[370] Sura imeneyi, Mtumiki (s.a.w) amafuna kuti msilamu aliyense ailoweze pamtima ndi kuzindikira bwino tanthauzo lake. Mtumiki (s.a.w) adali ndi chizolowezi chomawerenga Surayi asanagone. M’sura imeneyi muli chikumbutso chosonyeza kuti Allah Ngwamphamvu amachita mmene angafunire. Chimene wafuna chichitika ngakhale anthu sakufuna. Ndipo chimene sanafune kuti chichitike sichingachitike ngakhale anthu atafunitsitsa kuti chichitike. Zonse zakumwamba ndi zam’nthaka ndiZake.
[371] M’ma Ayah awa:- Allah akutilangiza kuti tikhale oganizira zomwe adalenga zimene zingatisonyeze nzeru Zake ndi mphamvu Zake zakuya. Tilingalire m’zolengedwa Zake, tisalingalire mwa Iye mwini chifukwa sitingathe kumlingalira mmene alili pomwe tikulephera kuulingalira mzimu wathu momwe ulili.