[430] Tanthauzo la Ayah iyi ndi masiku khumi olemekezeka omwe ali mkhumi loyamba la mwezi wa Thul-Hijjah umene ndi mwezi wa 12 pa kalendala ya Chisilamu. Amenewa ndi masiku olemekezeka kuposa masiku onse ngakhale masiku a Ramadan kupatula usiku wa LAILA-TUL-QADR, ndi masiku khumi omaliza a mwezi wa Ramadan. Choncho ndi bwino kuchulukitsa mapemphero m’masiku amenewa.
[431] Shafi ndi nambala yotheka kugawa ndi 2 (even number) Witri ndi nambala yosatheka kuigawa ndi 2 (odd number). Cholinga cha Allah pamenepa ndi kuzilumbilira zinthu zonse zimene adazilenga, zowerengedwa mnjira zonse ziwiri.
[432] (Ndime 7-9) Âdi aku Irama ndi mtundu wa Mneneri Hud. Adali akuluakulu matupi a mphamvu kwambiri mwakuti ankanena kuti: “Ndani wamphamvu kuposa ife!” Thamudu (Samudu) ndi mtundu wa Mneneri Swaleh. Iwowa adali kukhala ku mpoto kwa chilumba cha Arabia.