Ngati afuna kukunyenga pa chimvanochi, ndithudi, Allah akukwanira kwa iwe (kukuteteza). Iye ndi Yemwe anakuthangata ndi chipulumutso chake ndi okhulupirira.
Ndipo (Allah) analuzanitsa pakati pa mitima yawo (poika chikondi pakati pawo). Ngati ukanapereka zonse za m’dziko lapansi (ncholinga choti uwaluzanitse mitima yawo mwa iwe wekha) sukadatha kuluzanitsa pakati pa mitima yawo. Koma Allah adaluzanitsa pakati pawo. Ndithu Iye Ngwamphamvu zoposa Ngwanzeru zakuya.
Sichoyenera kwa Mneneri kukhala ndi akayidi mpaka amenye nkhondo (kwambiri) ndi kugonjetseratu maiko molimba (ndi pamene atha kukhala ndi akayidi). Mukufuna zinthu za m’dziko pomwe Allah akufuna (mupeze mphoto ya) tsiku lachimaliziro! Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa Ngwanzeru zakuya.
Pakadapanda lamulo la Allah limene linatsogolera kale (lokulolezani chuma chopeza ku nkhondo), chilango chachikulu chikanakugwerani, chifukwa cha zimene munatenga (ku-nkhondo ya Badri).