Qurani Kərimin mənaca tərcüməsi - Şişyo dilinə tərcümə - Xalid İbrahim Bəytələ.

An-Nûr

external-link copy
1 : 24

سُورَةٌ أَنزَلۡنَٰهَا وَفَرَضۡنَٰهَا وَأَنزَلۡنَا فِيهَآ ءَايَٰتِۭ بَيِّنَٰتٖ لَّعَلَّكُمۡ تَذَكَّرُونَ

Iyi ndi Sura; taivumbulutsa, ndipo taikamo malamulo. Ndipo m’menemo tatumizamo Ayah (ndime) zomveka kuti mukumbukire (malamulo ndi kuchita nawo m’njira yoyenera). info
التفاسير:

external-link copy
2 : 24

ٱلزَّانِيَةُ وَٱلزَّانِي فَٱجۡلِدُواْ كُلَّ وَٰحِدٖ مِّنۡهُمَا مِاْئَةَ جَلۡدَةٖۖ وَلَا تَأۡخُذۡكُم بِهِمَا رَأۡفَةٞ فِي دِينِ ٱللَّهِ إِن كُنتُمۡ تُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَٱلۡيَوۡمِ ٱلۡأٓخِرِۖ وَلۡيَشۡهَدۡ عَذَابَهُمَا طَآئِفَةٞ مِّنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ

Mkazi wachiwerewere ndi mwamuna wa chiwerewere aliyense wa iwo mkwapuleni zikoti zana limodzi (100). Musagwidwe chisoni ndi iwo pa chipembedzo (malamulo) cha Allah, ngati inu mukukhulupiriradi mwa Allah ndi tsiku la chimaliziro. Ndipo gulu la okhulupirira lionelere chilango chawo. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 24

ٱلزَّانِي لَا يَنكِحُ إِلَّا زَانِيَةً أَوۡ مُشۡرِكَةٗ وَٱلزَّانِيَةُ لَا يَنكِحُهَآ إِلَّا زَانٍ أَوۡ مُشۡرِكٞۚ وَحُرِّمَ ذَٰلِكَ عَلَى ٱلۡمُؤۡمِنِينَ

Mwamuna wa chiwerewere sakwatira mkazi (wabwino) koma wachiwerewere mnzake, kapena mkazi wopembedza mafano. Nayenso mkazi wachiwerewere sakwatiwa ndi mwamuna (wabwino) koma wachiwerewere mnzake, kapena wopembedza mafano. Ndipo zimenezi zaletsedwa kwa okhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 24

وَٱلَّذِينَ يَرۡمُونَ ٱلۡمُحۡصَنَٰتِ ثُمَّ لَمۡ يَأۡتُواْ بِأَرۡبَعَةِ شُهَدَآءَ فَٱجۡلِدُوهُمۡ ثَمَٰنِينَ جَلۡدَةٗ وَلَا تَقۡبَلُواْ لَهُمۡ شَهَٰدَةً أَبَدٗاۚ وَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡفَٰسِقُونَ

Ndipo amene akunamizira akazi odziteteza (powanamizira kuti achita chiwerewere), ndipo osabwera nazo mboni zinayi, akwapuleni zikoti 80; ndiponso musauvomereze umboni wawo mpaka kalekale. Iwo ngotuluka m’chilamulo cha Allah, info
التفاسير:

external-link copy
5 : 24

إِلَّا ٱلَّذِينَ تَابُواْ مِنۢ بَعۡدِ ذَٰلِكَ وَأَصۡلَحُواْ فَإِنَّ ٱللَّهَ غَفُورٞ رَّحِيمٞ

Kupatula amene alapa pambuyo pa zimenezo, ndipo nkukonza (zochita zawo), ndithu Allah Ngokhululuka; Ngwachisoni, (awakhululukira). info
التفاسير:

external-link copy
6 : 24

وَٱلَّذِينَ يَرۡمُونَ أَزۡوَٰجَهُمۡ وَلَمۡ يَكُن لَّهُمۡ شُهَدَآءُ إِلَّآ أَنفُسُهُمۡ فَشَهَٰدَةُ أَحَدِهِمۡ أَرۡبَعُ شَهَٰدَٰتِۭ بِٱللَّهِ إِنَّهُۥ لَمِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ

Ndipo amene akunamizira akazi awo (kuti achita chiwerewere) ndipo iwo nkukhala opanda mboni, koma (iwo) okha, choncho umboni wa mmodzi wa iwo (umene ungamchotsere chilango chomenyedwa zikoti 80), ndikupereka umboni kanayi polumbilira Allah kuti ndithu iye ndi mmodzi mwa onena zoona. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 24

وَٱلۡخَٰمِسَةُ أَنَّ لَعۡنَتَ ٱللَّهِ عَلَيۡهِ إِن كَانَ مِنَ ٱلۡكَٰذِبِينَ

Ndipo kachisanu (alumbire) kuti matembelero a Allah akhale pa iye ngati (iye) ali m’modzi mwa onama. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 24

وَيَدۡرَؤُاْ عَنۡهَا ٱلۡعَذَابَ أَن تَشۡهَدَ أَرۡبَعَ شَهَٰدَٰتِۭ بِٱللَّهِ إِنَّهُۥ لَمِنَ ٱلۡكَٰذِبِينَ

Ndipo (mkazi) chilango amchotsera atapereka umboni kanayi polumbilira Allah kuti (uyu mwamuna) ndi mmodzi mwa onama. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 24

وَٱلۡخَٰمِسَةَ أَنَّ غَضَبَ ٱللَّهِ عَلَيۡهَآ إِن كَانَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ

Ndipo kachisanu (alumbire) kuti mkwiyo wa Allah ukhale pa iye ngati (mwamuna wake) ali mmodzi mwa onena zoona. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 24

وَلَوۡلَا فَضۡلُ ٱللَّهِ عَلَيۡكُمۡ وَرَحۡمَتُهُۥ وَأَنَّ ٱللَّهَ تَوَّابٌ حَكِيمٌ

Ndipo pakadapanda ubwino wa Allah ndi chifundo Chake pa inu (mukadavutika). Ndipo ndithu Allah Ngolandira kulapa;. Wanzeru zakuya. info
التفاسير: