[446] Tanthauzo lake ndikuti mwa anthu alipo ena amene amachita zabwino ndipo ena amachita zoipa. Ena amagwira ntchito zothandiza pambuyo pa imfa pamodzi ndi kutumikira Allah. Ndipo pali ena omwe amangokhala otanganidwa ndi zadziko lapansi. Ena amachita zinthu zopindula pomwe ena satero.
[447] Tanthauzo lake apa ndikupereka chuma ndi kudzipereka pa zauzimu. Ndiye kuti munthu agwiritsire ntchito chuma chake m’njira ya Allah ndiponso kwa anthu anzake. Ayeneranso kudzipereka iye mwini pa moyo wauzimu.
[450] (Ndime 19-20)Tanthauzo la ma Ayah awiriwa nkuti munthu uyu sakupereka chuma chake chifukwa chobwezera chifundo cha anthu, kapena kuti adzamubwezerenso iye chifundo, koma akupereka chifukwa chofuna chikondi cha Mbuye wake basi.
[451] Tanthauzo lake apa ndikuti Allah adzamukondweretsa ndi malipiro Ake abwino kufikira munthuyo adzakondwera. Ma Ayah, kuyambira 17 mpaka 21, adatsika chifukwa cha Sayyidina Abu Bakr (r.a) yemwe adali kupereka chuma chake powagula akapolo omwe adali kuzunzidwa ndi mabwana awo chifukwa cholowa Chisilamu, pambuyo pake amawapatsa ufulu. Ndipo m’modzi wa iwowa ndi Sayyidina Bilal (r.a) amene adali Muazzini wa Mneneri Muhammad (s.a.w). Chomwechonso Ayah zimenezi zikumkhudza aliyense amene akugwiritsa ntchito chuma chake mnjira yopulumutsira chipembedzo.