আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা

পৃষ্ঠা নং:close

external-link copy
107 : 10

وَإِن يَمۡسَسۡكَ ٱللَّهُ بِضُرّٖ فَلَا كَاشِفَ لَهُۥٓ إِلَّا هُوَۖ وَإِن يُرِدۡكَ بِخَيۡرٖ فَلَا رَآدَّ لِفَضۡلِهِۦۚ يُصِيبُ بِهِۦ مَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦۚ وَهُوَ ٱلۡغَفُورُ ٱلرَّحِيمُ

Ndipo ngati Allah atakukhudza ndi masautso, palibe aliyense owachotsa kupatula Iye. Ngatinso atakufunira zabwino, palibe amene angaubweze ubwino Wake. (Iye) amadza ndi ubwinowo kwa amene wamfuna mwa akapolo Ake. Ndipo Iye Ngokhululuka Ngwachisoni zedi. info
التفاسير:

external-link copy
108 : 10

قُلۡ يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ قَدۡ جَآءَكُمُ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّكُمۡۖ فَمَنِ ٱهۡتَدَىٰ فَإِنَّمَا يَهۡتَدِي لِنَفۡسِهِۦۖ وَمَن ضَلَّ فَإِنَّمَا يَضِلُّ عَلَيۡهَاۖ وَمَآ أَنَا۠ عَلَيۡكُم بِوَكِيلٖ

Nena: “E inu anthu! Choonadi chakudzerani kuchokera kwa Mbuye wanu. Choncho amene waongoka, (zabwino zake) zili pa iye mwini. Ndipo amene wasokera, ndithu zotsatira za kusokera zili pa iye mwini. Ndipo ine sindili muyang’aniri pa inu, (udindo wanga ndi kuchenjeza basi).” info
التفاسير:

external-link copy
109 : 10

وَٱتَّبِعۡ مَا يُوحَىٰٓ إِلَيۡكَ وَٱصۡبِرۡ حَتَّىٰ يَحۡكُمَ ٱللَّهُۚ وَهُوَ خَيۡرُ ٱلۡحَٰكِمِينَ

Ndipo (andiuza kuti): “Tsatira zimene zikuvumbulutsidwa kwa iwe ndipo pirira kufikira Allah adzaweruze. Iye Ngoweruza bwino kuposa aweruzi onse.” info
التفاسير: