Qurani Kərimin mənaca tərcüməsi - Şişyo dilinə tərcümə - Xalid İbrahim Bəytələ.

Ash-Shûra

external-link copy
1 : 42

حمٓ

Hâ-Mîm. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 42

عٓسٓقٓ

‘Aîn-Sîn-Qâf. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 42

كَذَٰلِكَ يُوحِيٓ إِلَيۡكَ وَإِلَى ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِكَ ٱللَّهُ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ

Chomwecho akukuvumbulutsira iwe ndi atumiki amene adadza kale, Allah Ngopambana Wanzeru zakuya. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 42

لَهُۥ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۖ وَهُوَ ٱلۡعَلِيُّ ٱلۡعَظِيمُ

Zonse za kumwamba ndi pansi ndi za Iye Yekha. Ndipo Iye ndi Wotukuka, Wamkulu. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 42

تَكَادُ ٱلسَّمَٰوَٰتُ يَتَفَطَّرۡنَ مِن فَوۡقِهِنَّۚ وَٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ يُسَبِّحُونَ بِحَمۡدِ رَبِّهِمۡ وَيَسۡتَغۡفِرُونَ لِمَن فِي ٱلۡأَرۡضِۗ أَلَآ إِنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡغَفُورُ ٱلرَّحِيمُ

(Chifukwa chakukula Kwake ndi ulemelero Wake) mitambo ikuyandikira kuphwasuka pamwamba pa iyo. Ndipo angelo akulemekeza ndi kutamanda Mbuye wawo, ndi kuwapemphera chikhululuko amene ali pa dziko lapansi. Dziwani kuti ndithu Allah Yekha ndiye Wokhululuka kwabasi, Wachisoni chosatha. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 42

وَٱلَّذِينَ ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِهِۦٓ أَوۡلِيَآءَ ٱللَّهُ حَفِيظٌ عَلَيۡهِمۡ وَمَآ أَنتَ عَلَيۡهِم بِوَكِيلٖ

Ndipo awo amene adzipangira athandizi (a mafano) kusiya Allah, Allah ndi Wolondera (zochita) zawo; ndipo iwe si muyang’anili wawo (wosunga zochita zawo). info
التفاسير:

external-link copy
7 : 42

وَكَذَٰلِكَ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ قُرۡءَانًا عَرَبِيّٗا لِّتُنذِرَ أُمَّ ٱلۡقُرَىٰ وَمَنۡ حَوۡلَهَا وَتُنذِرَ يَوۡمَ ٱلۡجَمۡعِ لَا رَيۡبَ فِيهِۚ فَرِيقٞ فِي ٱلۡجَنَّةِ وَفَرِيقٞ فِي ٱلسَّعِيرِ

Chomwechonso (monga chilili chivumbulutso chapoyerachi) takuvumbulutsira Qur’an m’Chiarabu (popanda chikaiko) kuti uchenjeze (eni) manthu wa mizinda (Makka) ndi amene ali m’mbali mwake, ndikutinso uchenjeze (anthu) za tsiku la msonkhano, lopanda chikaiko. (Pa tsikulo anthu adzagawikana mmagulu awiri): gulu lina ku Jannah, ndipo gulu lina ku Moto. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 42

وَلَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ لَجَعَلَهُمۡ أُمَّةٗ وَٰحِدَةٗ وَلَٰكِن يُدۡخِلُ مَن يَشَآءُ فِي رَحۡمَتِهِۦۚ وَٱلظَّٰلِمُونَ مَا لَهُم مِّن وَلِيّٖ وَلَا نَصِيرٍ

Ndipo akadafuna Allah akadawachita iwo kukhala mpingo umodzi; koma amamulowetsa ku chifundo Chake amene wamfuna ndipo odzichitira okha chinyengo (pokana Allah) alibe mtetezi kapena mthandizi. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 42

أَمِ ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِهِۦٓ أَوۡلِيَآءَۖ فَٱللَّهُ هُوَ ٱلۡوَلِيُّ وَهُوَ يُحۡيِ ٱلۡمَوۡتَىٰ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ

Kapena adzichitira athandizi ena kusiya Iye (Allah)? Pomwe Allah Yekha ndiye Mthandizi woona ndipo Iye amaukitsa akufa. Ndipo Iye ndi Wokhoza pa chilichonse. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 42

وَمَا ٱخۡتَلَفۡتُمۡ فِيهِ مِن شَيۡءٖ فَحُكۡمُهُۥٓ إِلَى ٱللَّهِۚ ذَٰلِكُمُ ٱللَّهُ رَبِّي عَلَيۡهِ تَوَكَّلۡتُ وَإِلَيۡهِ أُنِيبُ

Ndipo chilichonse chimene mwasiyana mmenemo (mchipembedzo: za kukhulupirira ndi kusakhulupirira) chiweruzo chake nkwa Allah; (bwererani ku Buku la Allah ndi Hadith za mtumiki Wake). Ndipo Ameneyo ndi Allah, Mbuye wanga; kwa Iye Yekha ndatsamira, ndipo kwa Iye Yekha (ndiko) ndikutembenukira. info
التفاسير: