আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা

পৃষ্ঠা নং:close

external-link copy
79 : 10

وَقَالَ فِرۡعَوۡنُ ٱئۡتُونِي بِكُلِّ سَٰحِرٍ عَلِيمٖ

Ndipo Farawo adati: “Ndibweretsereni wamatsenga aliyense wodziwa kwambiri (zamatsenga).” info
التفاسير:

external-link copy
80 : 10

فَلَمَّا جَآءَ ٱلسَّحَرَةُ قَالَ لَهُم مُّوسَىٰٓ أَلۡقُواْ مَآ أَنتُم مُّلۡقُونَ

Ndipo pamene amatsenga adadza, Mûsa adati kwa iwo: “Ponyani zomwe mufuna kuponya (kuti musonyeze ukatswiri wanu kwa anthu).” info
التفاسير:

external-link copy
81 : 10

فَلَمَّآ أَلۡقَوۡاْ قَالَ مُوسَىٰ مَا جِئۡتُم بِهِ ٱلسِّحۡرُۖ إِنَّ ٱللَّهَ سَيُبۡطِلُهُۥٓ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يُصۡلِحُ عَمَلَ ٱلۡمُفۡسِدِينَ

Pamene adaponya, Mûsa adati: “Zomwe mwabweretsa ndi matsenga. Allah awaononga pompano. Ndithu Allah sakonza ntchito za oononga.” info
التفاسير:

external-link copy
82 : 10

وَيُحِقُّ ٱللَّهُ ٱلۡحَقَّ بِكَلِمَٰتِهِۦ وَلَوۡ كَرِهَ ٱلۡمُجۡرِمُونَ

“Ndipo Allah achilimbikitsa choonadi ndi mau Ake, ngakhale oipa anyansidwe nazo.” info
التفاسير:

external-link copy
83 : 10

فَمَآ ءَامَنَ لِمُوسَىٰٓ إِلَّا ذُرِّيَّةٞ مِّن قَوۡمِهِۦ عَلَىٰ خَوۡفٖ مِّن فِرۡعَوۡنَ وَمَلَإِيْهِمۡ أَن يَفۡتِنَهُمۡۚ وَإِنَّ فِرۡعَوۡنَ لَعَالٖ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَإِنَّهُۥ لَمِنَ ٱلۡمُسۡرِفِينَ

Sadamkhulupirire Mûsa kupatula achinyamata a mwa anthu ake, chifukwa choopa Farawo ndi nduna zake kuti angawazunze. Ndithu Farawo adali wodzikuza pa dziko, ndithudi, adali m’modzi mwa opyola malire. info
التفاسير:

external-link copy
84 : 10

وَقَالَ مُوسَىٰ يَٰقَوۡمِ إِن كُنتُمۡ ءَامَنتُم بِٱللَّهِ فَعَلَيۡهِ تَوَكَّلُوٓاْ إِن كُنتُم مُّسۡلِمِينَ

Ndipo Mûsa adati: “E inu anthu anga! Ngati inu mwakhulupirira Allah, choncho tsamirani kwa Iye ngati mulidi Asilamu (owona). info
التفاسير:

external-link copy
85 : 10

فَقَالُواْ عَلَى ٱللَّهِ تَوَكَّلۡنَا رَبَّنَا لَا تَجۡعَلۡنَا فِتۡنَةٗ لِّلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ

Choncho (iwo) adati: “Tayadzamira kwa Allah. E Mbuye wathu! Musatichite kukhala mayetsero kwa anthu oipa.” info
التفاسير:

external-link copy
86 : 10

وَنَجِّنَا بِرَحۡمَتِكَ مِنَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلۡكَٰفِرِينَ

“Ndipo tipulumutseni mwa chifundo Chanu ku anthu osakhulupirira.” info
التفاسير:

external-link copy
87 : 10

وَأَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰ مُوسَىٰ وَأَخِيهِ أَن تَبَوَّءَا لِقَوۡمِكُمَا بِمِصۡرَ بُيُوتٗا وَٱجۡعَلُواْ بُيُوتَكُمۡ قِبۡلَةٗ وَأَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَۗ وَبَشِّرِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ

Ndipo tidavumbulutsa kwa Mûsa ndi m’bale wake mawu Athu (oti): “Apangireni nyumba anthu anu mu Eguputo ndipo nyumba zanu zichiteni kukhala misikiti (pakuti simungathe kukhala ndi misikiti yoonekera), ndipo pempherani Swala. Ndipo auze nkhani yabwino okhulupirira (kuti Allah awapatsa zabwino pa moyo wa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro).” info
التفاسير:

external-link copy
88 : 10

وَقَالَ مُوسَىٰ رَبَّنَآ إِنَّكَ ءَاتَيۡتَ فِرۡعَوۡنَ وَمَلَأَهُۥ زِينَةٗ وَأَمۡوَٰلٗا فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا رَبَّنَا لِيُضِلُّواْ عَن سَبِيلِكَۖ رَبَّنَا ٱطۡمِسۡ عَلَىٰٓ أَمۡوَٰلِهِمۡ وَٱشۡدُدۡ عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ فَلَا يُؤۡمِنُواْ حَتَّىٰ يَرَوُاْ ٱلۡعَذَابَ ٱلۡأَلِيمَ

Ndipo Mûsa adati: “Mbuye wathu! Inu mwampatsa Farawo ndi nduna zake zodzikometsera, ndi chuma chambirimbiri pa moyo wa pa dziko. Mbuye wathu, (iwo akugwiritsa ntchito zimenezi) kuti asokeretse anthu pa njira Yanu. Mbuye wathu, wonongani chuma chawo ndipo iumitseni mitima yawo popeza sakhulupirira kufikira ataona chilango chowawa.” info
التفاسير: