[260] Tanthauzo lake nkuti pamene onse awiri adanyamuka adali kuyenda m’mphepete mwanyanja kufikira chombo chidawadutsa. Eni chombowo adamdziwa Khidhiru nawakweza onse awiri popanda malipiro. Atakwera m’chombomo Khidhiru adatenga nkhwangwa ndi kuzula thabwa limodzi la m’chombomo pomwe chombocho chidali pakatikati pa nyanja.
Musa ataona anati: “Bwanji ukuboola chombo pomwe anthuwa atinyamula mwaulere?” Ndipo adatenga kasanza nkuika pomwe panachotsedwa thabwapo.