আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা

পৃষ্ঠা নং:close

external-link copy
54 : 18

وَلَقَدۡ صَرَّفۡنَا فِي هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانِ لِلنَّاسِ مِن كُلِّ مَثَلٖۚ وَكَانَ ٱلۡإِنسَٰنُ أَكۡثَرَ شَيۡءٖ جَدَلٗا

Ndipo ndithu tawafotokozera anthu mwatsatanetsatane m’Qur’aniyi fanizo la mtundu uliwonse; koma munthu wapambana chinthu chilichonse pa makani. info
التفاسير:

external-link copy
55 : 18

وَمَا مَنَعَ ٱلنَّاسَ أَن يُؤۡمِنُوٓاْ إِذۡ جَآءَهُمُ ٱلۡهُدَىٰ وَيَسۡتَغۡفِرُواْ رَبَّهُمۡ إِلَّآ أَن تَأۡتِيَهُمۡ سُنَّةُ ٱلۡأَوَّلِينَ أَوۡ يَأۡتِيَهُمُ ٱلۡعَذَابُ قُبُلٗا

Ndipo palibe chimene chaletsa anthu kukhulupirira (tsopano) pamene chiongoko choonadi chawadzera ndikupempha chikhululuko kwa Mbuye wawo, koma akuyembekezera kuti chiwadzere chikhalidwe cha anthu oyamba, kapena chiwadzere chilango masomphenya. info
التفاسير:

external-link copy
56 : 18

وَمَا نُرۡسِلُ ٱلۡمُرۡسَلِينَ إِلَّا مُبَشِّرِينَ وَمُنذِرِينَۚ وَيُجَٰدِلُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِٱلۡبَٰطِلِ لِيُدۡحِضُواْ بِهِ ٱلۡحَقَّۖ وَٱتَّخَذُوٓاْ ءَايَٰتِي وَمَآ أُنذِرُواْ هُزُوٗا

Ndiponso sitituma atumiki (ndi cholinga choti adzetse chilango), koma kuti akhale onena nkhani zabwino ndi ochenjeza. Ndipo amene sadakhulupirire, akuchita makani ndi chabodza kuti kupyolera m’chabodzacho achotse choonadi, ndipo Ayah Zanga ndi zomwe achenjezedwa nazo, akuzichitira chipongwe! info
التفاسير:

external-link copy
57 : 18

وَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّن ذُكِّرَ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِۦ فَأَعۡرَضَ عَنۡهَا وَنَسِيَ مَا قَدَّمَتۡ يَدَاهُۚ إِنَّا جَعَلۡنَا عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ أَكِنَّةً أَن يَفۡقَهُوهُ وَفِيٓ ءَاذَانِهِمۡ وَقۡرٗاۖ وَإِن تَدۡعُهُمۡ إِلَى ٱلۡهُدَىٰ فَلَن يَهۡتَدُوٓاْ إِذًا أَبَدٗا

Ndindani woipitsitsa kwabasi woposa yemwe akukumbutsidwa ndi Ayah za Mbuye wake, koma iye nkuzinyoza, ndipo nkuiwala (zoipa) zimene manja ake adatsogoza? Ndithu Ife taika m’mitima mwawo zitsekelero kuti asazizindikire. Ndiponso m’makutu mwawo mwalemedwa ndi ugonthi. Ndipo ukawaitanira kuchiongoko (choonadi), salola kuongoka ngakhale pang’ono. info
التفاسير:

external-link copy
58 : 18

وَرَبُّكَ ٱلۡغَفُورُ ذُو ٱلرَّحۡمَةِۖ لَوۡ يُؤَاخِذُهُم بِمَا كَسَبُواْ لَعَجَّلَ لَهُمُ ٱلۡعَذَابَۚ بَل لَّهُم مَّوۡعِدٞ لَّن يَجِدُواْ مِن دُونِهِۦ مَوۡئِلٗا

Ndipo Mbuye wako Ngokhululuka kwambiri mwini chifundo. Ndipo akadawathira m’dzanja pa zoipa zomwe akhala akuchita, ndiye kuti ndithu akadawapatsa chilango mwachangu; koma iwo ali nalo lonjezo ndipo sadzapeza pothawira paliponse ndikulipewa. info
التفاسير:

external-link copy
59 : 18

وَتِلۡكَ ٱلۡقُرَىٰٓ أَهۡلَكۡنَٰهُمۡ لَمَّا ظَلَمُواْ وَجَعَلۡنَا لِمَهۡلِكِهِم مَّوۡعِدٗا

Ndipo imeneyo ndi midzi tidawaononga (okhalamo) pamene adadzichitira zoipa; ndipo tidawaikira lonjezo la nthawi yoikidwa la kuonongeka kwawo. info
التفاسير:

external-link copy
60 : 18

وَإِذۡ قَالَ مُوسَىٰ لِفَتَىٰهُ لَآ أَبۡرَحُ حَتَّىٰٓ أَبۡلُغَ مَجۡمَعَ ٱلۡبَحۡرَيۡنِ أَوۡ أَمۡضِيَ حُقُبٗا

Ndipo (kumbukani) pamene Mûsa adanena kwa mnyamata wake (Yusha’ Ibn Nun): “Ndipitiriza kuyenda kufikira ndikafike pamajiga pa nyanja ziwiri, kapena ndizingoyenda zaka ndi zaka (kufikira nditakumana naye amene ndikumfunayo).” info
التفاسير:

external-link copy
61 : 18

فَلَمَّا بَلَغَا مَجۡمَعَ بَيۡنِهِمَا نَسِيَا حُوتَهُمَا فَٱتَّخَذَ سَبِيلَهُۥ فِي ٱلۡبَحۡرِ سَرَبٗا

Choncho pamene adafika pamajiga (pa nyanja ziwirizo) adaiwala nsomba yawo yomwe idatenga njira yake kunka m’nyanja ngati una (Mûsa adaiwala kumfunsa mnyamata wake za nsombayo; naye mnyamata adaiwala kumfotokozera Mûsa zomwe zidachitika ndi nsoinbayo). info
التفاسير: