Qurani Kərimin mənaca tərcüməsi - Şişyo dilinə tərcümə - Xalid İbrahim Bəytələ.

Səhifənin rəqəmi:close

external-link copy
6 : 28

وَنُمَكِّنَ لَهُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَنُرِيَ فِرۡعَوۡنَ وَهَٰمَٰنَ وَجُنُودَهُمَا مِنۡهُم مَّا كَانُواْ يَحۡذَرُونَ

Ndi kuwapatsa mphamvu za pa dziko (kuti azichita mmene angafunire) ndi kuti timuonetse Farawo ndi Hamana ndi magulu awo ankhondo kuchokera kwa iwo (ana a Israel), zomwe amaziwopa (kuti zingawathetsere ufumu wawo). info
التفاسير:

external-link copy
7 : 28

وَأَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰٓ أُمِّ مُوسَىٰٓ أَنۡ أَرۡضِعِيهِۖ فَإِذَا خِفۡتِ عَلَيۡهِ فَأَلۡقِيهِ فِي ٱلۡيَمِّ وَلَا تَخَافِي وَلَا تَحۡزَنِيٓۖ إِنَّا رَآدُّوهُ إِلَيۡكِ وَجَاعِلُوهُ مِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ

Ndipo tidamzindikiritsa mayi wa Mûsa (tinati): “Muyamwitse (mwana wako), ndipo ukamuopera (chiwembu cha Farawo), mponye mu mtsinje usaope, ndipo usadandaule ndithu Ife tidzamubwezera kwa iwe, ndipo tidzamchita kukhala mmodzi wa atumiki.” info
التفاسير:

external-link copy
8 : 28

فَٱلۡتَقَطَهُۥٓ ءَالُ فِرۡعَوۡنَ لِيَكُونَ لَهُمۡ عَدُوّٗا وَحَزَنًاۗ إِنَّ فِرۡعَوۡنَ وَهَٰمَٰنَ وَجُنُودَهُمَا كَانُواْ خَٰطِـِٔينَ

Choncho adamtola anthu a Farawo kuti mapeto ake adzakhale m’dani kwa iwo ndi odandaulitsa. Ndithu Farawo ndi Hamana ndi magulu awo ankhondo adali olakwa. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 28

وَقَالَتِ ٱمۡرَأَتُ فِرۡعَوۡنَ قُرَّتُ عَيۡنٖ لِّي وَلَكَۖ لَا تَقۡتُلُوهُ عَسَىٰٓ أَن يَنفَعَنَآ أَوۡ نَتَّخِذَهُۥ وَلَدٗا وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ

Ndipo mkazi wa Farawo adati: “(Musamuphe, akhale) chosangalatsa diso langa ndi lako; musamuphe mwina angatithandize, kapena tingam’chite kukhala mwana (wathu.” Adanena izi) iwo asakudziwa (kuti adzakhala m’dani wawo). info
التفاسير:

external-link copy
10 : 28

وَأَصۡبَحَ فُؤَادُ أُمِّ مُوسَىٰ فَٰرِغًاۖ إِن كَادَتۡ لَتُبۡدِي بِهِۦ لَوۡلَآ أَن رَّبَطۡنَا عَلَىٰ قَلۡبِهَا لِتَكُونَ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ

Ndipo mu mtima mwa mayi wa Mûsa mudali mopanda kanthu (mudalibe maganizo ena koma maganizo a mwana wake). Padatsala pang’ono kuti aonetse (chinsinsi cha mwanayo ponena kuti adali mwana wake), tikadapanda kulimbitsa mtima wake, kuti akhale mmodzi mwa okhulupirira (lonjezo la Allah). info
التفاسير:

external-link copy
11 : 28

وَقَالَتۡ لِأُخۡتِهِۦ قُصِّيهِۖ فَبَصُرَتۡ بِهِۦ عَن جُنُبٖ وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ

Ndipo (mayi wa Musayo) adauza mlongo wake (wa Mûsa): “Mtsatire, (komwe madzi akupita naye).” Choncho iye ankamuyang’ana chapatali pomwe iwo samadziwa (za ichi). info
التفاسير:

external-link copy
12 : 28

۞ وَحَرَّمۡنَا عَلَيۡهِ ٱلۡمَرَاضِعَ مِن قَبۡلُ فَقَالَتۡ هَلۡ أَدُلُّكُمۡ عَلَىٰٓ أَهۡلِ بَيۡتٖ يَكۡفُلُونَهُۥ لَكُمۡ وَهُمۡ لَهُۥ نَٰصِحُونَ

Ndipo poyamba tidamuletsa kuti asayamwe mawere a woyamwitsa, (kufikira pomwe mlongo wake) adati: “Kodi ndikusonyezeni eni nyumba omwe angakulelereni ndi kukhala naye momteteza bwino mwanayo?” info
التفاسير:

external-link copy
13 : 28

فَرَدَدۡنَٰهُ إِلَىٰٓ أُمِّهِۦ كَيۡ تَقَرَّ عَيۡنُهَا وَلَا تَحۡزَنَ وَلِتَعۡلَمَ أَنَّ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقّٞ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ

Choncho tidamubwezera kwa mayi wake kuti maso ake atonthole, (mtima wake ukhazikike) ndi kuti asadandaule; ndi kuti adziwe kuti lonjezo la Allah ndi loona. Koma ambiri a iwo sadziwa. info
التفاسير: