আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা

পৃষ্ঠা নং:close

external-link copy
71 : 10

۞ وَٱتۡلُ عَلَيۡهِمۡ نَبَأَ نُوحٍ إِذۡ قَالَ لِقَوۡمِهِۦ يَٰقَوۡمِ إِن كَانَ كَبُرَ عَلَيۡكُم مَّقَامِي وَتَذۡكِيرِي بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ فَعَلَى ٱللَّهِ تَوَكَّلۡتُ فَأَجۡمِعُوٓاْ أَمۡرَكُمۡ وَشُرَكَآءَكُمۡ ثُمَّ لَا يَكُنۡ أَمۡرُكُمۡ عَلَيۡكُمۡ غُمَّةٗ ثُمَّ ٱقۡضُوٓاْ إِلَيَّ وَلَا تُنظِرُونِ

Ndipo awerengere (molakatula) nkhani za Nuh pamene adanena kwa anthu ake: “E inu anthu anga! Ngati kukhala kwanga pamodzi ndi inu ndi kukumbutsa kwanga Ayah za Allah kukukukulirani, ine ndatsamira kwa Allah (sindisiya ntchito yangayi). Choncho sonkhanitsani zinthu zanu pamodzi ndi milungu yanuyo; (sonkhanani kuti mundichitire choipa, ine sindilabadira chilichonse). Ndipo chinthu chanucho chisabisike kwa inu, (chitani moonekera. Ine sinditekeseka ndi chilichonse). Kenako chitani pa ine (chimene mufuna kuchita) ndipo musandipatse danga. info
التفاسير:

external-link copy
72 : 10

فَإِن تَوَلَّيۡتُمۡ فَمَا سَأَلۡتُكُم مِّنۡ أَجۡرٍۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَى ٱللَّهِۖ وَأُمِرۡتُ أَنۡ أَكُونَ مِنَ ٱلۡمُسۡلِمِينَ

Ngati mutembenuka ndikunyoza, (ndikufuna kwanu). Ine sindinakupempheni malipiro. Malipiro anga kulibe kulikonse (kumene ndingalandire) koma kwa Allah, ndipo ndalamulidwa kuti ndikhale mmodzi mwa Asilamu (ogonjera Iye).” info
التفاسير:

external-link copy
73 : 10

فَكَذَّبُوهُ فَنَجَّيۡنَٰهُ وَمَن مَّعَهُۥ فِي ٱلۡفُلۡكِ وَجَعَلۡنَٰهُمۡ خَلَٰٓئِفَ وَأَغۡرَقۡنَا ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَاۖ فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُنذَرِينَ

Koma adamutsutsa. Choncho tidampulumutsa pamodzi ndi amene adali naye m’chombo. Ndipo tidawasankha iwo kukhala otsala (pa dziko anzawo ataonongeka). Ndipo tidawamiza amene adatsutsa Ayah Zathu. Choncho taona momwe mapeto a ochenjezedwa adalili! info
التفاسير:

external-link copy
74 : 10

ثُمَّ بَعَثۡنَا مِنۢ بَعۡدِهِۦ رُسُلًا إِلَىٰ قَوۡمِهِمۡ فَجَآءُوهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ فَمَا كَانُواْ لِيُؤۡمِنُواْ بِمَا كَذَّبُواْ بِهِۦ مِن قَبۡلُۚ كَذَٰلِكَ نَطۡبَعُ عَلَىٰ قُلُوبِ ٱلۡمُعۡتَدِينَ

Pambuyo pake tidawatumiza atumiki (ambiri) kwa anthu awo. Adawadzera ndi zisonyezo zoonekera poyera koma sadali okhulupirira zimene ena adazitsutsa kale, (adatsatira njira zomwezo za anzawo). Umo ndi momwe tikudindira zidindo m’mitima ya anthu opyola malire. info
التفاسير:

external-link copy
75 : 10

ثُمَّ بَعَثۡنَا مِنۢ بَعۡدِهِم مُّوسَىٰ وَهَٰرُونَ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَمَلَإِيْهِۦ بِـَٔايَٰتِنَا فَٱسۡتَكۡبَرُواْ وَكَانُواْ قَوۡمٗا مُّجۡرِمِينَ

Kenako pambuyo pawo tidamtuma Mûsa ndi Haarun pamodzi ndi zizindikiro zathu kwa Farawo ndi nduna zake, koma adadzikweza. Tero adali anthu ochita zoipa. info
التفاسير:

external-link copy
76 : 10

فَلَمَّا جَآءَهُمُ ٱلۡحَقُّ مِنۡ عِندِنَا قَالُوٓاْ إِنَّ هَٰذَا لَسِحۡرٞ مُّبِينٞ

Ndipo pamene choonadi chidawadzera kuchokera kwa Ife, adanena: “Ndithu awa ndimatsenga oonekera.” info
التفاسير:

external-link copy
77 : 10

قَالَ مُوسَىٰٓ أَتَقُولُونَ لِلۡحَقِّ لَمَّا جَآءَكُمۡۖ أَسِحۡرٌ هَٰذَا وَلَا يُفۡلِحُ ٱلسَّٰحِرُونَ

Mûsa adati: “Mukutero pa choonadi pamene chakudzerani? Kodi matsenga ali chonchi? Ndipo amatsenga sangapambane (ngakhale zitatani).” info
التفاسير:

external-link copy
78 : 10

قَالُوٓاْ أَجِئۡتَنَا لِتَلۡفِتَنَا عَمَّا وَجَدۡنَا عَلَيۡهِ ءَابَآءَنَا وَتَكُونَ لَكُمَا ٱلۡكِبۡرِيَآءُ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَمَا نَحۡنُ لَكُمَا بِمُؤۡمِنِينَ

(Iwo) adati: “Kodi watidzera kuti utichotse ku zimene tidawapeza nazo makolo athu kuti ukulu ukhale wa inu awiri m’dzikoli? Koma ife sitingakukhulupirireni awirinu.” info
التفاسير: