Qurani Kərimin mənaca tərcüməsi - Şişyo dilinə tərcümə - Xalid İbrahim Bəytələ.

Səhifənin rəqəmi:close

external-link copy
89 : 10

قَالَ قَدۡ أُجِيبَت دَّعۡوَتُكُمَا فَٱسۡتَقِيمَا وَلَا تَتَّبِعَآنِّ سَبِيلَ ٱلَّذِينَ لَا يَعۡلَمُونَ

(Allah) adati: “Pempho lanu lavomerezedwa! Choncho lungamani mwaubwino, ndipo musatsate njira za omwe sadziwa.” info
التفاسير:

external-link copy
90 : 10

۞ وَجَٰوَزۡنَا بِبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ٱلۡبَحۡرَ فَأَتۡبَعَهُمۡ فِرۡعَوۡنُ وَجُنُودُهُۥ بَغۡيٗا وَعَدۡوًاۖ حَتَّىٰٓ إِذَآ أَدۡرَكَهُ ٱلۡغَرَقُ قَالَ ءَامَنتُ أَنَّهُۥ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا ٱلَّذِيٓ ءَامَنَتۡ بِهِۦ بَنُوٓاْ إِسۡرَٰٓءِيلَ وَأَنَا۠ مِنَ ٱلۡمُسۡلِمِينَ

Ndipo tidawaolotsa pa nyanja ana a Israyeli. Ndipo Farawo ndi asilikali ake ankhondo adawatsata moipitsa ndi mwamtopola, kufikira pamene kumira kudampeza; (iye) adati: “Ndakhulupirira kuti palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Yemwe ana a Israyeli amkhulupirira. Ndipo ine ndine mmodzi mwa Asilamu (omugonjera monga iwo akumgonjera).” info
التفاسير:

external-link copy
91 : 10

ءَآلۡـَٰٔنَ وَقَدۡ عَصَيۡتَ قَبۡلُ وَكُنتَ مِنَ ٱلۡمُفۡسِدِينَ

(Angelo adamuuza kuti:) “Tsopano (ndipamene ukukhulupirira), pomwe kale udanyoza ndikukhala mmodzi wa oononga!” info
التفاسير:

external-link copy
92 : 10

فَٱلۡيَوۡمَ نُنَجِّيكَ بِبَدَنِكَ لِتَكُونَ لِمَنۡ خَلۡفَكَ ءَايَةٗۚ وَإِنَّ كَثِيرٗا مِّنَ ٱلنَّاسِ عَنۡ ءَايَٰتِنَا لَغَٰفِلُونَ

“Choncho lero tikupulumutsa (polisunga) thupi lako, kuti ukhale chisonyezo kwa amene akudza m’mbuyo mwako (kuti adziwe kuti sudali mulungu). Koma ndithu anthu ambiri salabadira zisonyezo Zathu.” info
التفاسير:

external-link copy
93 : 10

وَلَقَدۡ بَوَّأۡنَا بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ مُبَوَّأَ صِدۡقٖ وَرَزَقۡنَٰهُم مِّنَ ٱلطَّيِّبَٰتِ فَمَا ٱخۡتَلَفُواْ حَتَّىٰ جَآءَهُمُ ٱلۡعِلۡمُۚ إِنَّ رَبَّكَ يَقۡضِي بَيۡنَهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ فِيمَا كَانُواْ فِيهِ يَخۡتَلِفُونَ

Ndipo ndithu (pambuyo pake) tidawakonzera mokhala mwabwino ana a Israyeli, ndikuwapatsa zabwino. Sadasiyane kufikira pamene kuzindikira kudawadzera. Ndithu Mbuye wako adzaweruza pakati pawo tsiku la Qiyâma pa zimene adali kutsutsana. info
التفاسير:

external-link copy
94 : 10

فَإِن كُنتَ فِي شَكّٖ مِّمَّآ أَنزَلۡنَآ إِلَيۡكَ فَسۡـَٔلِ ٱلَّذِينَ يَقۡرَءُونَ ٱلۡكِتَٰبَ مِن قَبۡلِكَۚ لَقَدۡ جَآءَكَ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّكَ فَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡمُمۡتَرِينَ

Ngati uli ndi chipeneko pa zimene takuvumbulutsira, afunse amene akuwerenga mabuku akale (Ayuda ndi Akhrisitu amene alowa m’Chisilamu). Ndithu choonadi chakufika kuchokera kwa Mbuye wako. Choncho usakhale mwa amene akukaikira. info
التفاسير:

external-link copy
95 : 10

وَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ فَتَكُونَ مِنَ ٱلۡخَٰسِرِينَ

Ndiponso usakhale mwa omwe akutsutsa zizindikiro za Allah, kuopa kuti ungadzakhale m’gulu la otaika. info
التفاسير:

external-link copy
96 : 10

إِنَّ ٱلَّذِينَ حَقَّتۡ عَلَيۡهِمۡ كَلِمَتُ رَبِّكَ لَا يُؤۡمِنُونَ

Ndithu aja amene liwu la Mbuye wako latsimikizika pa iwo, sakhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
97 : 10

وَلَوۡ جَآءَتۡهُمۡ كُلُّ ءَايَةٍ حَتَّىٰ يَرَوُاْ ٱلۡعَذَابَ ٱلۡأَلِيمَ

Ndipo ngakhale kuti chisonyezo chamtundu uliwonse chiwadzere (sangakhulupirirebe), mpaka aone chilango chopweteka. info
التفاسير: