Ndipo wakuba wamwamuna ndi wakuba wamkazi, aduleni manja awo; kukhala mphoto ya zomwe achita ndi chilango chochokera kwa Allah. Allah Ngwanyonga zoposa, Ngwanzeru zakuya.
Koma amene walapa pambuyo pakuchita kwake zoipa, namachita zabwino, Allah alandira kulapa kwake. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwabasi Ngwachisoni chosatha.[165]
[165] Taona chifundo cha Allah! Iye akulonjeza wochimwa kuti ngati asiya machimo ake amlandira. Tero munthu asadzione kuti waonongeka kotero kuti Allah sangamlandire. Iyayi! Abwelere ndi mtima wake wonse kwa Allah ndipo Allah amlandira.