Translation of the Meanings of the Noble Qur'an - Chewa translation - Khaled Ibrahim Batyala

An-Naml

external-link copy
1 : 27

طسٓۚ تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱلۡقُرۡءَانِ وَكِتَابٖ مُّبِينٍ

Tâ-Sîn. Izi ndi Ayah (ndime) (za Qur’an buku lodzazidwa ndi zothandiza), ndiponso buku lofotokoza (chilichonse chauzimu ndi chamoyo wadziko). info
التفاسير:

external-link copy
2 : 27

هُدٗى وَبُشۡرَىٰ لِلۡمُؤۡمِنِينَ

(Qur’an) nchiongoko ndi nkhani yabwino kwa okhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 27

ٱلَّذِينَ يُقِيمُونَ ٱلصَّلَوٰةَ وَيُؤۡتُونَ ٱلزَّكَوٰةَ وَهُم بِٱلۡأٓخِرَةِ هُمۡ يُوقِنُونَ

Amene akupemphera Swala (zisanu, modzichepetsa ndi mokwaniritsa malamulo ake) ndi kumapereka Zakaat (m’nthawi yake), ndipo iwo ali ndi chitsimikizo champhamvu cha (moyo wa) tsiku la chimaliziro. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 27

إِنَّ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ زَيَّنَّا لَهُمۡ أَعۡمَٰلَهُمۡ فَهُمۡ يَعۡمَهُونَ

Ndithu amene sakhulupirira za (moyo wa) tsiku la chimaliziro, tawakometsera zochita zoipa kukhala ngati zabwino; choncho iwo akungoyumbayumba (m’kusokera kwawo). info
التفاسير:

external-link copy
5 : 27

أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ لَهُمۡ سُوٓءُ ٱلۡعَذَابِ وَهُمۡ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ هُمُ ٱلۡأَخۡسَرُونَ

Iwowo ndiamene adzapeza chilango choipa; iwo tsiku lachimaliziro ngotayika zedi, (adzaonongeka ku Moto motheratu). info
التفاسير:

external-link copy
6 : 27

وَإِنَّكَ لَتُلَقَّى ٱلۡقُرۡءَانَ مِن لَّدُنۡ حَكِيمٍ عَلِيمٍ

Ndipo ndithu iwe ukuphunzitsidwa Qur’an kuchokera kwa mwini nzeru zakuya, Wodziwa kwambiri. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 27

إِذۡ قَالَ مُوسَىٰ لِأَهۡلِهِۦٓ إِنِّيٓ ءَانَسۡتُ نَارٗا سَـَٔاتِيكُم مِّنۡهَا بِخَبَرٍ أَوۡ ءَاتِيكُم بِشِهَابٖ قَبَسٖ لَّعَلَّكُمۡ تَصۡطَلُونَ

(Kumbuka) Mûsa pamene adauza banja lake (mkazi wake): “Ndithu ine ndaona moto; posachedwapa ndikubweretserani nkhani za kumeneko, kapena ndikubweretserani chikuni cha moto kuti inu muothe. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 27

فَلَمَّا جَآءَهَا نُودِيَ أَنۢ بُورِكَ مَن فِي ٱلنَّارِ وَمَنۡ حَوۡلَهَا وَسُبۡحَٰنَ ٱللَّهِ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

Choncho pamene adaudzera (motowo) kudaitanidwa: “Wadalitsidwa yemwe ali m’moto ndi yemwe ali m’mphepete mwake; ndipo walemekezeka Allah Mbuye wa zolengedwa. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 27

يَٰمُوسَىٰٓ إِنَّهُۥٓ أَنَا ٱللَّهُ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ

E iwe Mûsa! Ndithu ine ndine Allah, Wamphamvu zoposa; Wanzeru zakuya. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 27

وَأَلۡقِ عَصَاكَۚ فَلَمَّا رَءَاهَا تَهۡتَزُّ كَأَنَّهَا جَآنّٞ وَلَّىٰ مُدۡبِرٗا وَلَمۡ يُعَقِّبۡۚ يَٰمُوسَىٰ لَا تَخَفۡ إِنِّي لَا يَخَافُ لَدَيَّ ٱلۡمُرۡسَلُونَ

Ndipo ponya (pansi) ndodo yako! (Pamene adaiponya idasanduka njoka), tero pamene adaiwona ikugwedezeka (ndodo ija) ngati njoka, adatembenuka kuthawa, ndipo sadacheuke (kapena kudikira kuti amve mawu omvekawo): “E iwe Mûsa! Usaope. Ndithu Ine, saopa kwa Ine atumiki.” info
التفاسير:

external-link copy
11 : 27

إِلَّا مَن ظَلَمَ ثُمَّ بَدَّلَ حُسۡنَۢا بَعۡدَ سُوٓءٖ فَإِنِّي غَفُورٞ رَّحِيمٞ

“Koma amene wadzichitira yekha zoipa, kenako nkusintha (pochita) zabwino pambuyo pa zoipa, (ndimkhululukira) pakuti Ine ndine Wokhululuka kwabasi, Wachifundo chambiri.” info
التفاسير:

external-link copy
12 : 27

وَأَدۡخِلۡ يَدَكَ فِي جَيۡبِكَ تَخۡرُجۡ بَيۡضَآءَ مِنۡ غَيۡرِ سُوٓءٖۖ فِي تِسۡعِ ءَايَٰتٍ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَقَوۡمِهِۦٓۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَوۡمٗا فَٰسِقِينَ

“Ndipo lowetsa dzanja lako palisani la mkanjo wako, ndipo lituluka lili loyera, (kuyera) kopanda matenda. (Ziwirizi) zili m’gulu la zododometsa zisanu ndi zinayi. Pita nazo kwa Farawo ndi anthu ake; ndithu iwo ndianthu otuluka m’chilamulo cha Allah.” info
التفاسير:

external-link copy
13 : 27

فَلَمَّا جَآءَتۡهُمۡ ءَايَٰتُنَا مُبۡصِرَةٗ قَالُواْ هَٰذَا سِحۡرٞ مُّبِينٞ

Tero pamene zidawadzera zizindikiro Zathu zosonyeza (kuti iye ndimtumiki wa Allah) adati: “Awa ndimatsenga woonekera.” info
التفاسير: