ndipo samakonza (chilichonse koma kuchiononga). info
التفاسير:

external-link copy
49 : 27

قَالُواْ تَقَاسَمُواْ بِٱللَّهِ لَنُبَيِّتَنَّهُۥ وَأَهۡلَهُۥ ثُمَّ لَنَقُولَنَّ لِوَلِيِّهِۦ مَا شَهِدۡنَا مَهۡلِكَ أَهۡلِهِۦ وَإِنَّا لَصَٰدِقُونَ

(Iwo) adati: “Aliyense wa ife alumbire kwa Allah (kuti) iye (Swaleh) ndi banja lake timthira nkhondo usiku, ndipo kenako Timuuza mlowam’malo wake (kuti): “Sitidaone kuonongeka kwa m’bale wake; ndithu ife tikunena zoona.” info
التفاسير:

external-link copy
50 : 27

وَمَكَرُواْ مَكۡرٗا وَمَكَرۡنَا مَكۡرٗا وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ

Ndipo adakonza chiwembu ndi kutchera misampha yamphamvu, nafenso tidawatchera misampha yowaononga, iwo asakudziwa. info
التفاسير:

external-link copy
51 : 27

فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ مَكۡرِهِمۡ أَنَّا دَمَّرۡنَٰهُمۡ وَقَوۡمَهُمۡ أَجۡمَعِينَ

Tsono tayang’ana, kodi malekezero a chiwembu chawo adali otani! Tidawaononga iwo ndi anthu awo onse. info
التفاسير:

external-link copy
52 : 27

فَتِلۡكَ بُيُوتُهُمۡ خَاوِيَةَۢ بِمَا ظَلَمُوٓاْۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗ لِّقَوۡمٖ يَعۡلَمُونَ

Izo ndinyumba zawo (zomwe zasanduka) mabwinja chifukwa cha chinyengo chawo. Ndithu m’zimenezo muli phunziro kwa odziwa. info
التفاسير:

external-link copy
53 : 27

وَأَنجَيۡنَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَكَانُواْ يَتَّقُونَ

Ndipo tidawapulumutsa amene adakhulupirira pakuti amamuopa (Allah). info
التفاسير:

external-link copy
54 : 27

وَلُوطًا إِذۡ قَالَ لِقَوۡمِهِۦٓ أَتَأۡتُونَ ٱلۡفَٰحِشَةَ وَأَنتُمۡ تُبۡصِرُونَ

Ndipo (akumbutse nkhani ya) Luti pamene adanena kwa anthu ake: “Kodi mukuchita zadama uku inu mukuziona?” info
التفاسير:

external-link copy
55 : 27

أَئِنَّكُمۡ لَتَأۡتُونَ ٱلرِّجَالَ شَهۡوَةٗ مِّن دُونِ ٱلنِّسَآءِۚ بَلۡ أَنتُمۡ قَوۡمٞ تَجۡهَلُونَ

“Kodi inu mukugona ndi amuna pokwaniritsa chilakolako (cha chilengedwe) kusiya akazi? koma inu ndinu mbuli.” info
التفاسير: