Qurani Kərimin mənaca tərcüməsi - Şişyo dilinə tərcümə - Xalid İbrahim Bəytələ.

Al-Infitâr

external-link copy
1 : 82

إِذَا ٱلسَّمَآءُ ٱنفَطَرَتۡ

Pamene thambo lidzasweke,[397] info

[397] Kuyambira pa Ayah 1 mpaka 4, Allah akutisonyeza zododometsa zina za tsiku lachimaliziro.

التفاسير:

external-link copy
2 : 82

وَإِذَا ٱلۡكَوَاكِبُ ٱنتَثَرَتۡ

Ndi pamene nyenyezi zidzayoyoke (ndi kumwazikana), info
التفاسير:

external-link copy
3 : 82

وَإِذَا ٱلۡبِحَارُ فُجِّرَتۡ

Pamenenso nyanja zikuluzikulu zidzaphwasulidwe. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 82

وَإِذَا ٱلۡقُبُورُ بُعۡثِرَتۡ

Ndiponso pamene manda adzafukulidwe (ndikutuluka akufa omwe adali mmenemo), info
التفاسير:

external-link copy
5 : 82

عَلِمَتۡ نَفۡسٞ مَّا قَدَّمَتۡ وَأَخَّرَتۡ

(Panthawiyo) mzimu uliwonse udzadziwa zimene udatsogoza (zabwino ndi zoipa) ndi zimene udasiya m’mbuyo.[398] info

[398] Munthu aliyense pa tsiku limenelo adzadziwa zimene adachita, zabwino ndi zoipa.

التفاسير:

external-link copy
6 : 82

يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡإِنسَٰنُ مَا غَرَّكَ بِرَبِّكَ ٱلۡكَرِيمِ

E iwe munthu! Nchiani chakunyenga kumsiya Mbuye wako wa ufulu (kufikira pomnyoza)? info
التفاسير:

external-link copy
7 : 82

ٱلَّذِي خَلَقَكَ فَسَوَّىٰكَ فَعَدَلَكَ

Amene adalenga iwe nakulinganiza (ziwalo zako) ndi kukulongosola (moyenera); info
التفاسير:

external-link copy
8 : 82

فِيٓ أَيِّ صُورَةٖ مَّا شَآءَ رَكَّبَكَ

Ndipo maonekedwe amtundu uliwonse omwe adawafuna adakuveka (popanda chifuniro chako). info
التفاسير:

external-link copy
9 : 82

كَلَّا بَلۡ تُكَذِّبُونَ بِٱلدِّينِ

Ayi, sichoncho! Koma inu mukutsutsa za (tsiku) lamalipiro. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 82

وَإِنَّ عَلَيۡكُمۡ لَحَٰفِظِينَ

Ndithu pa inu alipo okuyang’ anirani,[399] info

[399] Munthu aliyense ali nawo angelo awiri, Rakibu ndi Atidu. Ntchito zawo ndi kulemba ntchito za munthu, zabwino ndi zoipa zomwe.

التفاسير:

external-link copy
11 : 82

كِرَامٗا كَٰتِبِينَ

Olemekezeka, olemba (zochita zanu.) info
التفاسير:

external-link copy
12 : 82

يَعۡلَمُونَ مَا تَفۡعَلُونَ

Akudziwa (zonse) zimene mukuchita (zabwino ndi zoipa). info
التفاسير:

external-link copy
13 : 82

إِنَّ ٱلۡأَبۡرَارَ لَفِي نَعِيمٖ

Ndithudi ochita zabwino adzakhala mu mtendere. info
التفاسير:

external-link copy
14 : 82

وَإِنَّ ٱلۡفُجَّارَ لَفِي جَحِيمٖ

Ndipo ndithu amene ali olakwira malamulo a Allah adzakhala ku Moto wopsereza. info
التفاسير:

external-link copy
15 : 82

يَصۡلَوۡنَهَا يَوۡمَ ٱلدِّينِ

Adzaulowa tsiku la malipiro. info
التفاسير:

external-link copy
16 : 82

وَمَا هُمۡ عَنۡهَا بِغَآئِبِينَ

Ndipo iwo kumeneko sadzachokako. info
التفاسير:

external-link copy
17 : 82

وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا يَوۡمُ ٱلدِّينِ

Kodi nchiyani chingakudziwitse za tsiku la malipiro? info
التفاسير:

external-link copy
18 : 82

ثُمَّ مَآ أَدۡرَىٰكَ مَا يَوۡمُ ٱلدِّينِ

Ndipo nchiyani chingakudziwitse za tsiku lamalipiro? info
التفاسير:

external-link copy
19 : 82

يَوۡمَ لَا تَمۡلِكُ نَفۡسٞ لِّنَفۡسٖ شَيۡـٔٗاۖ وَٱلۡأَمۡرُ يَوۡمَئِذٖ لِّلَّهِ

Limeneli ndi tsiku limene mzimu uliwonse sudzakhala ndi mphamvu (yodzetsa mtendere kapena yochotsa chovuta) pa mzimu wina. Ndipo lamulo pa tsiku limeneli ndi la Allah yekha.[400] info

[400] Tanthauzo lake ndikuti tsiku limenelo sipadzakhala munthu wotha kumthandiza mnzake pa chilichonse ndiponso palibe adzakhale ndi mphamvu zolamula kupatula Allah yekha.

التفاسير: