அல்குர்ஆன் மொழிபெயர்ப்பு - ஷேவா(Chewa) மொழிபெயர்ப்பு - காலித் இப்ராஹிம் பேடாலா

Al-Lail

external-link copy
1 : 92

وَٱلَّيۡلِ إِذَا يَغۡشَىٰ

Ndikulumbilira usiku pamene ukuphimba (chilichonse). info
التفاسير:

external-link copy
2 : 92

وَٱلنَّهَارِ إِذَا تَجَلَّىٰ

Ndi usana pamene kukuyera. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 92

وَمَا خَلَقَ ٱلذَّكَرَ وَٱلۡأُنثَىٰٓ

Ndiponso Yemwe adalenga chachimuna ndi chachikazi. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 92

إِنَّ سَعۡيَكُمۡ لَشَتَّىٰ

Ndithu zochita zanu nzosiyanasiyana.[446] info

[446] Tanthauzo lake ndikuti mwa anthu alipo ena amene amachita zabwino ndipo ena amachita zoipa. Ena amagwira ntchito zothandiza pambuyo pa imfa pamodzi ndi kutumikira Allah. Ndipo pali ena omwe amangokhala otanganidwa ndi zadziko lapansi. Ena amachita zinthu zopindula pomwe ena satero.

التفاسير:

external-link copy
5 : 92

فَأَمَّا مَنۡ أَعۡطَىٰ وَٱتَّقَىٰ

Tsono yemwe akupereka (pa njira ya Allah) ndikumamuopa (Mbuye wake ndikupewa zoletsedwa),[447] info

[447] Tanthauzo lake apa ndikupereka chuma ndi kudzipereka pa zauzimu. Ndiye kuti munthu agwiritsire ntchito chuma chake m’njira ya Allah ndiponso kwa anthu anzake. Ayeneranso kudzipereka iye mwini pa moyo wauzimu.

التفاسير:

external-link copy
6 : 92

وَصَدَّقَ بِٱلۡحُسۡنَىٰ

Ndikumavomereza zinthu zabwino; (komwe kuli kukhulupirira Allah mwanzeru),[448] info

[448] Tanthauzo la “Kuvomereza zinthu zabwino” ndiko kugwirizana nazo zimene Allah walamula, chifukwa chakuti Iye amalamula zinthu zabwino zokhazokha ndikuletsa zoipa.

التفاسير:

external-link copy
7 : 92

فَسَنُيَسِّرُهُۥ لِلۡيُسۡرَىٰ

Choncho timufewetsera njira yompititsa ku zabwino.[449] info

[449] Tanthauzo la Ayah imeneyi ndikuti: Timufewetsera njira yochitira zinthu zabwino mpaka kufikira kuti akapanda kuchita chinthu chabwino sapeza mtendere mu mtima mwake.

التفاسير:

external-link copy
8 : 92

وَأَمَّا مَنۢ بَخِلَ وَٱسۡتَغۡنَىٰ

Koma uyo achite umbombo ndikuganiza za kuti iye payekha ngokwana; info
التفاسير:

external-link copy
9 : 92

وَكَذَّبَ بِٱلۡحُسۡنَىٰ

Ndi kumatsutsa zinthu zabwino, info
التفاسير:

external-link copy
10 : 92

فَسَنُيَسِّرُهُۥ لِلۡعُسۡرَىٰ

Choncho timufewetsera njira yompititsa ku mavuto (a muyaya). info
التفاسير:

external-link copy
11 : 92

وَمَا يُغۡنِي عَنۡهُ مَالُهُۥٓ إِذَا تَرَدَّىٰٓ

Ndipo chuma chake sichidzamthandiza (chilichonse) akadzagwera ku Moto. info
التفاسير:

external-link copy
12 : 92

إِنَّ عَلَيۡنَا لَلۡهُدَىٰ

Ndithu Ife ndi amene timawalongosolera anthu njira yabwino ndi njira yoipa. info
التفاسير:

external-link copy
13 : 92

وَإِنَّ لَنَا لَلۡأٓخِرَةَ وَٱلۡأُولَىٰ

Ndipo ndithu moyo womaliza ndi moyo woyamba uli m’manja mwathu. info
التفاسير:

external-link copy
14 : 92

فَأَنذَرۡتُكُمۡ نَارٗا تَلَظَّىٰ

Basi, ndikukuchenjezani za Moto woyaka mwa mphamvu. info
التفاسير:

external-link copy
15 : 92

لَا يَصۡلَىٰهَآ إِلَّا ٱلۡأَشۡقَى

Sakaulowa koma (kafiri) woipitsitsa kwambiri. info
التفاسير:

external-link copy
16 : 92

ٱلَّذِي كَذَّبَ وَتَوَلَّىٰ

Yemwe amatsutsa (choona) ndi kunyoza (zisonyezo za Allah). info
التفاسير:

external-link copy
17 : 92

وَسَيُجَنَّبُهَا ٱلۡأَتۡقَى

Koma yemwe akuopa Allah kwambiri akatalikitsidwa ndi Moto. info
التفاسير:

external-link copy
18 : 92

ٱلَّذِي يُؤۡتِي مَالَهُۥ يَتَزَكَّىٰ

Amene akupereka chuma chake ndi cholinga chodziyeretsa. info
التفاسير:

external-link copy
19 : 92

وَمَا لِأَحَدٍ عِندَهُۥ مِن نِّعۡمَةٖ تُجۡزَىٰٓ

Ndipo palibe aliyense kwa iye, amene adamchitira za chifundo zomwe zikulipidwa.[450] info

[450] (Ndime 19-20)Tanthauzo la ma Ayah awiriwa nkuti munthu uyu sakupereka chuma chake chifukwa chobwezera chifundo cha anthu, kapena kuti adzamubwezerenso iye chifundo, koma akupereka chifukwa chofuna chikondi cha Mbuye wake basi.

التفاسير:

external-link copy
20 : 92

إِلَّا ٱبۡتِغَآءَ وَجۡهِ رَبِّهِ ٱلۡأَعۡلَىٰ

Koma (akuchita zimenezi) kufuna chikondi cha Mbuye wake Wapamwambamwamba. info
التفاسير:

external-link copy
21 : 92

وَلَسَوۡفَ يَرۡضَىٰ

Ndipo posachedwa adzasangalala.[451] info

[451] Tanthauzo lake apa ndikuti Allah adzamukondweretsa ndi malipiro Ake abwino kufikira munthuyo adzakondwera. Ma Ayah, kuyambira 17 mpaka 21, adatsika chifukwa cha Sayyidina Abu Bakr (r.a) yemwe adali kupereka chuma chake powagula akapolo omwe adali kuzunzidwa ndi mabwana awo chifukwa cholowa Chisilamu, pambuyo pake amawapatsa ufulu. Ndipo m’modzi wa iwowa ndi Sayyidina Bilal (r.a) amene adali Muazzini wa Mneneri Muhammad (s.a.w). Chomwechonso Ayah zimenezi zikumkhudza aliyense amene akugwiritsa ntchito chuma chake mnjira yopulumutsira chipembedzo.

التفاسير: