[361] Arabu amatchedwa “Ummiyyuna” chifukwa chakuti samadziwa kulemba ndi kuwerenga. Kusadziwa kulemba ndi kuwerenga kudafala pakati pawo ndipo ngakhale Mtumiki amene samadziwa kulemba ndi kuwerenga chilichonse. M’ndime imeneyi, Allah akutiphunzitsa kuti adampereka Muhammad (s.a.w) kuti awaongolere anthu ku njira yoongoka. Iyeyu adaperekedwa panyengo imene anthu adali ndi khumbo la Mneneri wa Allah kuti awatsogolere ku njira yolungama pakuti pa nthawiyo zipembedzo zonse za Allah zidali zitaonongeka. Pachiyambi Arabu amatsatira chipembedzo cha Ibrahim. Kenako adasintha nkuyamba kupembedza mafano. Adayambitsa zinthu zambiri zosalolezedwa ndi Allah. Ndipo nawonso anthu amabuku, Ayuda ndi Akhrisitu, adasintha zophunzitsa za mabuku awo. Choncho Allah adapereka Muhammad (s.a.w) ndi malamulo aakulu okwanira bwino. Mkati mwake mudali chilichonse chofunika m’moyo wa anthu pa nyengo zosiyanasiyana pa moyo wa pa dziko ndi wa pa tsiku lachimaliziro. Allah adampatsa zabwino zomwe sadampatseponso wina aliyense, woyamba ndi womaliza.
[362] Allah Wotukuka, akufanizira Ayuda amene amadziwa kuwerenga Taurat bwinobwino, koma zomwe akuwerengazo osazigwiritsa ntchito, ngati bulu wosenza mabuku akuluakulu popanda chopeza pomwe mabukuwo ali odzaza ndi zinthu zabwino zophunzitsa nzeru zabwino.
[363] M’ndime imeneyi akutiphunzitsa kuti tikamva adhana (kuitana) tsiku la Ijuma, tisiye chilichonse chimene tikuchita ndi kupita mwachangu kukapemphera pemphero la Ijuma. Pempheroli ndilofunika kwa msilamu aliyense makamaka amuna. Asilamu amasonkhana m’Misikiti ikuluikulu pa tsiku limeneli pa sabata iliyonse. Ndipo pa tsiku limeneli ndipomwe Allah adakwaniritsa zolenga zake zonse. Adam adalengedwa pa tsikuli ndipo adalowetsedwa ku Jannah tsiku lomweli. Ndipo adatulutsidwa m’menemo pa tsiku la Ijuma. Mtumiki adafotokozanso za kuti Qiyâma idzadza tsiku la Ijuma.