Qurani Kərimin mənaca tərcüməsi - Şişyo dilinə tərcümə - Xalid İbrahim Bəytələ.

Səhifənin rəqəmi:close

external-link copy
38 : 2

قُلۡنَا ٱهۡبِطُواْ مِنۡهَا جَمِيعٗاۖ فَإِمَّا يَأۡتِيَنَّكُم مِّنِّي هُدٗى فَمَن تَبِعَ هُدَايَ فَلَا خَوۡفٌ عَلَيۡهِمۡ وَلَا هُمۡ يَحۡزَنُونَ

Tidati: “Tsikani m’menemo nonsenu. Ngati chitakufikani chiongoko chochokera kwa Ine, choncho amene adzatsate chiongoko Changacho, pa iwo sipadzakhala mantha. Ndiponso iwo sadzadandaula.” info
التفاسير:

external-link copy
39 : 2

وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَكَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَآ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلنَّارِۖ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ

“Koma amene sanakhulupirire natsutsa mawu athu, iwowo ndiwo anthu a ku Moto. M’menemo akakhalamo nthawi yaitali.” info
التفاسير:

external-link copy
40 : 2

يَٰبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ٱذۡكُرُواْ نِعۡمَتِيَ ٱلَّتِيٓ أَنۡعَمۡتُ عَلَيۡكُمۡ وَأَوۡفُواْ بِعَهۡدِيٓ أُوفِ بِعَهۡدِكُمۡ وَإِيَّٰيَ فَٱرۡهَبُونِ

E inu ana a Israyeli! kumbukirani chisomo Changa chomwe ndidakudalitsani nacho, ndipo kwaniritsani pangano Langa Nanenso ndikwaniritsi pangano lanu. Ndipo Ine Ndekha ndiopeni. info
التفاسير:

external-link copy
41 : 2

وَءَامِنُواْ بِمَآ أَنزَلۡتُ مُصَدِّقٗا لِّمَا مَعَكُمۡ وَلَا تَكُونُوٓاْ أَوَّلَ كَافِرِۭ بِهِۦۖ وَلَا تَشۡتَرُواْ بِـَٔايَٰتِي ثَمَنٗا قَلِيلٗا وَإِيَّٰيَ فَٱتَّقُونِ

Ndipo khulupirirani zimene ndavumbulutsa, zomwe zikuchitira umboni zimene muli nazo, ndipo musakhale oyamba kuzikana; ndipo musagulitse mawu Anga ndi (zinthu za) mtengo wochepa. Ndipo Ine Ndekha ndiopeni. info
التفاسير:

external-link copy
42 : 2

وَلَا تَلۡبِسُواْ ٱلۡحَقَّ بِٱلۡبَٰطِلِ وَتَكۡتُمُواْ ٱلۡحَقَّ وَأَنتُمۡ تَعۡلَمُونَ

Ndipo musasakanize choona ndi chonama; ndi kubisa choona uku mukudziwa. info
التفاسير:

external-link copy
43 : 2

وَأَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتُواْ ٱلزَّكَوٰةَ وَٱرۡكَعُواْ مَعَ ٱلرَّٰكِعِينَ

Ndipo pempherani Swala moyenera ndikupereka chopereka (Zakaat), ndipo weramani pamodzi ndi owerama. info
التفاسير:

external-link copy
44 : 2

۞ أَتَأۡمُرُونَ ٱلنَّاسَ بِٱلۡبِرِّ وَتَنسَوۡنَ أَنفُسَكُمۡ وَأَنتُمۡ تَتۡلُونَ ٱلۡكِتَٰبَۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ

Kodi mukulamula anthu kuchita zabwino ndi kudziiwala inu eni pomwe inu mukuwerenga Buku? Kodi simuzindikira? info
التفاسير:

external-link copy
45 : 2

وَٱسۡتَعِينُواْ بِٱلصَّبۡرِ وَٱلصَّلَوٰةِۚ وَإِنَّهَا لَكَبِيرَةٌ إِلَّا عَلَى ٱلۡخَٰشِعِينَ

Ndipo dzithandizeni (pa zinthu zanu) popirira ndi popemphera Swala. Ndithudi, Swala yo ndiyolemera kupatula kwa odzichepetsa (kwa Allah). info
التفاسير:

external-link copy
46 : 2

ٱلَّذِينَ يَظُنُّونَ أَنَّهُم مُّلَٰقُواْ رَبِّهِمۡ وَأَنَّهُمۡ إِلَيۡهِ رَٰجِعُونَ

Omwe akutsimikiza kuti adzakumana ndi Mbuye wawo, ndi kuti adzabwerera kwa Iye. info
التفاسير:

external-link copy
47 : 2

يَٰبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ٱذۡكُرُواْ نِعۡمَتِيَ ٱلَّتِيٓ أَنۡعَمۡتُ عَلَيۡكُمۡ وَأَنِّي فَضَّلۡتُكُمۡ عَلَى ٱلۡعَٰلَمِينَ

E inu ana a Israyeli! Kumbukirani chisomo Changa chomwe ndidakudalitsani nacho. Ndithudi, Ine ndinakuchitirani ubwino kuposa zolengedwa zonse (pa nthawiyo). info
التفاسير:

external-link copy
48 : 2

وَٱتَّقُواْ يَوۡمٗا لَّا تَجۡزِي نَفۡسٌ عَن نَّفۡسٖ شَيۡـٔٗا وَلَا يُقۡبَلُ مِنۡهَا شَفَٰعَةٞ وَلَا يُؤۡخَذُ مِنۡهَا عَدۡلٞ وَلَا هُمۡ يُنصَرُونَ

Choncho opani tsiku lomwe munthu aliyense sadzathandiza mnzake ndi chilichonse, ndipo sikudzavomerezedwa kwa iye (munthuyo) dandaulo lililonse, ndiponso silidzalandiridwa dipo kwa iye; ndipo iwo sadzapulumutsidwa. info
التفاسير: