Übersetzung der Bedeutungen von dem heiligen Quran - Die Übersetzung in Chichewa - Khalid Ibrahim Bityala.

Nummer der Seite:close

external-link copy
11 : 21

وَكَمۡ قَصَمۡنَا مِن قَرۡيَةٖ كَانَتۡ ظَالِمَةٗ وَأَنشَأۡنَا بَعۡدَهَا قَوۡمًا ءَاخَرِينَ

Ndi ambiri mwa eni midzi yomwe idali yosalungama, tidawaononga; ndipo pambuyo pake tidalenga anthu ena. info
التفاسير:

external-link copy
12 : 21

فَلَمَّآ أَحَسُّواْ بَأۡسَنَآ إِذَا هُم مِّنۡهَا يَرۡكُضُونَ

Pamene adazindikira za chilango chathu, pompo adayamba kuchithawa. info
التفاسير:

external-link copy
13 : 21

لَا تَرۡكُضُواْ وَٱرۡجِعُوٓاْ إِلَىٰ مَآ أُتۡرِفۡتُمۡ فِيهِ وَمَسَٰكِنِكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تُسۡـَٔلُونَ

Musathawe, (kuthawa sikukupulumutsani), koma bwererani ku zimene mwasangalatsidwa nazo ndi m’malo mwanu, kuti mufunsidwe. info
التفاسير:

external-link copy
14 : 21

قَالُواْ يَٰوَيۡلَنَآ إِنَّا كُنَّا ظَٰلِمِينَ

Adanena: “Tsoka lathu ndithu! Tidali ochita zoipa.” info
التفاسير:

external-link copy
15 : 21

فَمَا زَالَت تِّلۡكَ دَعۡوَىٰهُمۡ حَتَّىٰ جَعَلۡنَٰهُمۡ حَصِيدًا خَٰمِدِينَ

Kukuwa kwawoko sikudathe, kufikira tidawapanga ngati (mbewu) zokololedwa, mpaka kupuma kwawo kudazima (adafa). info
التفاسير:

external-link copy
16 : 21

وَمَا خَلَقۡنَا ٱلسَّمَآءَ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَا لَٰعِبِينَ

Ndipo sitidalenge thambo ndi nthaka ndi zapakati pake, mwamasewera. info
التفاسير:

external-link copy
17 : 21

لَوۡ أَرَدۡنَآ أَن نَّتَّخِذَ لَهۡوٗا لَّٱتَّخَذۡنَٰهُ مِن لَّدُنَّآ إِن كُنَّا فَٰعِلِينَ

Tikadafuna kupanga choti tiziseweretsa (sitidakapanga zomwe mukuzionazi) tikadapanga mwazomwe tili nazo, tikadakhala oti tichite (zachibwana). info
التفاسير:

external-link copy
18 : 21

بَلۡ نَقۡذِفُ بِٱلۡحَقِّ عَلَى ٱلۡبَٰطِلِ فَيَدۡمَغُهُۥ فَإِذَا هُوَ زَاهِقٞۚ وَلَكُمُ ٱلۡوَيۡلُ مِمَّا تَصِفُونَ

Koma (chimene timachita ndi ichi), timachiponya choona pa chachabe ndi kuchiswa bongo bwake, ndipo chachabecho chimachoka. Ndipo chilango chili pa inu chifukwa cha zomwe mukunena (kumnamizira Allah). info
التفاسير:

external-link copy
19 : 21

وَلَهُۥ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَمَنۡ عِندَهُۥ لَا يَسۡتَكۡبِرُونَ عَنۡ عِبَادَتِهِۦ وَلَا يَسۡتَحۡسِرُونَ

Onse akumwamba ndi pansi, Ngake (Allah); ndipo amene ali kwa Iye (angelo), sadzitukumula pakumulambira, ndiponso satopa (ndi mapemphero) info
التفاسير:

external-link copy
20 : 21

يُسَبِّحُونَ ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَ لَا يَفۡتُرُونَ

Amamlemekeza usiku ndi usana, ndipo sagwidwa ndi ulesi. info
التفاسير:

external-link copy
21 : 21

أَمِ ٱتَّخَذُوٓاْ ءَالِهَةٗ مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ هُمۡ يُنشِرُونَ

Kapena adzipangira milungu yochokera m’nthaka youkitsa akufa, (kotero kuti aichita kukhala milungu yawo mmalo mwa Allah)? info
التفاسير:

external-link copy
22 : 21

لَوۡ كَانَ فِيهِمَآ ءَالِهَةٌ إِلَّا ٱللَّهُ لَفَسَدَتَاۚ فَسُبۡحَٰنَ ٱللَّهِ رَبِّ ٱلۡعَرۡشِ عَمَّا يَصِفُونَ

Kukadakhala kuti ilipo m’menemo milungu ina (kuthambo ndi pansi) kupatula Allah, (ziwirizi) zikadawonongeka, wapatukana Allah Mbuye wa Arsh (Mpando Wachifumu) ndi zimene akunena (osakhulupirira). info
التفاسير:

external-link copy
23 : 21

لَا يُسۡـَٔلُ عَمَّا يَفۡعَلُ وَهُمۡ يُسۡـَٔلُونَ

Safunsidwa pa zimene akuchita, koma iwo adzafunsidwa. info
التفاسير:

external-link copy
24 : 21

أَمِ ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِهِۦٓ ءَالِهَةٗۖ قُلۡ هَاتُواْ بُرۡهَٰنَكُمۡۖ هَٰذَا ذِكۡرُ مَن مَّعِيَ وَذِكۡرُ مَن قَبۡلِيۚ بَلۡ أَكۡثَرُهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ ٱلۡحَقَّۖ فَهُم مُّعۡرِضُونَ

Kapena adzipangira milungu ina m’malo mwa Iye? Nena: ‘“Bweretsani umboni wanu (pa zimenezi), (izi ndikuuzani) ndichikumbutso kwa awa ali pamodzi ndi ine, ndiponso ndichikumbutso kwa amene adalipo patsogolo panga.” Koma ambiri a iwo sadziwa za choonadi, tero iwo akunyozera. info
التفاسير: