Übersetzung der Bedeutungen von dem heiligen Quran - Die Übersetzung in Chichewa - Khalid Ibrahim Bityala.

Al-Anbiyâ’

external-link copy
1 : 21

ٱقۡتَرَبَ لِلنَّاسِ حِسَابُهُمۡ وَهُمۡ فِي غَفۡلَةٖ مُّعۡرِضُونَ

۞ Chiwerengero chayandikira kwa anthu pomwe iwo ali m’kusalabadira ndi M’kunyozera. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 21

مَا يَأۡتِيهِم مِّن ذِكۡرٖ مِّن رَّبِّهِم مُّحۡدَثٍ إِلَّا ٱسۡتَمَعُوهُ وَهُمۡ يَلۡعَبُونَ

Palibe pamene ukuwadzera ulaliki watsopano wochokera kwa Mbuye wawo koma amaumvetsera uku akuchita zachibwana. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 21

لَاهِيَةٗ قُلُوبُهُمۡۗ وَأَسَرُّواْ ٱلنَّجۡوَى ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ هَلۡ هَٰذَآ إِلَّا بَشَرٞ مِّثۡلُكُمۡۖ أَفَتَأۡتُونَ ٱلسِّحۡرَ وَأَنتُمۡ تُبۡصِرُونَ

Mitima yawo ikunyozera (osalabadira za kudza kwa Qiyâma). Ndipo akunenezana mobisa amene adzichitira zoipa; (akuuzana motere): “Kodi uyu (Muhammadiyu) ndi ndani, simunthu monga inu? Kodi mukuudzera ufiti pomwe mukuuona?” info
التفاسير:

external-link copy
4 : 21

قَالَ رَبِّي يَعۡلَمُ ٱلۡقَوۡلَ فِي ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِۖ وَهُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ

(Mneneri Muhammad{s.a.w}) adati: “Mbuye wanga akudziwa zimene zikunenedwa kumwamba ndi pansi; ndipo Iye Ngwakumva; Ngodziwa. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 21

بَلۡ قَالُوٓاْ أَضۡغَٰثُ أَحۡلَٰمِۭ بَلِ ٱفۡتَرَىٰهُ بَلۡ هُوَ شَاعِرٞ فَلۡيَأۡتِنَا بِـَٔايَةٖ كَمَآ أُرۡسِلَ ٱلۡأَوَّلُونَ

Koma (osakhulupirira) adati: “(Izi zimene akufotokozazi) ndi maloto opanda pake.” (Ndipo nthawi zina amati:) “Koma zimenezi wazipeka.” (Penanso amati:) “Koma iyeyu ndi mlakatuli. Chonchotu, atibweretsere chizizwa monga mmene adatumiziridwa (aneneri) oyamba.” info
التفاسير:

external-link copy
6 : 21

مَآ ءَامَنَتۡ قَبۡلَهُم مِّن قَرۡيَةٍ أَهۡلَكۡنَٰهَآۖ أَفَهُمۡ يُؤۡمِنُونَ

Sadakhulupirire apatsogolo pawo, eni midzi imene tidaiononga (ngakhale kuti zozizwitsa adaziona); nanga iwo akhulupirira? info
التفاسير:

external-link copy
7 : 21

وَمَآ أَرۡسَلۡنَا قَبۡلَكَ إِلَّا رِجَالٗا نُّوحِيٓ إِلَيۡهِمۡۖ فَسۡـَٔلُوٓاْ أَهۡلَ ٱلذِّكۡرِ إِن كُنتُمۡ لَا تَعۡلَمُونَ

Ndipo sitidawatume patsogolo pako, (iwe Mtumiki,) koma anthu, (osati angelo); tidawavumbulutsira (chivumbulutso Chathu.) Choncho, afunseni eni kudziwa ngati inu simukudziwa (nkhani zakale). info
التفاسير:

external-link copy
8 : 21

وَمَا جَعَلۡنَٰهُمۡ جَسَدٗا لَّا يَأۡكُلُونَ ٱلطَّعَامَ وَمَا كَانُواْ خَٰلِدِينَ

Ndipo sitidawachite (aneneriwo) kukhala matupi osadya chakudya ndipo sadalinso okhala nthawi yaitali. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 21

ثُمَّ صَدَقۡنَٰهُمُ ٱلۡوَعۡدَ فَأَنجَيۡنَٰهُمۡ وَمَن نَّشَآءُ وَأَهۡلَكۡنَا ٱلۡمُسۡرِفِينَ

Kenako tidawatsimikizira lonjezo (la kuwathangata pa adani awo), ndipo tidawapulumutsa iwo ndi amene tidawafuna (mwa omwe adawatsata), ndipo olumpha malire (a Allah) Tidawaononga. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 21

لَقَدۡ أَنزَلۡنَآ إِلَيۡكُمۡ كِتَٰبٗا فِيهِ ذِكۡرُكُمۡۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ

Ndithu tatumiza kwa inu buku lomwe m’kati mwake muli ulaliki wanu (malangizo kwa inu). Kodi simukuzindikira? info
التفاسير: