Qurani Kərimin mənaca tərcüməsi - Şişyo dilinə tərcümə - Xalid İbrahim Bəytələ.

Al-Insân

external-link copy
1 : 76

هَلۡ أَتَىٰ عَلَى ٱلۡإِنسَٰنِ حِينٞ مِّنَ ٱلدَّهۡرِ لَمۡ يَكُن شَيۡـٔٗا مَّذۡكُورًا

Ndithu munthu idampita nthawi yaitali kwambiri (asanauziridwe mzimu) pomwe sadali chinthu chotchulidwa. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 76

إِنَّا خَلَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ مِن نُّطۡفَةٍ أَمۡشَاجٖ نَّبۡتَلِيهِ فَجَعَلۡنَٰهُ سَمِيعَۢا بَصِيرًا

Ndithu Ife tamlenga munthu kuchokera ku mbewu ya munthu yosakanikirana (ya mkazi ndi ya mwamuna) kuti timuyese mayeso (ndi malamulo Athu); choncho tidampanga kukhala wakumva ndi wopenya; (amve mawu a Allah ndi kuti aone zisonyezo Zake). info
التفاسير:

external-link copy
3 : 76

إِنَّا هَدَيۡنَٰهُ ٱلسَّبِيلَ إِمَّا شَاكِرٗا وَإِمَّا كَفُورًا

Ndithu Ife tidamlongosolera njira yoongoka: kukhala wokhulupirira kapena wotsutsa (Zonse zili kwa iye). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 76

إِنَّآ أَعۡتَدۡنَا لِلۡكَٰفِرِينَ سَلَٰسِلَاْ وَأَغۡلَٰلٗا وَسَعِيرًا

Ndithu Ife okana tawakonzera unyolo (wam’miyendo yawo) ndi magoli (am’manja ndi m’makosi awo) ndi Moto waukali woyaka. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 76

إِنَّ ٱلۡأَبۡرَارَ يَشۡرَبُونَ مِن كَأۡسٖ كَانَ مِزَاجُهَا كَافُورًا

Ndithu ochita zabwino adzamwa vinyo, chosakanizira chake chidzakhala (madzi a) kaafura. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 76

عَيۡنٗا يَشۡرَبُ بِهَا عِبَادُ ٱللَّهِ يُفَجِّرُونَهَا تَفۡجِيرٗا

(Kaafura ameneyo) ndikasupe amene adzikamwapo akapolo a Allah ndi kumtulutsa (paliponse pamene afuna) kumtulutsa mofewa. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 76

يُوفُونَ بِٱلنَّذۡرِ وَيَخَافُونَ يَوۡمٗا كَانَ شَرُّهُۥ مُسۡتَطِيرٗا

(Amene) akukwaniritsa zimene adalonjeza (okha kwa Allah), ndiponso akuopa tsiku (lalikulu) limene zoipa zake zidzakhala zofalikira ponseponse. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 76

وَيُطۡعِمُونَ ٱلطَّعَامَ عَلَىٰ حُبِّهِۦ مِسۡكِينٗا وَيَتِيمٗا وَأَسِيرًا

Ndipo amadyetsa chakudya masikini, amasiye ndi ogwidwa pa nkhondo, pomwe iwo akuchifunanso. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 76

إِنَّمَا نُطۡعِمُكُمۡ لِوَجۡهِ ٱللَّهِ لَا نُرِيدُ مِنكُمۡ جَزَآءٗ وَلَا شُكُورًا

Amanena (chamumtima akamapereka chakudyacho): “Tikukudyetsani chifukwa chofuna chikondi cha Allah basi; sitikufuna kwa inu malipiro kapena kuthokoza. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 76

إِنَّا نَخَافُ مِن رَّبِّنَا يَوۡمًا عَبُوسٗا قَمۡطَرِيرٗا

Ndithu ife tikuopa kwa Mbuye wathu tsiku lokhwinyata nkhope ndi mavuto akulu.” info
التفاسير:

external-link copy
11 : 76

فَوَقَىٰهُمُ ٱللَّهُ شَرَّ ذَٰلِكَ ٱلۡيَوۡمِ وَلَقَّىٰهُمۡ نَضۡرَةٗ وَسُرُورٗا

Ndipo Allah adzawateteza mu mavuto a tsiku limenelo ndiponso adzawapatsa mtendere ndi chisangalalo. info
التفاسير:

external-link copy
12 : 76

وَجَزَىٰهُم بِمَا صَبَرُواْ جَنَّةٗ وَحَرِيرٗا

Ndipo adzawalipira chifukwa cha kupirira kwawo Munda wamtendere ndi nsalu zaveleveti. info
التفاسير:

external-link copy
13 : 76

مُّتَّكِـِٔينَ فِيهَا عَلَى ٱلۡأَرَآئِكِۖ لَا يَرَوۡنَ فِيهَا شَمۡسٗا وَلَا زَمۡهَرِيرٗا

Atatsamira m’menemo pa makama (amtengo wapatali); sadzamva m’menemo kutentha kwa dzuwa kapena kuzizira. info
التفاسير:

external-link copy
14 : 76

وَدَانِيَةً عَلَيۡهِمۡ ظِلَٰلُهَا وَذُلِّلَتۡ قُطُوفُهَا تَذۡلِيلٗا

Mithunzi yake ikawayandikira iwo ndipo mikoko yazipatso idzatewa pafupi (moti munthu atha kuthyola ali chigonere). info
التفاسير:

external-link copy
15 : 76

وَيُطَافُ عَلَيۡهِم بِـَٔانِيَةٖ مِّن فِضَّةٖ وَأَكۡوَابٖ كَانَتۡ قَوَارِيرَا۠

Ndipo adzakhala akuzunguliridwa (ndi otumikira) uku atatenga zomwera za siliva ndi matambula onyezimira ndiponso olangala. info
التفاسير:

external-link copy
16 : 76

قَوَارِيرَاْ مِن فِضَّةٖ قَدَّرُوهَا تَقۡدِيرٗا

Zolangala zopangidwa ku siliva, atalinga bwino zakumwazo (malinga ndi kufuna kwawo). info
التفاسير:

external-link copy
17 : 76

وَيُسۡقَوۡنَ فِيهَا كَأۡسٗا كَانَ مِزَاجُهَا زَنجَبِيلًا

Ndipo (anthu abwino) akamwetsedwa kumeneko vinyo, chosakanizira chake chikafanana ndi Zanjabila (chikasu). info
التفاسير:

external-link copy
18 : 76

عَيۡنٗا فِيهَا تُسَمَّىٰ سَلۡسَبِيلٗا

M’menemo muli kasupe wotchedwa Salisabila, info
التفاسير:

external-link copy
19 : 76

۞ وَيَطُوفُ عَلَيۡهِمۡ وِلۡدَٰنٞ مُّخَلَّدُونَ إِذَا رَأَيۡتَهُمۡ حَسِبۡتَهُمۡ لُؤۡلُؤٗا مَّنثُورٗا

Ndipo azikawazungulira anyamata osasinthika (chilengedwe chawo,) utawaona (chifukwa cha kukongola kwawo ndi kuwala kwa nkhope zawo) ungawaganizire kuti ndi ngale zomwazidwa. info
التفاسير:

external-link copy
20 : 76

وَإِذَا رَأَيۡتَ ثَمَّ رَأَيۡتَ نَعِيمٗا وَمُلۡكٗا كَبِيرًا

Ndipo ukadzaona kumeneko (ku Jannah) ukaona mtendere ndi ufumu waukulu. info
التفاسير:

external-link copy
21 : 76

عَٰلِيَهُمۡ ثِيَابُ سُندُسٍ خُضۡرٞ وَإِسۡتَبۡرَقٞۖ وَحُلُّوٓاْ أَسَاوِرَ مِن فِضَّةٖ وَسَقَىٰهُمۡ رَبُّهُمۡ شَرَابٗا طَهُورًا

Pamwamba pawo padzakhala nsalu zaveleveti zopyapyala, zobiriwira ndi nsalu zaveleveti zochindikala, akavekedwa m’manja mwawo zibangiri zasiliva; Mbuye wawo akawamwetsa chakumwa china choyera kwambiri. info
التفاسير:

external-link copy
22 : 76

إِنَّ هَٰذَا كَانَ لَكُمۡ جَزَآءٗ وَكَانَ سَعۡيُكُم مَّشۡكُورًا

(Akawauza kuti:) “Ndithu iyi ndi mphoto yanu ndipo ntchito zanu ndi zolandiridwa.” info
التفاسير:

external-link copy
23 : 76

إِنَّا نَحۡنُ نَزَّلۡنَا عَلَيۡكَ ٱلۡقُرۡءَانَ تَنزِيلٗا

Ndithu Ife taivumbulutsa kwa iwe Qur’an mwapang’onopang’ono (kuti uisunge bwino, usaiwale). info
التفاسير:

external-link copy
24 : 76

فَٱصۡبِرۡ لِحُكۡمِ رَبِّكَ وَلَا تُطِعۡ مِنۡهُمۡ ءَاثِمًا أَوۡ كَفُورٗا

Choncho, pirira ndi lamulo la Mbuye wako ndipo usamvere wamachimo kapena wokanira aliyense mwa iwo. info
التفاسير:

external-link copy
25 : 76

وَٱذۡكُرِ ٱسۡمَ رَبِّكَ بُكۡرَةٗ وَأَصِيلٗا

Ndipo kumbukira dzina la Mbuye wako; mmawa, ndi madzulo (Swala za Subuhi, Dhuhr ndi Asri). info
التفاسير:

external-link copy
26 : 76

وَمِنَ ٱلَّيۡلِ فَٱسۡجُدۡ لَهُۥ وَسَبِّحۡهُ لَيۡلٗا طَوِيلًا

Ndipo usiku mlambire Iye, (Swala ya Maghrib ndi Isha); ndiponso umulemekeze usiku nthawi yaitali (popemphera sunna za tahajjudi). info
التفاسير:

external-link copy
27 : 76

إِنَّ هَٰٓؤُلَآءِ يُحِبُّونَ ٱلۡعَاجِلَةَ وَيَذَرُونَ وَرَآءَهُمۡ يَوۡمٗا ثَقِيلٗا

Ndithu awa akukonda moyo wa dziko lapansi, ndipo akulisiya kumbuyo kwao tsiku lovuta. info
التفاسير:

external-link copy
28 : 76

نَّحۡنُ خَلَقۡنَٰهُمۡ وَشَدَدۡنَآ أَسۡرَهُمۡۖ وَإِذَا شِئۡنَا بَدَّلۡنَآ أَمۡثَٰلَهُمۡ تَبۡدِيلًا

Ife ndi amene tidawalenga ndipo tidalimbika kalengedwe kawo; ndipo titafuna tingabweretse ena onga iwo (omvera Allah) kulowa m’malo mwawo. info
التفاسير:

external-link copy
29 : 76

إِنَّ هَٰذِهِۦ تَذۡكِرَةٞۖ فَمَن شَآءَ ٱتَّخَذَ إِلَىٰ رَبِّهِۦ سَبِيلٗا

Ndithu ichi ndichikumbutso choncho amene afuna atsata njira yopitira kwa Mbuye wake (pomukhulupirira ndi kumumvera). info
التفاسير:

external-link copy
30 : 76

وَمَا تَشَآءُونَ إِلَّآ أَن يَشَآءَ ٱللَّهُۚ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ عَلِيمًا حَكِيمٗا

Koma simungafune nokha chilichonse pokhapokha atafuna Allah, ndithu Allah ndi Wodziwa zedi, Wanzeru zakuya. info
التفاسير:

external-link copy
31 : 76

يُدۡخِلُ مَن يَشَآءُ فِي رَحۡمَتِهِۦۚ وَٱلظَّٰلِمِينَ أَعَدَّ لَهُمۡ عَذَابًا أَلِيمَۢا

Akumlowetsa amene wamfuna ku chifundo Chake; koma oyipa wawalinganizira chilango chowawa kwambiri. info
التفاسير: