Qurani Kərimin mənaca tərcüməsi - Şişyo dilinə tərcümə - Xalid İbrahim Bəytələ.

Səhifənin rəqəmi:close

external-link copy
56 : 25

وَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ إِلَّا مُبَشِّرٗا وَنَذِيرٗا

Ndipo Ife sitidakutume koma kuti ukhale wouza nkhani zabwino (okhulupirira); ndi wochenjeza (osakhulupirira). info
التفاسير:

external-link copy
57 : 25

قُلۡ مَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مِنۡ أَجۡرٍ إِلَّا مَن شَآءَ أَن يَتَّخِذَ إِلَىٰ رَبِّهِۦ سَبِيلٗا

Nena: “Sindikupemphani malipiro pa zimenezi (zomwe ndikukuphunzitsani) koma amene afuna ayende pa njira yopita kwa Mbuye wake, (popanda chopereka).” info
التفاسير:

external-link copy
58 : 25

وَتَوَكَّلۡ عَلَى ٱلۡحَيِّ ٱلَّذِي لَا يَمُوتُ وَسَبِّحۡ بِحَمۡدِهِۦۚ وَكَفَىٰ بِهِۦ بِذُنُوبِ عِبَادِهِۦ خَبِيرًا

Ndipo tsamira kwa (Allah) Wamoyo, Wamuyaya Yemwe saafa. Ndipo mulemekeze pomtamanda ndi mbiri Zake. Ndipo Iye akukwana kudziwa bwinobwino machimo a akapolo Ake. info
التفاسير:

external-link copy
59 : 25

ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَا فِي سِتَّةِ أَيَّامٖ ثُمَّ ٱسۡتَوَىٰ عَلَى ٱلۡعَرۡشِۖ ٱلرَّحۡمَٰنُ فَسۡـَٔلۡ بِهِۦ خَبِيرٗا

Yemwe adalenga thambo ndi nthaka ndi zimene zikupezeka mkati mwake. (Adazilenga) m’masiku asanu ndi limodzi, ndipo adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu, m’kukhazikika kodziwa Yekha). Iye Ngwachifundo chambiri; mufunseni wodziwa za Iye. info
التفاسير:

external-link copy
60 : 25

وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ ٱسۡجُدُواْۤ لِلرَّحۡمَٰنِ قَالُواْ وَمَا ٱلرَّحۡمَٰنُ أَنَسۡجُدُ لِمَا تَأۡمُرُنَا وَزَادَهُمۡ نُفُورٗا۩

Ndipo akauzidwa (kuti): “Mulambireni (Allah) Wachifundo chambiri.” Amati: “Ndani Wachifundo chambiri? Kodi tilambire Yemwe iwe ukutilamula?” (Mawu amenewa) adawaonjezera iwo mwano. info
التفاسير:

external-link copy
61 : 25

تَبَارَكَ ٱلَّذِي جَعَلَ فِي ٱلسَّمَآءِ بُرُوجٗا وَجَعَلَ فِيهَا سِرَٰجٗا وَقَمَرٗا مُّنِيرٗا

Watukuka Mwini kupereka madalitso Yemwe adakhazikitsa nyenyezi ku thambo, ndipo m’menemo adaika nyali (dzuwa) ndi mwezi wounika. info
التفاسير:

external-link copy
62 : 25

وَهُوَ ٱلَّذِي جَعَلَ ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَ خِلۡفَةٗ لِّمَنۡ أَرَادَ أَن يَذَّكَّرَ أَوۡ أَرَادَ شُكُورٗا

Ndipo Iye ndi Yemwe adapanga usiku ndi usana kuti zizitsatana (ndikusinthana). (Izi zingapindulitse) kwa amene afuna kukumbukira kapena (amene) afuna kuthokoza. info
التفاسير:

external-link copy
63 : 25

وَعِبَادُ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلَّذِينَ يَمۡشُونَ عَلَى ٱلۡأَرۡضِ هَوۡنٗا وَإِذَا خَاطَبَهُمُ ٱلۡجَٰهِلُونَ قَالُواْ سَلَٰمٗا

Ndipo akapolo a (Allah) Wachifundo chambiri ndi omwe akuyenda pa dziko modzichepetsa, ndipo mbuli zikanena kwa iwo (mawu amwano), amaziyankha mawu abwino. info
التفاسير:

external-link copy
64 : 25

وَٱلَّذِينَ يَبِيتُونَ لِرَبِّهِمۡ سُجَّدٗا وَقِيَٰمٗا

Ndi omwe amapititsa nthawi ina ya usiku uku akulambira ndi kuimilira chifukwa cha kulemekeza Mbuye wawo. info
التفاسير:

external-link copy
65 : 25

وَٱلَّذِينَ يَقُولُونَ رَبَّنَا ٱصۡرِفۡ عَنَّا عَذَابَ جَهَنَّمَۖ إِنَّ عَذَابَهَا كَانَ غَرَامًا

Ndi omwe akunena: “E Mbuye wathu tipewetsereni chilango cha Jahannam; ndithu chilango chake nchosasiyana nacho.” info
التفاسير:

external-link copy
66 : 25

إِنَّهَا سَآءَتۡ مُسۡتَقَرّٗا وَمُقَامٗا

“Ndithu iyo ndi malo woipa; ndiponso pokhala poipa.” info
التفاسير:

external-link copy
67 : 25

وَٱلَّذِينَ إِذَآ أَنفَقُواْ لَمۡ يُسۡرِفُواْ وَلَمۡ يَقۡتُرُواْ وَكَانَ بَيۡنَ ذَٰلِكَ قَوَامٗا

Ndi omwe amati akamagawira anthu ena chuma chawo, samwaza pachabe ndiponso sachita umbombo, koma amachita mwapakatikati. info
التفاسير: